ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
N’chifukwa Chiyani Sindikuyenera Kutsanzira Khalidwe la Anthu Omwe Amaonetsedwa M’mafilimu, pa TV ndi M’magazini?—Gawo 1: Ya Atsikana
Kodi ndi anthu otani amene tikukambirana m’nkhaniyi?
Taonani mawu otsatirawa ndipo kenako muyankhe mafunsowo.
Mbali Yoyamba |
Mbali Yachiwiri |
---|---|
Achibwana |
Oganiza bwino |
Osamvera |
Omvera malamulo |
Okonda chiwerewere |
Akhalidwe labwino |
Opanda nzeru |
Anzeru |
Okonda miseche |
Ozindikira |
Achinyengo |
Oona mtima |
Kodi ndi mawu amene ali m’mbali iti omwe mukuona kuti akufotokoza bwino khalidwe la atsikana amene amaonetsedwa m’mafilimu, m’ma TV, komanso amene amajambulidwa m’magazini?
Nanga ndi mawu amene ali m’mbali iti omwe akufotokoza bwino khalidwe limene inuyo mumafuna mutamadziwika nalo?
N’kutheka kuti mwayankha funso loyambalo kuti “mbali yoyamba,” ndipo pa funso lachiwiri mwayankha kuti “mbali yachiwiri.” Ngati mwayankha choncho, ndiye kuti simuli nokha, ndipo zikusonyeza kuti mumafunitsitsa mutakhala munthu wabwino wosiyana ndi anthu amene amasonyezedwa m’mafilimu, m’ma TV, ndi m’magazini. N’chifukwa chiyani tikutero?
“Mafilimu amasonyeza kuti atsikana achinyamata ndi osamvera ndiponso ovuta. Zimenezi zimachititsa kuti anthu aziganiza kuti mtsikana aliyense wachinyamata ndi wosadalirika ndiponso wovuta.”—Erin.
“Atsikana omwe amaonetsedwa m’mafilimu ndi m’ma TV, nthawi zonse amafuna kuti anthu aziganiza za iwowo. Choncho iwo amadzikongoletsa monyanyira, amavala mosiyana ndi ena, amayesetsa kuti atchuke kwambiri komanso amangoganizira za anyamata.”—Natalie.
“Kawirikawiri atsikana a m’mafilimu komanso m’ma TV omwe amaonetsedwa kuti ndi otsogola, amakonda kumwa, kugona ndi anyamata ndiponso amakhala osamvera makolo. Ngati mtsikana wa pa TV kapena mufilimu sakuchita zimenezi, ndiye kuti amakhala akumusonyeza kuti ndi wogona kapena wotsatira zachipembedzo monyanyira.”—Maria.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi mmene ndimavalira, mmene ndimachitira zinthu ndiponso mmene ndimalankhulira, zimasonyeza kuti ndimangotsanzira anthu otchuka amene amasonyezedwa m’mafilimu ndi m’ma TV?’
Zimene muyenera kudziwa
Anthu ambiri amene amaganiza kuti akuchita zinthu m’njira yawoyawo amakhala akungotsanzira anthu ena. Mtsikana wina wazaka 23 dzina lake Karen anati: “Mng’ono wanga amasonyeza khalidwe limeneli. Iye amangoganizira za zovala ndi anyamata basi, ndipo amanamizira kuti zinthu zina zonse alibe nazo ntchito. Mng’ono wangayu ndi wanzeru ndithu ndipo ndikudziwa kuti amakondanso zinthu zina. Koma iye amanamizira kuti sakonda zinthu zinazo n’cholinga choti azifanana ndi ‘atsikana onse.’ Iye akuchita zimenezi ngakhale kuti ali ndi zaka 12 zokha!”
Baibulo limati: “Musamatengere nzeru za nthawi ino.”—Aroma 12:2.
Zimene atsikana osonyezedwa m’mafilimu ndi m’ma TV amachita sikuti ndi zimene atsikana onse ayenera kuchita. Alexis, yemwe ndi mtsikana wazaka 15, anati: “Mafilimu ndi ma TV amasonyeza kuti atsikanafe nthawi zonse tikuyenera kumangochita zinthu zoti tizioneka bwino. Mafilimuwa amasonyezanso kuti tikuyenera kumachita zinthu mobalalika ndiponso mwachibwana. Koma ndikuona kuti atsikana ambirife tili ndi nzeru ndithu ndipo pali zinthu zambiri zaphindu zimene tingachite pamoyo wathu, kusiyana n’kumangoganizira za anyamata ooneka bwino.”
