Kodi a Mboni za Yehova Anasintha Zina N’zina M’Baibulo Kuti Zigwirizane ndi Zimene Amakhulupirira?
Ayi sitinasinthe. M’malomwake, tikazindikira kuti zina n’zina zimene timakhulupirira sizikugwirizana ndi Baibulo, timasintha zimene tinkakhulupirirazo.
Tisanayambe kufalitsa Baibulo lachingelezi la Baibulo la Dziko Latsopano mu 1950, tinkafufuza mosamala zimene Baibulo limanena. Tinkagwiritsira ntchito Mabaibulo osiyanasiyana pofuna kuonetsetsa kuti zimene timakhulupirira n’zogwirizana ndi Baibulo. Taonani zitsanzo zochepa za zinthu zimene takhala tikuzikhulupirira kwa nthawi yaitali ndipo muone ngati n’zogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.
Zimene timakhulupirira: Palibe milungu itatu mwa Mulungu mmodzi. Nsanja ya Olonda ya mu July 1882, yomwe pa nthawiyo inkatchedwa Zion’s Watch Tower, inanena kuti: “Anthu amene amawerenga magazini athu amadziwa bwino kuti timakhulupirira Yehova, Yesu komanso Mzimu woyera. Amadziwanso kuti sitikhulupirira zoti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi, chifukwa Baibulo siliphunzitsa zimenezi.”
Zimene Baibulo limanena: “Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi.” (Deuteronomo 6:4, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) “Koma kwa ife pali Mulungu m’modzi yekha, Atate, kwa amene zinthu zonse zidachokera ndi kwa amene ife tikhalira: ndipo pali Ambuye m’modzi, Yesu Khristu, amene zinthu zonse zinachokera ndi mwa Iye ife tili ndi moyo.” (1 Akorinto 8:6, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Ndipo Yesu ananena yekha kuti: “Atate ndi wamkulu kuposa Ine.”—Yohane 14:28, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.
Zimene timakhulupirira: Kulibe malo amene anthu oipa amawotchedwako kwamuyaya. Magazini ya Nsanja ya Olonda ya mu June 1882 inali ndi mutu wochokera pa mawu a pa Aroma 6:23 mu Baibulo lachingelezi la King James Version. Magaziniyi inali ndi mutu wakuti, “Mphotho Yake ya Uchimo ndi Imfa,” ndipo inati: “Zimenezitu n’zosavuta kumva. Koma zodabwitsa n’zakuti, anthu ambiri amene amaona kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu, amatsutsanabe ndi lemba losavuta kumvetsali. Iwo amakhulupirirabe kuti Baibulo limaphunzitsa zakuti mphotho yake ya uchimo ndi moyo wozunzika kwamuyaya ku Gehena.”
Zimene Baibulo limanena: “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” (Ezekieli 18:4, 20, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Chilango chomaliza chimene chidzaperekedwe kwa anthu amene amatsutsa Mulungu chidzakhala “chiwonongeko chosatha,” osati kuzunzidwa kwamuyaya ku Gehena.—2 Atesalonika 1:9, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Zimene timakhulupirira: Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni, osati uli mumtima mwa munthu. Pofotokoza nkhani yokhudza Ufumu wa Mulungu, magazini ya Nsanja ya Olonda ya mu December 1881 inanena kuti: “Ufumuwu ukadzakhazikitsidwa udzachotsa maufumu onse a padziko lapansi.”
Zimene Baibulo limanena: “Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Kodi a Mboni za Yehova amadalira Baibulo la Dziko Latsopano pofuna kusonyeza kuti zimene amakhulupirira n’zochokeradi m’Baibulo?
Ayi sichoncho, chifukwa tikupitirizabe kugwiritsira ntchito Mabaibulo osiyanasiyana pa ntchito yathu yolalikira. Ngakhale kuti timaphunzira ndi anthu kwa ulele ndipo timawapatsa Baibulo la Dziko Latsopano popanda kuwauza mtengo, timaphunziranso ndi amene amafuna kuti tizigwiritsira ntchito Mabaibulo ena.