Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Akhristu Ayenera Kusunga Sabata?

Kodi Akhristu Ayenera Kusunga Sabata?

Yankho la m’Baibulo

 Masiku ano Akhristu sayenera kusunga sabata chifukwa amayendera “chilamulo cha Khristu,” chomwe sichimawalamula kusunga Sabata. (Agalatiya 6:2; Akolose 2:16, 17) Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Choyamba tiyeni tione zimene zinachitika kuti anthu ayambe kusunga Sabata.

Kodi mawu akuti Sabata amatanthauza chiyani?

 Mawu akuti “sabata” anachokera ku mawu a Chiheberi omwe amatanthauza “kupuma kapena kusiya kugwira ntchito.” Mawuwa amapezeka koyamba m’Baibulo m’malamulo amene Mulungu anapatsa Aisiraeli. (Ekisodo 16:23) Mwachitsanzo, lamulo la nambala 4 m’Malamulo Khumi limati: “Muyenera kusunga tsiku la sabata ndi kuliona kukhala lopatulika, muzichita ntchito zanu zonse masiku 6. Koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wanu. Musagwire ntchito iliyonse.” (Ekisodo 20:8-10) Sabata linkayamba Lachisanu dzuwa likalowa ndipo linkatha Loweruka dzuwa likalowa. Pa tsikuli Aisiraeli sankayenera kuchoka pa nyumba zawo, kusonkha moto, kukatola nkhuni kapena kunyamula katundu. (Ekisodo 16:29; 35:3; Numeri 15:32-36; Yeremiya 17:21) Ndipo aliyense wogwira ntchito tsiku la Sabata ankaphedwa.—Ekisodo 31:15.

 Malinga ndi kalendala ya Ayuda masiku ena komanso chaka cha 7 ndi cha 50 zinkatchedwanso kuti sabata. Pa zaka zimenezi anthu sankaloledwa kulima minda yawo kapena kukakamiza amene anali ndi ngongole yawo kubweza.—Levitiko 16:29-31; 23:6, 7, 32; 25:4, 11-14; Deuteronomo 15:1-3.

Nsembe ya Yesu inapangitsa kuti lamulo losunga Sabata lisiye kugwira ntchito

N’chifukwa chiyani Akhristu sasunga Sabata?

 Anthu amene ankatsatira Chilamulo cha Mose ndi amene anali oyenera kusunga Sabata. (Deuteronomo 5:2, 3; Ezekieli 20:10-12) Mulungu sanalamule anthu ena kuti azisunga sabata. Kuwonjezera pamenepa ngakhale Ayuda ‘anamasulidwa ku Chilamulo’ cha Mose komanso ku Malamulo Khumi chifukwa cha nsembe ya Yesu Khristu. (Aroma 7:6, 7; 10:4; Agalatiya 3:24, 25; Aefeso 2:15) Choncho Akhristu satsatira Chilamulo cha Mose, m’malo mwake amatsatira lamulo loti azikondana.—Aroma 13:9, 10; Aheberi 8:13.

Zimene anthu ena amanena zokhudza Sabata

 Zimene anthu ena amanena: Mulungu ndi amene anayambitsa Sabata chifukwa anapuma pa tsiku la 7.

 Zimene Baibulo limanena: Baibulo limati: “Mulungu anadalitsa tsiku la 7. Analipatula kuti likhale lopatulika, chifukwa kuyambira pa tsikuli, iye wakhala akupuma pa ntchito yake yonse yolenga ndi yopanga zimene anafuna.” (Genesis 2:3) Lembali likungosonyeza zimene Mulungu anachita pa tsiku la 7 osati kuti ndi lamulo limene anapereka kwa anthu. Ndipo palibe pena paliponse m’Baibulo pamene pamasonyeza kuti nthawi ya Mose isanafike anthu ankasunga sabata.

 Zimene anthu ena amanena: Aisiraeli ankasunga Sabata ngakhale asanalandire Chilamulo cha Mose.

 Zimene Baibulo limanena: Mose anauza Aisiraeli kuti : “Yehova Mulungu wathu anachita nafe pangano ku Horebe.” Derali lili pafupi ndi Phiri la Sinai. Panganoli linaphatikizaponso lamuloli losunga Sabata. (Deuteronomo 5:2, 12) Zomwe Aisiraeli ankachita pa nthawi imene analamulidwa kuti azisunga Sabata, zikusonyeza kuti lamuloli linali latsopano. Zikanakhala kuti Aisiraeli ankasunga Sabata pa nthawi yomwe anali ku Iguputo, kodi zikanakhala zomveka kuti Sabatalo linkawakumbutsa kuti Mulungu anawapulumutsa ku Iguputo. (Deuteronomo 5:15) Kodi Aisiraeliwo anafunikiranso kuchita kuuzidwa kuti asamatole mana pa tsiku la 7? (Ekisodo 16:25-30) Nanga n’chifukwa chiyani anasonyeza kuti sankadziwa zoyenera kuchita ndi munthu woyamba amene sanasunge Sabata?—Numeri 15:32-36.

