Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi “Alefa ndi Omega ndi Ndani”?

Kodi “Alefa ndi Omega ndi Ndani”?

Yankho la m’Baibulo

 Mawu akuti “Alefa ndi Omega,” amanena za Yehova Mulungu Wamphamvuyonse. Ndipo mawuwa amapezeka pamavesi atatu m’Baibulo.​—Chivumbulutso 1:8; 21:6; 22:13. a

N’chifukwa chiyani Mulungu anadzipatsa mayina akuti “Alefa ndi Omega”?

 Alefa ndi chilembo choyambirira ndipo omega ndi chilembo chomaliza mu afabeti ya Chigiriki. Chigawo cha Baibulo chomwe chimadziwika ndi dzina lakuti Chipangano Chatsopano, chomwenso mumapezeka buku la Chivumbulutso, chinalembedwa m’Chigiriki. Popeza chilembo cha alefa ndi choyambirira ndipo chilembo cha omega ndi chomaliza, zikusonyeza kuti Yehova yekha ndiye woyamba ndi womaliza. (Chivumbulutso 21:6) Iye ndi Mulungu Wamphamvuyonse kuyambira kalekale ndipo adzakhalabe Mulungu Wamphamvuyonse mpaka kalekale. Iye yekha ndiye anakhalapo “kuyambira kalekale” ndipo adzakhalapo “mpaka kalekale.”​—Salimo 90:2.

Kodi “woyamba ndi wotsiriza,” ndi ndani?

 Baibulo likamanena kuti “woyamba ndi wotsiriza,” limanena za Yehova Mulungu kapena Yesu. Koma matanthauzo ake amakhala osiyana. Tiyeni tikambirane zitsanzo ziwiri izi:

  •   Pa Yesaya 44:6, Yehova ananena kuti “Ine ndine woyamba ndi womaliza ndipo palibenso Mulungu kupatulapo ine.” Palembali Yehova anasonyeza kuti iye yekha ndi Mulungu woona ndipo sipadzapezekanso wina mpaka kalekale. (Deuteronomo 4:35, 39) Choncho tingati mogwirizana ndi lembali mawu akuti “woyamba ndi womaliza,” tanthauzo lake ndi lofanana ndi mawu akuti “Alefa ndi Omega.”

  •   Kuwonjezera pamenepo, mawu akuti “Woyamba [kuchokera ku mawu akuti pro’tos, osati alefa] ndi Wotsiriza [kuchokera ku mawu akuti e’skha·tos, osati omega] amapezeka pa Chivumbulutso 1:17, 18 ndi pa 2:8.” Mavesiwa akusonyeza kuti munthu amene akutchulidwayo, poyamba anafa n’kukhalanso ndi moyo. Choncho mavesiwa sangakhale kuti akunena za Mulungu chifukwa iye sanafepo. (Habakuku 1:12) Koma timadziwa kuti nthawi ina, Yesu anafa n’kuukitsidwa. (Machitidwe 3:13-15) Iye anali woyamba kuukitsidwa ndi kupatsidwa moyo wauzimu kumwamba. Ndipo panopo ali kumwambako komwe adzakhale “kwamuyaya.” (Chivumbulutso 1:18; Akolose 1:18) Kuchokera nthawi imeneyo, Yesu anapatsidwa udindo wodzaukitsa anthu ena omwe anamwalira. (Yohane 6:40, 44) Choncho Yesu ndi womaliza kuukitsidwa mwachindunji ndi Yehova mwiniwakeyo. (Machitidwe 10:40) Mfundo imeneyi yatithandiza kudziwa chifukwa chake ndi pomveka kuti Yesu azitchulidwa kuti “Woyamba ndi Wotsiriza.”

Kodi lemba la Chivumbulutso 22:13, limasonyeza kuti Yesu ndi “Alefa ndi Omega”?

 Ayi. Munthu amene akulankhula mawu omwe ali pa Chivumbulutso 22:13, sakudziwika bwinobwino kuti ndi ndani. Ndipo chaputala chimenechi chili ndi anthu angapo omwe akulankhula. Polankhulapo za vesi limeneli, Professor William Barclay analemba kuti: “Nkhaniyi siinalembedwe mwa ndondomeko . . . choncho ndi zovuta kudziwa munthu amene akulankhula pavesili.” (The Revelation of John, Volume 2, Revised Edition, tsamba 223) Choncho dzina la “Alefa ndi Omega” lomwe likupezeka pa Chivumbulutso 22:13, liyenera kuti limanena za Yehova Mulungu monga mmene zilili m’mavesi ena a m’buku la Chivumbulutso.

a Ulendo wa nambala 4, mawuwa amapezeka m’Baibulo la King James Version pa Chivumbulutso 1:11. Komabe m’Mabaibulo ambiri, pavesili palibe mawu amenewa chifukwa sapezeka m’Baibulo loyambirira la Chigiriki. Patapita nthawi, m’pamene mawu amenewa anadzayamba kupezeka pavesili m’malemba opatulika.