Anapulumutsidwa Akufuna Kudzipha
ANTHU awiri a Mboni za Yehova akulalikira kunyumba ndi nyumba, anafika panyumba ina. Atagogoda, bambo wina yemwe anali ndi nkhope yachisoni anatsegula chitseko, ndipo m’katimo mumaonekera chingwe chimene anachimangirira kumasitepe opita kuchipinda chosanja.
Bamboyo atauza anthu a Mboniwo kuti alowe, iwo anamufunsa za chingwecho. Bamboyo anawauza kuti anali atatsala pang’ono kudzimangirira pamene amamva kugogoda pachitseko chake ndipo anaganiza kuti atsegule chitsekocho komaliza asanadzikhweze. Anthu a Mboniwo anayesetsa kulimbikitsa bamboyo kuti asadziphe ndipo anam’perekeza kwa dokotala yemwe anamuthandiza.
Nkhani imeneyi inalembedwa m’nyuzipepala ina ya ku Belgium. Komabe, sikuti ndi nthawi yokhayi pamene a Mboni za Yehova anathandiza munthu kuti asadziphe. Taonani nkhani zina zotsatirazi zomwe zinachitika m’mayiko osiyanasiyana zofanana ndi nkhani imeneyi.
Mayi wina ku Greece analemba kuti: “Mwamuna yemwe ndinkakhala naye ankandichitira nkhanza zoopsa moti ndinayamba kudwala matenda a maganizo. Ndinkavutika maganizo kwambiri moti ndinaganiza zongodzipha basi. Maganizo oti ndidziphe akandibwerera, ndinkamvako bwino chifukwa ndinkaona kuti ndisiyana ndi mavuto anga.
”
Komabe mayiyu anayesetsa kupita kwa madokotala a matenda a zamaganizo kuti amuthandize. Patangopita nthawi yochepa, anakumana ndi a Mboni ndipo anayamba kuphunzira Baibulo kenako anayamba kufika kumisonkhano yawo. Mayiyo analemba kuti: “Abale ndi alongo amandikonda kwambiri. Ndipotu ndakhala ndikusowa chikondi chimenechi kwa zaka zonsezi.
Pano ndapeza anzanga enieni amene ndimawadalira. Panopa ndine wosangalala ndipo sindidera nkhawa za m’tsogolo.
”
Mayi wina wa Mboni ku England analemba kuti: “Munthu wina yemwe ndimadziwana naye anandiimbira foni usiku atakhumudwa kwambiri n’kundiuza kuti akufuna kudzipha usiku womwewo. Choncho ndinagwiritsa ntchito mfundo zimene ndinawerenga mu Galamukani! ya May 2008 n’kumulimbikitsa kuti asadziphe. Ndinakambirana nayenso malemba angapo pomulimbikitsa. Zimenezi zinathandiza chifukwa panopa, ngakhale kuti adakali ndi mavuto, safunanso kudzipha.
”
Ku Ghana, munthu wina wa Mboni za Yehova dzina lake Michael anayamba kucheza ndi mayi wina yemwe amagulitsa zinthu kuntchito kwake. Tsiku lina Michael anaona kuti mayiyo wakhumudwa kwambiri ndipo anamufunsa chifukwa chake wakhumudwa.
Mayiyo anati amaganizira zongodzipha chifukwa mwamuna wake anamusiya n’kukatenga mkazi wina. Michael anamulimbikitsa kuti asadziphe ndipo anam’patsa mabuku awiri amene amafotokoza Malemba. Zimenezi zinathandiza mayiyo kuti asamaganizenso zodzipha. Mayiyo anapitiriza kuphunzira Baibulo ndipo panopo ndi wa Mboni za Yehova.
Nyuzipepala ina ku United States inalemba nkhani yakuti mnyamata wina wa Mboni ankagwira ntchito yolalikira ndipo anaona galimoto itangoima koma ikulira.
Mnyamatayo anati: “Nditayang’anitsitsa, ndinaona kuti kotulukira utsi kwa galimotoyo kwalumikizidwa paipi. Mbali ina ya paipiyo inalowa mkati mwa galimotoyo kudzera pawindo ndipo panamatidwa zolimba kuti utsi usamatuluke m’galimotomo.
“Ndinathamanga n’kufika pamene panali galimotoyo ndipo nditasuzumira mkati, ndinaona mayi akulira pakatikati pa utsi wakuda kwambiri. Ndinakuwa kuti, ‘Kodi mayi inu, mwatani?’
“Nditagwira chitseko kuti nditsegule, ndinaona kuti m’galimotoyo munalinso ana atatu omwe anawaika pampando wakumbuyo. Nditatsegula, mayiyo anati: ‘Mundisiye ndife basi! Ndisiyeni! Ndife pamodzi ndi ana angawa.’
“Koma ine ndinati, ‘Chonde mayi, musachite zimenezi. Zimene mukufuna kuchitazi sizithandiza.’
“Mayiyo anayankha kuti: ‘Ndikufuna ndizipita kumwamba pamodzi ndi ana angawa.’
“Apa n’kuti mayiyo akulirabe ndipo ndinagwada. Nanenso ndinayamba kulira ndipo ndinachondereranso mayiyo kuti: ‘Chonde mayi, musachite zimenezi.’ Kenako ndinalowa m’galimotoyo n’kumutulutsa mwapang’onopang’ono, nditamukumbatira.
“Mwadzidzidzi ndinangomva mayiyo akukuwa kuti, ‘Nditulutsireni ana angawo asanafe!’
“Nthawi yomweyo ndinatulutsa ana onse. Panali ana awiri aakazi, wazaka 5 wazaka 4 komanso panali kamnyamata kazaka ziwiri. Anawo anali pampando wakumbuyo ndipo samadziwa chilichonse.
“Nditatulutsa anthu onse anayi, ndinazimitsa injini ya galimotoyo. Kenako anthu 5 tonse tinakhala pampanda wina ndipo ndinafunsa mayiyo kuti, ‘N’chifukwa chiyani munachita zimenezi?’”
A Mboni za Yehova amaona kuti moyo ndi mphatso ya mtengo wapatali yochokera kwa Mlengi wathu. Padziko lonse lapansi, iwo amayesetsa kutonthoza anthu amene achibale awo anadzipha komanso amayesetsa kuthandiza anthu amene akufuna kudzipha.