Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JULY 19, 2019
SPAIN

Chinthu Chosaiwalika: A Mboni za Yehova Atulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso la Chisipanishi

Chinthu Chosaiwalika: A Mboni za Yehova Atulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso la Chisipanishi

Lachisanu pa 19 July, 2019, lomwe linali tsiku loyamba la Msonkhano Wamayiko wakuti “Chikondi Sichitha” ku Madrid m’dziko la Spain, a Mboni za Yehova anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso la Chisipanishi, lomwe anthu akhala akuliyembekezera kwa nthawi yaitali. Baibulo lokonzedwansoli tsopano likupezeka pa jw.org® kuti abale ndi alongo oposa 2.5 miliyoni oyankhula Chisipanishi padziko lonse, athe kuliwerenga komanso kupanga dawunilodi. Chisipanishi ndi chinenero chomwe chili ndi chiwerengero chachikulu kwambiri cha a Mboni za Yehova omwe amachigwiritsa ntchito. a

M’bale Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lolamulira, ndi amene anatulutsa Baibuloli m’nkhani yochita kujambulidwa imene inaonetsedwa pa sitediyamu ya Wanda Metropolitano Stadium mumzinda wa Madrid, pomwe pankachitikira msonkhanowu. Nthawi yomweyo, vidiyo ya nkhaniyi inaonetsedwanso ku malo ena a misonkhano 11 m’dziko la Spain omwe analumikizidwa. Patatha nthawi yochepa Baibuloli litatulutsidwa, vidiyo ya nkhaniyi inaikidwa pa JW Broadcasting®.

Abale ndi alongo akusangalala Baibulo la Chisipanishi lokonzedwanso litatulutsidwa

Pamalo amene msonkhano wamayikowu unkachitikira, panapangidwa dongosolo lapadera kuti anthu omwe anali pamsonkhanowu athe kupanga dawunilodi Baibuloli pa jw.org m’mafomati monga EPUB, JWPUB, kapena PDF. Abale ndi alongo amene ankaonera msonkhanowu m’malo osiyanasiyana 11 m’dziko la Spain, nawonso anapanga dawunilodi Baibuloli polumikiza zipangizo zawo zamakono ku JW Box, yomwe ndi Wi-Fi imene inapangidwa ndi a Mboni za Yehova. Kumalo a msonkhano wamayikowu komanso kumalo omwe ankachita kuonera msonkhanowu, kunali anthu oposa 1,200 amene anadzipereka kuthandiza anthu kuti apange dawunilodi Baibulo lokonzedwansoli.

Abale ndi alongo akupanga dawunilodi Baibulo la Dziko Latsopano la Chisipanishi lokonzedwanso pazipangizo zawo zamakono

Ntchito yomasulira Baibulo m’Chisipanishi inali yovuta kwambiri chifukwa choti pali a Mboni ambiri omwe amayankhula Chisipanishi amene amakhala m’mayiko ambiri osiyanasiyana. M’bale Pedro Gil yemwe ndi wa m’Komiti ya Nthambi ya ku Spain, anati: “Pa dziko lonse pali anthu pafupifupi 577 miliyoni amene amayankhula Chisipanishi, ndipo mawu amodzi komanso gulu la mawu, amakhala ndi matanthauzo osiyana potengera dziko. Kuonjezera pamenepo, chinenero cha Chisipanishi chasintha kwambiri m’zaka zaposachedwapa.”

Mlongo wachitsikana akuthandiza mlongo wachikulire kupanga dawunilodi Baibulo lomwe latulutsidwa

Pofuna kuthandiza omasulira kuti amasulire Baibuloli molondola komanso kuti likhale losavuta kuwerenga, abale ndi alongo 100 a m’mayiko osiyanasiyana anafunsidwa kuti anene maganizo awo ngati lamasuliridwa molondola komanso momveka bwino. Ntchito yonse yomasulira Baibuloli inatenga zaka 4 ndi hafu.

M’bale Gil anati: “Chisipanishi chamakono chomwe chagwiritsidwa ntchito mu Baibulo la Dziko Latsopano chili ndi mawu omwe aliyense akamva. Zimenezi zithandiza kuti ofalitsa asavutike kuligwiritsa ntchito muutumiki kapena pamisonkhano. Ndife osangalala kwambiri kuti kukonzanso Baibuloli kuthandizanso abale ndi alongo oyankhula Chisipanishi kuti ayandikire kwambiri Yehova.”

Tikuthokoza Yehova chifukwa cha Baibulo lokonzedwanso lomwe likulemekeza dzina lake. Tikukhulupirira kuti Baibuloli lithandiza a Mboni za Yehova kupitiriza kulalikira “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”—Machitidwe 1:8.

a Chifukwa choti pankafunika Mabaibulo osindikizidwa ochuluka kwambiri kuti aliyense alandire, m’malo onse omwe msonkhanowu unachitikira sikunagawidwe Mabaibulo osindikizidwa. Komabe, mipingo ya Chisipanishi pa dziko lonse ilandira Mabaibulo osindikizidwa akayamba kupezeka. Baibulo la Chisipanishi lokonzedwanso liyamba kupezeka pa JW Library® pambuyo pa Lolemba, pa 22 July.