KUPHUNZIRA BAIBULO MOTHANDIZIDWA NDI MUNTHU WINA
Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale
Muziphunzira Baibulo mokambirana komanso mwaulere. Pa nthawi yomwe mukuphunzira, mudzapeza mayankho a mafunso ngati awa:
Kodi ndingatani kuti ndizikhala moyo wosangalala?
Kodi kuvutika komanso zinthu zoipa zidzathadi?
Kodi anzanga ndi achibale omwe anamwalira ndingadzakumane nawonso?
Kodi Mulungu amasamaladi za ine?
Kodi ndizipemphera bwanji kuti Mulungu azimva mapemphero anga?
Kuphunziraku Ndi Kwaulere
Simudzalipira ndalama pa nthawi yonse yomwe mudzakhale mukuphunzira. Buku lophunzirira la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale komanso Baibulo, zidzakhala zaulere.
Malo ndi Nthawi
Muzikumana ndi mphunzitsi wanu pamasom’pamaso kapena muziphunzira kudzera pafoni kapena pa intaneti, pa nthawi ndi malo omwe mungakonde.
Simukukakamizidwa
Phunziroli si lokakamiza. Mukhoza kumasuka kunena ngati simukufuna kupitiriza kuphunzira.
Kodi phunziro la Baibulo limachitika bwanji?
Mphunzitsi wanu adzakuthandizani kudziwa zomwe Baibulo limaphunzitsa, pokambirana phunziro lililonse palokha. Pogwiritsa ntchito buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, mudzaphunzira Baibulo pang’onopang’ono ndipo mudzamvetsa bwino uthenga wake komanso mmene ungakuthandizireni. Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene phunziroli limachitikira, onerani vidiyoyi kapena pezani mayankho a mafunso omwe anthu amafunsa kawirikawiri.
Kodi mukufuna kuona nkhani zomwe zili m’bukuli?
Onani maphunziro oyambirira a m’bukuli.
Kodi mukufuna muyeserere?
Dinani mawu ali m’munsiwa kuti muyambe kuphunzira Baibulo.