N’chifukwa Chiyani Simukondwerera Khirisimasi?
Zimene anthu ambiri amanena
Bodza limene anthu amanena: A Mboni za Yehova sakondwerera Khirisimasi chifukwa chakuti sakhulupirira Yesu.
Zoona zake: Ife ndife Akhristu ndipo timakhulupirira kuti anthu adzapulumutsidwa kudzera mwa Yesu Khristu.—Machitidwe 4:12.
Bodza limene anthu amanena: Mumasokoneza mabanja chifukwa mumawaphunzitsa kuti asamakondwerere Khirisimasi.
Zoona zake: Timaona kuti banja ndi la mtengo wapatali kwambiri ndipo timagwiritsira ntchito malangizo a m’Baibulo pothandiza anthu kuti akhale ndi mabanja olimba.
Bodza limene anthu amanena: Mumamanidwa zinthu zimene anthu amachita pa Khirisimasi, monga kupatsana mphatso, kulimbikitsa mtendere padzikoli komanso kufunirana mafuno abwino.
Zoona zake: Timayesetsa kuchitira anthu zabwino komanso kukhala nawo mwamtendere tsiku lililonse. (Miyambo 11:25; Aroma 12:18) Mwachitsanzo, timasonyeza zimenezi pochita misonkhano yathu komanso kulalikira mogwirizana ndi zimene Yesu anatilangiza kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mateyu 10:8) Komanso timayembekezera kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzabweretse mtendere weniweni padzikoli.—Mateyu 10:7.
N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova sakondwerera Khirisimasi?
Yesu analamula kuti tizikumbukira imfa yake osati kubadwa kwake.—Luka 22:19, 20.
Atumwi a Yesu komanso ophunzira ake oyambirira sankakondwerera Khirisimasi. Buku lina limanena kuti “anthu anayamba kukondwerera Khirisimasi pambuyo pa chaka cha 243 [C.E.],” ndipo panali patadutsa zaka zoposa 100 kuchokera nthawi imene atumwi omalizira anamwalira.—The New Catholic Encyclopedia
Palibe umboni woti Yesu anabadwa pa December 25, ndipo palibe paliponse m’Baibulo pamene pamanena tsiku limene anabadwa.
Timakhulupirira kuti Mulungu savomereza zoti anthu azikondwerera Khirisimasi chifukwa inachokera ku miyambo yachikunja.—2 Akorinto 6:17.
N’chifukwa chiyani mumaona kuti kukondwerera Khirisimasi ndi nkhani yaikulu?
Anthu ambiri amakondwererabe Khirisimasi ngakhale kuti amadziwa kuti inachokera ku miyambo yachikunja ndipo ndi mwambo wosagwirizana ndi Baibulo. Anthu otero amadzifunsa kuti n’chifukwa chiyani a Mboni amaona kuti kukondwerera Khirisimasi ndi nkhani yaikulu?
Baibulo limatilimbikitsa kuti tisamangochita zinthu chifukwa chakuti ambiri akuchita koma tizigwiritsa ntchito “luntha la kuganiza.” (Aroma 12:1, 2) Limatilimbikitsanso kuti tizitsatira zinthu zoonadi. (Yohane 4:23, 24) Choncho ngakhale kuti timasamala ndi mmene anthu angaonere zochita zathu, timatsatira kwambiri mfundo za m’Baibulo ngakhale anthu ambiri atakhala kuti sakutsatira.
Ngakhale kuti ifeyo sitikondwerera Khirisimasi, sitikakamiza anthu ena kuti nawonso asamakondwerere. Timalemekeza ufulu wa munthu aliyense wosankha yekha zochita pa nkhani yokondwerera Khirisimasi.