25 JANUARY, 2022
SOUTH AFRICA
Akuluakulu a ku South Africa Ayamikira a Mboni za Yehova Chifukwa Choyesetsa Kuthandiza Anthu Avuto Losamva
Mabuku a M’Baibulo Enanso Awiri Atulutsidwa M’Chilankhulo Chamanja cha ku South Africa
Anthu amene amagwira ntchito zothandiza anthu omwe ali ndi vuto losamva, ayamikira a Mboni za Yehova pothandiza anthu amene ali ndi vutoli potulutsa mavidiyo opangidwa bwino kwambiri a m’Chilankhulo Chamanja cha ku South Africa (SASL). Izi zachitika a Mboni za Yehova atangotulutsa mabuku a Agalatiya ndi Aefeso a Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Achigiriki Achikhristu mu Chilankhulo Chamanja cha ku South Africa pa 15 November, 2021. Pofika pano, ndiye kuti mabuku a m’Baibulo omwe atulutsidwa m’Chilankhulochi alipo 10. Mabuku ena 4 akuyembekezeka kutulutsidwa mu April 2022. Mabuku onsewa akupezeka pa webusaiti ya jw.org kapena pa apu ya JW Library Sign Language.
Minna Steyn yemwe ndi katswiri woona za maphunziro komanso mtsogoleri wa Boma la Western Cape, anafotokoza izi ponena za Mboni za Yehova: “Ndimasangalala kwambiri ndikawaona akumasulira m’chinenero chamanja moti ndikufuna kuwathokoza komanso kuyamikira kwambiri bungwe lanuli chifukwa cha mavidiyo okonzedwa bwino a chilankhulochi.”
Bongani Makama, ndi mtsogoleri wa Bungwe Loona za Anthu Olumala ku Eswatini. Iye ananena kuti: “Tikuthokoza a Mboni za Yehova chifukwa chothandiza anthu a vuto losamva kuti nawonso apeze zinthu zomwe anthu ena onse ali nazo.” Anawonjezeranso kuti: “[Anthu a vuto losamvawa] nawonso amafunikira kukhala ndi Baibulo la m’chilankhulo chawo. N’chifukwa chake tikuthokoza a Mboni za Yehova chifukwa chotulutsa mabuku a m’Baibulo amenewa kwa anthu a vutoli m’chilankhulo chapamtima pawo. Moti tikudikira mwachidwi kutulutsidwa kwa mabuku onse 66 a m’Baibulo la m’chilankhulo chamanja.”
Anthu pafupifupi 450,000 ku South Africa, amagwiritsa ntchito chilankhulo chamanja. Ku South Africa kuli ofalitsa 283 omwe ali ndi vuto losamva. Chifukwa cha khama lomwe Amboni akusonyeza, “anthu, kaya akhale a mtundu wotani” ali ndi mwayi wophunzira choonadi. Ndipo izi zikuphatikizaponso anthu a vuto losamva omwe ali m’gawo la nthambi ya South Africa.—1 Timoteyo 2:4.