1 FEBRUARY 2021
ERITREA
A Mboni za Yehova Enanso Atatu Atulutsidwa M’ndende ku Eritrea
Pa 1 February 2021, akuluakulu a boma ku Eritrea anatulutsa m’ndende m’bale mmodzi ndi alongo awiri. Iwo akhala m’ndende kuyambira zaka 4 mpaka 9 chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira. Tikupitiriza kupempherera abale ndi alongo 20 omwe adakali m’ndende omwe akupitirizabe kukhala okhulupirika kwa Yehova.—2 Akorinto 1:11.