Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Nyumba ya Ufumu ya ku Tortola asanaikonze komanso pambuyo poikonza. Imeneyi ndi imodzi mwa Nyumba za Ufumu 5 zomwe zinaonongeka ndi mphepo yamkuntho ya Maria ku British ndi U.S. Virgin Islands, ndipo inali yoyamba kukonzedwa.

JANUARY 19, 2018
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Mboni Akugwira Mwakhama Ntchito Yothandiza Anthu Omwe Anakhudzidwa Ndi Mphepo Zamkuntho

A Mboni Akugwira Mwakhama Ntchito Yothandiza Anthu Omwe Anakhudzidwa Ndi Mphepo Zamkuntho

NEW YORK—Ntchito yothandiza anthu okhudzidwa ndi mphepo yamkuntho ya Irma komanso ya Maria ili mkati. Mphepo ziwirizi zinaomba ndi kuononga kwambiri zinthu m’madera ozungulira nyanja ya Caribbean mu September 2017. Malipoti otsatirawa ochokera ku maofesi a nthambi ku Barbados, Cuba, Dominican Republic, France, ndi United States, akusonyeza mmene abale athu akhala akuthandizira anthu okhudzidwa.

Madera Ozungulira Nthambi ya Barbados—Anguilla, Antigua ndi Barbuda, Dominica, ndi St. Maarten (dera la a Datchi)

Makomiti othandiza pangozi zadzidzidzi atatu, kuphatikizapo komiti imene inapangidwa mogwirizana ndi nthambi ya France, anagwirira limodzi ntchito yokhazikitsa magulu a abale ndi alongo oti athandize ofalitsa okhudzidwa ndi ngoziyi powapatsa zinthu zofunikira mwamsanga. Zikuoneka kuti ntchito yokonza nyumba zomwe zinaonongeka m’madera a nthambi ya Barbados itenga ndalama zokwana pafupifupi madola 2.4 miliyoni a ku America. Ndipo ntchitoyi ikuphatikizapo kukonza Nyumba za Ufumu 8 komanso nyumba 122 za abale. Nyumba zinanso 19 n’zofunika kuzimanganso.

Nyumba ya Ufumu yomwe inawonongeka kwambiri ndi mphepo yamkuntho ya Maria ku Grand Bay, Dominica.

Dera la Nthambi ya Cuba

Nthambiyi yanena kuti ofalitsa amene anakhudzidwa ndi Mphepo Yamkuntho ya Irma akulandira thandizo lofunikira. Thandizoli likuphatikizapo maulendo a ubusa amene abale ochokera ku ofesi ya nthambi akuchita.

Dera la Nthambi ya Dominican Republic

Makomiti atatu anatsogolera ntchito yothandiza ofalitsa 57 omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi. Abale ndi alongo a m’derali anapereka zinthu monga chakudya, madzi, zovala ndi zinthu zina zofunika. Pofika kumapeto kwa mwezi wa October, abale ndi alongo ongodzipereka a m’derali anakonza ndi kuyeretsa nyumba zonse zomwe zinaonongeka.

Madera a Nthambi ya France—Guadeloupe ndi St. Martin

Ofesi ya nthambi ku France inakhazikitsa komiti pachilumba cha St. Martin komanso malo oyendetsera ntchito yothandiza anthu pangozi pa chilumba cha Guadeloupe, kuti atsogolere ntchito yomanga yomwe ingafunike ndalama pafupifupi madola 1.4 miliyoni a ku America. Ntchitoyi ikuphatikizapo kukonza Nyumba za Ufumu zokwana 12 ku Guadeloupe, Nyumba za Ufumu ziwiri ndi nyumba za abale 24 ku St. Martin. Anthu ogwira ntchito yomanga ongodzipereka okwana 22 ochokera ku France, Guadeloupe, ndi Martinique adzathandiza pa ntchito yothandiza anthu imeneyi.

Zinthu za wofalitsa wina zomwe zinaonongeka ndi mphepo yamkuntho ya Maria ku St. Martin.

Madera a Nthambi ya United States—British ndi U.S. Virgin Islands, Florida, Georgia, Puerto Rico, Turks ndi Caicos Islands

Ofalitsa opitirira 13,000 a m’dera la nthambiyi anakhudzidwa ndi ngoziyi. Pakalipano makomiti 4 akuthandiza abale ndi alongo athu okhudzidwawa ndipo amaliza kale mbali yoyamba ya ntchitoyi, yomwe inaphatikizapo kukonza nyumba ndi zinthu zina zambiri za abale zomwe zinaonongeka komanso kugawa zinthu zofunika monga chakudya ndi madzi. Mbali yoyamba ya ntchitoyi ili mkati ku Puerto Rico komanso ku British ndi U.S. Virgin Islands.

Anthu akugwira ntchito yoyeretsa imodzi mwa nyumba za ofalitsa oposa 3,200 omwe anakhudzidwa ndi mphepozi ku Puerto Rico.

Anthu ogwira ntchito yomanga ongodzipereka okwana 690, akathandiza pa ntchito yokonza Nyumba za Ufumu komanso nyumba za abale athu. Pa gululi, anthu 450 akathandiza kugwira ntchitoyi m’zilumba pomwe 240 akathandiza ku Florida ndi ku Georgia. Zikuoneka kuti ntchitoyi itenga ndalama zopitirira madola 30 miliyoni a ku America, ndipo zinthu zimene zikonzedwe m’maderawa ndi:

  • British ndi U.S. Virgin Islands – Nyumba za Ufumu 5 ndi nyumba za abale 190

  • Florida – Nyumba za Ufumu 40 ndi nyumba za abale 1,174

  • Puerto Rico – Nyumba za Ufumu 106, Nyumba za Misonkhano ziwiri ndi nyumba za abale 1,216

  • Turks ndi Caicos – Nyumba za Ufumu ziwiri ndi nyumba za abale 56

Pemphero lathu ndi lakuti Yehova alimbitse manja a onse amene akuthandiza nawo pa ntchitoyi. Tili ndi chikhulupiriro kuti ntchitoyi limodzinso ndi chilimbikitso chochokera m’Baibulo, zithandiza abale athuwa ndipo ziwalimbikitsa kupitiriza kutumikira Mulungu wathu wamkulu Yehova.—Nehemiya 2:18.

Lankhulani ndi:

Kuchokera ku Mayiko Ena: David A. Semonian, Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani, +1-845-524-3000

Ku Barbados: John Medford, +1-246-438-0655

Ku Dominican Republic: Josué Féliz, +1-809-595-4007

Ku France: Guy Canonici, +33-2-32-25-55-55