Kodi Muli ndi Lamulo Loletsa Mavidiyo Ena, Mabuku Ena Ndiponso Nyimbo Zina?
Ayi. Gulu lathu silinaike lamulo loletsa mafilimu, mabuku kapena nyimbo, zimene anthu a m’chipembedzochi ayenera kupewa. N’chifukwa chiyani zili choncho?
Baibulo limalimbikitsa munthu aliyense kuti aphunzitse ‘mphamvu zake za kuzindikira’ kuti azisiyanitsa choyenera ndi chosayenera.—Aheberi 5:14.
Malemba amapereka mfundo zimene Mkhristu angaziganizire akafuna kusankha zosangalatsa. a Pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku, timayesetsa ‘nthawi zonse kutsimikiza kuti chovomerezeka kwa Ambuye n’chiti.’—Aefeso 5:10.
Baibulo limaphunzitsa kuti bambo yemwe ndi mutu wa banja ali ndi udindo woyang’anira banja lake. Choncho akhoza kusankha kuti anthu a m’banja mwake asamaonere mavidiyo ena, asamawerenge mabuku ena ndiponso asamamvetsere nyimbo zina. (1 Akorinto 11:3; Aefeso 6:1-4) Koma palibe munthu amene ali ndi udindo wosankhira anthu a mu mpingo zinthu zina zosangalatsa zimene sayenera kuonera kapena kumvera.—Agalatiya 6:5.
a Mwachitsanzo, Baibulo limaletsa chinthu chilichonse chimene chimalimbikitsa chiwawa, zamizimu kapena zachiwerewere.—Deuteronomo 18:10-13; Aefeso 5:3; Akolose 3:8.