 Zimene anthu ena amanena: Lamulo losunga Sabata silidzatha ndipo anthu ayenera kumaligwiritsa ntchito mpaka kalekale.

 Zimene Baibulo limanena: Mabaibulo ena amamasulira kuti Sabata ndi “pangano losatha.” (Ekisodo 31:16, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Komabe mawu amene anawamasulira kuti “losatha” m’Chiheberi, angatanthauzenso “chomwe chingakhalepo kwa nthawi yaitali,” osati mpaka muyaya. Mwachitsanzo, Baibulo limagwiritsanso ntchito mawu omwewa likamafotokoza za ansembe a chiisiraeli. Komano zochititsa chidwi n’zakuti Mulungu anathetsa maudindo awo monga ansembe zaka 2,000 zapitazo.—Ekisodo 40:15; Aheberi 7:11, 12.

 Zimene anthu ena amanena: Akhristu ayenera kusunga Sabata chifukwa nayenso Yesu ankasunga.

 Zimene Baibulo limanena: Yesu ankasunga Sabata chifukwa anali Myuda ndipo mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose, Ayuda onse ankafunika kusunga Sabata. (Agalatiya 4:4) Koma Yesu atamwalira, Pangano la Chilamulo lomwe limaphatikizapo kusunga Sabata, silinkagwiranso ntchito.—Akolose 2:13, 14.

 Zimene anthu ena amanena: Mtumwi Paulo nayenso ankasunga Sabata chifukwa anali Mkhristu.

 Zimene Baibulo limanena: Paulo ankalowa m’masunagoge tsiku la Sabata koma cholinga chake sichinali kusunga Sabata ngati Ayuda. (Machitidwe 13:14; 17:1-3; 18:4) Iye ankakalalikira uthenga wabwino ndipo pa nthawiyo anthu ochokera kwina ankaloledwa kulalikira m’sunagoge. (Machitidwe 13:15, 32) Ndipotu Paulo ankalalikira “tsiku ndi tsiku” osati pa tsiku la Sabata lokha.—Machitidwe 17:17.

 Zimene anthu ena amanena: Lamlungu ndi tsiku la Sabata kwa Akhristu.

 Zimene Baibulo limanena: Palibe lamulo lililonse m’Baibulo losonyeza kuti Akhristu ayenera kuona kuti Lamlungu ndi tsiku lopuma ndi kulambira basi. Akhristu oyambirira ankagwiranso ntchito Lamlungu mofanana ndi masiku ena. Buku lina linanena kuti: “Kuyambira mu 300 C.E., anthu anayamba kuona kuti Lamlungu ndilo tsiku la Sabata. Izi zinayamba pamene Constantine amene anali mfumu ya Aroma yemwenso sankalambira Mulungu, analamula kuti anthu asamagwire ntchito zina pa tsiku la Mlungu.” aThe International Standard Bible Encyclopedia

 N’chifukwa chiyani mavesi ena m’Baibulo amasonyeza kuti Lamlungu linali tsiku lapadera? Baibulo limanena kuti mtumwi Paulo anadya chakudya ndi Akhristu anzake “pa tsiku loyamba la mlungu” lomwe linali Lamlungu. Zimenezi zinali zomveka chifukwa Pauloyo ankachoka tsiku lotsatira. (Machitidwe 20:7) Komanso mipingo ina inauzidwa kuti izisunga ndalama “tsiku lililonse loyamba la mlungu” lomwe linali Lamlungu kuti zidzakhale chopereka. Koma amenewa anangokhala malangizo owathandiza kuti azisungiratu ndalama zimene akufuna kupereka. Ndipotu munthu aliyese ankasunga ndalamazi kunyumba kwake ndipo sankazipereka pa malo olambirira.—1 Akorinto 16:1, 2.

 Zimene anthu ena amanena: Si zoyenera kusankha tsiku limodzi mlungu uliwonse kuti likhale lopuma kapena kulambira.

 Zimene Baibulo limanena: Baibulo limapatsa Mkhristu aliyense ufulu wosankha pa nkhani imeneyi.—Aroma 14:5.

a Onaninso New Catholic Encyclopedia, Second Edition, Volume 13, tsamba 608.