Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 28, 2020
SOUTH KOREA

Mvula Yamphamvu Kwambiri Yawononga ku South Korea

Mvula Yamphamvu Kwambiri Yawononga ku South Korea

Malo

South Korea

Ngozi yake

  • Ku Korea kwagwa mvula kwa nthawi yaitali kuposa kale lonse

  • Mvulayi yachititsa kuti zinthu ziwonongeke chifukwa cha madzi osefukira komanso kugumuka kwa nthaka

Mmene yakhudzira abale ndi alongo

  • Ofalitsa 16 anathawa kaye m’nyumba zawo

Zinthu zimene zawonongeka

  • Nyumba 30 zawonongeka

  • Nyumba za Ufumu 19 zawonongeka

Zimene zachitika pothandiza anthu

  • Ofesi ya Nthambi ya ku Korea yakhazikitsa makomiti atatu (DRC) oti athandize anthu

  • Makomitiwa limodzi ndi oyang’anira madera akugwira ntchito ndi akulu kuti athandize abale ndi alongo m’madera amene akhudzidwa

  • Ntchito yoyeretsa ndiponso kukonza nyumba za abale ndi Nyumba za Ufumu ili mkati

Zimene zachitika

  • M’bale Min-seong Lee ndi mkazi wake amakhala mumzinda wa Gurye, womwe wakhudzidwa kwambiri ndi mvulayi ndipo anafunika kuchoka kwawo n’kusiya katundu yense. Madzi osefukira anadzaza m’nyumba yawo. Ntchito yothandiza anthu itayambika, abale amukomiti ina ya DRC anayeretsa nyumba ya m’bale ndi mlongo Lee n’kuwapatsa zinthu zofunika pamoyo. Abalewo anawalimbikitsanso kuti maganizo akhale m’malo komanso akhalebe olimba mwauzimu. Poyamikira zimene abalewo anachitira banja lawo, Mlongo Lee anati: “Ndikuthokoza kwambiri zimene anachita potithandiza. Anatichitira zazikulu. Ankagwira ntchito ngati akukonza zinthu za kunyumba kwawo. N’zoona kuti zinthu zambiri zinawonongeka koma zomwe tapeza n’zochuluka kuposa zimene tinali nazo.”

Tikuthokoza kwambiri kuti Yehova, yemwe ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse,” akupitiriza kusamalira abale ndi alongo athu ku Korea pa nthawi yovutayi.​—2 Akorinto 1:3, 4.