Baibulo limati: “Anthu okhwima mwauzimu . . . aphunzitsa mphamvu zawo za kuzindikira kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.”—Aheberi 5:14.
Atsikana otchuka a m’mafilimu ndi pa TV amangochita zimene otsatsa malonda akufuna. Pofuna kupeza phindu lochuluka, makampani akuluakulu akutsatsa kwambiri malonda awo kwa atsikana ang’onoang’ono, omwe sanafike n’komwe pa unyamata. Ena mwa makampaniwa ndi olemba magazini, osoka zovala zamafashoni, opanga zipangizo zamakono komanso ojambula mafilimu ndi mapulogalamu a pa TV. Poikira ndemanga pa nkhaniyi, buku lina linati: “Otsatsa malonda amatsatsa malonda awowo m’njira yoti ana aziganiza kuti munthu yemwe alibe zovala za m’fasho, majuwelo, zophodera, komanso zipangizo zamakono, ndi wotsalira. Ana amaona kapena kumva mauthenga otsatsa malondawa mobwerezabwereza, ndipo amakopeka mpaka amafika poona kuti nawonso akufunika kukhala ndi zinthuzo.”—12 Going on 29.
Baibulo limati: “Chilichonse cha m’dziko, monga chilakolako cha thupi, chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake, sizichokera kwa Atate, koma kudziko.”—1 Yohane 2:16.
Zoti muganizire: Kodi ndi ndani amene amapeza phindu inuyo mukamangokhalira kuganizira za mafashoni? Nanga ndi ndani amapeza phindu inuyo mukamayesetsa kukhala ndi foni iliyonse yamakono n’cholinga choti muzioneka kuti ndinu wotsogola pagulu la anzanu? Kodi otsatsa malondawo amaganizira kwambiri za inuyo kapena phindu limene iwowo angapeze?
Zimene mungachite
Musamangotsatira zilizonse zimene atsikana a m’mafilimu ndi pa TV akuchita. Mukamakula, mumayamba kuona bwino zinthu ndipo simukopeka ndi zilizonse. Muziganizira mwakuya mmene anthu ena angamakuonereni ngati mukungotsanzira zilizonse zimene anthu osonyezedwa m’mafilimu ndi m’ma TV amachita. Mtsikana wina wazaka 14 dzina lake Alana, anati: “Anthu a m’mafilimu ndi m’ma TV amasonyeza kuti mtsikana ayenera kumadziphoda monyanyira. Ndipotu atsikana ambiri sadziwa kuti saoneka bwino n’komwe akadziphoda kwambiri. Iwo amaonetseratu kuti akungofuna zoti anthu ena aziwaona.”
Mukhale ndi zolinga zokhudza khalidwe limene inuyo mukufuna kukhala nalo. Mwachitsanzo, ganizirani makhalidwe amene munasankha kuti mukufuna kukhala nawo, chakumayambiriro kwa nkhani ino. Bwanji osayamba panopa kuyesetsa kuti mukhale ndi makhalidwe amenewo, kapena ngati muli nawo kale, kuti muziwasonyeza kwambiri? Baibulo limati: “Muvale umunthu watsopano umene Mulungu amapereka, kutanthauza kuti mwa kudziwa zinthu molondola, muchititse umunthu wanu kukhala watsopano mogwirizana ndi chifaniziro cha Mulungu,” osati mogwirizana ndi zimene anthu otsatsa malonda amalimbikitsa.—Akolose 3:10.
Muzitsanzira anthu a makhalidwe abwino. Ena mwa anthu amenewa angakhale achibale anu, monga mayi kapena azakhali anu. Mungamatsanzirenso azimayi ena kapena anzanu omwe ndi oganiza bwino komanso a khalidwe labwino. A Mboni za Yehova sasowa anthu owatsanzira chifukwa mumpingo wawo muli azimayi ambiri achikhristu omwe ali ndi makhalidwe abwino.—Tito 2:3-5.
Mungachite izi: Gwiritsani ntchito buku la Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo kuti muphunzire zokhudza akazi okhulupirika omwe anali ndi makhalidwe abwino. Ena mwa akazi amenewa anali Rute, Hana, Abigayeli, Esitere, Mariya ndi Marita. A Mboni za Yehova ndi omwe amafalitsa buku la Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo, ndipo likupezeka pa www.isa4310.com.