MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA
Ana ndi Mafoni—Mbali Yachiwiri: Phunzitsani Ana Anu Kugwiritsa Ntchito Foni Mosamala
Foni ndi chida champhamvu ndipo ikhoza kumuthandiza munthu kapena kumubweretsera mavuto, malinga ndi mmene waigwiritsira ntchito. Kodi mungaphunzitse bwanji ana anu kugwiritsa ntchito foni mosamala? Mwachitsanzo, kodi muyenera kuwalola kuti azikhala nthawi yochuluka bwanji pafoni tsiku lililonse? a
Zimene muyenera kudziwa
Pafoni pamapezekanso zinthu zoipa. Monga momwe tinafotokozera munkhani yakuti “Ana ndi Mafoni—Mbali Yoyamba: Phunzitsani Ana Anu Kugwiritsa Ntchito Foni Mosamala, foni imapatsa munthu mpata woona chilichonse chimene chili pa intaneti, kaya chabwino kapena choipa.
“N’zosavuta kuiwala kuti ana athu akakhala pafoni akhoza kuuzidwa zinthu zoipa kapenanso kukumana ndi anthu ochita zinthu zoopsa.”—Anatero Brenda.
Ana amafunika kuphunzitsidwa. Ana akhala akugwiritsa ntchito zipangizo zamakono chibadwireni, pamene achikulire ambiri angoyamba kumene. Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti makolo sakuzidziwa n’komwe zipangizo zamakonozo. Sizikutanthauzanso kuti ana ndi amene angadziwe bwino kagwiritsiridwe ntchito kabwino ka foni kapena kuchuluka kwa nthawi imene akuyenera kuthera pafoni.
N’zoona kuti mwina ana anu amadziwa bwino kugwiritsa ntchito foni, koma zimenezi sizikutanthauza kuti akudziwanso kuigwiritsa ntchito mosamala. Ngakhale ana amene amadziwa bwino kugwiritsa ntchito foni amafunika kuphunzitsidwa ndi makolo awo mmene angaigwiritsire ntchito mosamala.
“Kupatsa mwana wanu foni popanda kumuphunzitsa kagwiritsidwe ntchito kake kuli ngati kumupatsa makiyi a galimoto, kumuika pampando wadalaivala, kuliza injini, kenako n’kumuuza kuti, ‘tiye yamba kuyendetsa koma usamale’ musanamuphunzitse n’komwe kuyendetsa galimotoyo.”—Anatero a Seth.
Zimene mungachite
Dziwani mmene foni ya mwana wanu imagwirira ntchito. Pezani njira zimene zingathandize mwana wanu kugwiritsa ntchito foniyo mosamala. Mwachitsanzo:
Kodi foniyo ili ndi njira zotani zimene zingathandize makolo kuchepetsa nthawi imene mwana amathera pafonipo komanso kumuletsa kupita ku mawebusaiti oipa?
Kodi mukudziwa kuti njira zina zothandiza kuti mwana asaone zinthu zoipa pafoni sizimagwira ntchito bwinobwino?
Mukaidziwa bwino foni ya mwana wanu, m’pamenenso mungamuthandize bwino kuigwiritsira ntchito mosamala.
Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu wodziwa zinthu amachulukitsa mphamvu zake.”—Miyambo 24:5.
Khazikitsani malamulo. Ganizirani zinthu zimene muzilola ndi zimene simuzilola. Mwachitsanzo:
Kodi muzilola kuti mwana wanu azibweretsa foni patebulo mukamadya kapena muzimulola kukhala pafoni mukamacheza ndi achibale kapena anzanu?
Kodi ana anu azigona ndi foni kuchipinda?
Kodi muzilola kuti aike mapulogalamu ati pafonipo?
Kodi muzilola mwana wanu kukhala pafoni kwanthawi yaitali bwanji?
Kodi mukhazikitsa malire a nthawi imene akuyenera kukhala pafoni tsiku lililonse?
Muyenera kuuza mwana wanu malamulo amene mwakhazikitsa, ndipo muyenera kukhala okonzeka kumupatsa chilango akaphwanya malamulowo.
Mfundo ya m’Baibulo: “Usam’mane chilango mwana.”—Miyambo 23:13.
Muziona zimene zili pafonipo. Muyenera kudziwa nambala yachinsinsi yotsegulira foni ya mwana wanu ndipo muziona zimene zili pafonipo, monga mauthenga, mapulogalamu, zithunzi, ndi mawebusaiti amene anatsegula.
“Tinauza mwana wathu wamkazi kuti nthawi ndi nthawi tizitsegula foni yake kuti tione zimene zili pafonipo popanda kumuuziratu. Tikapeza kuti sakuigwiritsa ntchito mosamala, tizimuchepetsera nthawi ndi zinthu zimene angachite pafonipo.”—Anatero a Lorraine.
Monga kholo, muli ndi ufulu wonse wodziwa mmene mwana wanu akugwiritsira ntchito foni yake.
Mfundo ya m’Baibulo: “Mnyamata amadziwika ndi ntchito zake, ngati zochita zake zili zoyera ndiponso zowongoka.”—Miyambo 20:11.
M’phunzitseni mfundo zabwino. Thandizani mwana wanu kuti azifuna yekha kuchita zinthu zabwino. N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kuli kofunika? Chifukwa chakuti ngati mwana akufuna kubisira makolo ake zinazake, amapeza njira yochitira zimenezi ngakhale makolowo atayesetsa bwanji kuti adziwe zimene mwanayo akuchita. b
Choncho phunzitsani mwana wanu kukhala ndi makhalidwe abwino monga kuona mtima, kudziletsa, komanso kuzindikira kuti chilichonse chimene amachita chimakhala ndi zotsatirapo zabwino kapena zoipa. Mwana amene amayendera mfundo zabwino savutika kugwiritsa ntchito foni mosamala.
Mfundo ya m’Baibulo: ‘Anthu okhwima mwauzimu amaphunzitsa mphamvu zawo za kuzindikira kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’—Aheberi 5:14.
a Munkhani ino, tikunena za foni imene imatha kupita pa intaneti. Foni yotereyi imangokhala ngati kompyuta imene.
b Mwachitsanzo, ana ena amagwiritsa ntchito pulogalamu yooneka ngati yabwinobwino, mwatchitsanzo yooneka ngati kakyuleta, pofuna kubisa pulogalamu yoipa imene sakufuna kuti makolo awo aone.