Ntchito Yomasulira Mabuku ku Mexico ndi ku Central America
Pali anthu 290 amene akumasulira mabuku m’mayiko 6 ku Mexico ndi ku Central America m’zinenero zoposa 60. N’chifukwa chiyani akumasulira mabuku m’zinenero zonsezi? N’chifukwa chakuti anthu akamawerenga mabuku othandiza pophunzira Baibulo m’zinenero zawo, zimene akuwerengazo zimawafika pamtima.—1 Akorinto 14:9.
Omasulira ena amene ankagwirira ntchitoyi ku ofesi ya Mboni za Yehova ya mumzinda wa Mexico City, anawasamutsira kumadera kumene kuli anthu olankhula zinenerozo. Anachita izi pofuna kuti azimasulira mogwirizanadi ndi mmene anthu a chinenerocho amalankhulira. Zimenezi zathandiza kwambiri chifukwa omasulira amalankhulana ndi anthu amene amawerenga zimene akumasulirazo. Choncho amadziwa bwino zimene anganene kuti anthuwo asavutike kumva.
Kodi omasulira mabuku akumva bwanji kugwira ntchito m’madera atsopanowa? Federico, yemwe amamasulira mabuku m’Chinawato cha ku Guerrero ananena kuti: “Kwa zaka zonse 10 zimene ndinkagwirira ntchitoyi mumzinda wa Mexico City, ndinapeza banja limodzi lokha lolankhula chinenero chimene ndikumasulira. Koma panopa, pafupifupi anthu onse a m’matawuni oyandikana ndi maofesi athu omasulirira mabuku amalankhula chinenerochi.”
Karin, amamasulira mabuku m’chinenero cha kumpoto kwa Germany. Iye amakhala pa ofesi yomwe ili ku Mexico m’chigawo cha Chihuahua. Iye ananena kuti: “Kukhala kuno limodzi ndi anthu amene amalankhula chinenero chimene ndikumasulira kwandithandiza kuti ndizidziwa mmene anthuwa amalankhulira. Malo amene tikukhala komanso kugwirira ntchito ali m’tauni yaing’ono ndipo ndimati ndikasuzumira pawindo, ndimatha kuona anthu amene apindule ndi ntchito yomasulira imene tikugwira.”
Neyfi, yemwe panopa akukhala ku ofesi yomasulirira mabuku yomwe ili ku Mérida m’dziko la Mexico, ananena kuti: “Tikamachititsa maphunziro a Baibulo m’Chimaya, timadziwa mawu amene anthu olankhula chinenerochi amawavuta kumva. Ndiye tikamamasulira, timaganizira njira zimene tingafotokozere mawu otere kuti anthu aziwamva mosavuta.”
Anthu amapindula kwambiri akamawerenga mabuku omwe amasuliridwa m’chinenero chawo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira a Elena omwe chinenero chawo chobadwira ndi Chitilapeniki. Kwa zaka 40, nthawi zonse ankapita ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Koma sankamvetsa zimene ankaphunzira chifukwa misonkhanoyi inkachitikira m’Chisipanishi. Iwo ananena kuti: “Ndinkangoti bola ndikupezeka pamisonkhano basi.” Koma ataphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito timabuku ta Chitilapeniki, anayamba kukonda kwambiri Mulungu moti anabatizidwa mu 2013 posonyeza kuti adzipereka kwa iye. Poyamikira, a Elena ananena kuti, “Ndikuthokoza Yehova pondithandiza kumvetsa Baibulo.”