Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuona Malo ku Beteli

Tikukuitanani kuti mudzaone maofesi athu a nthambi omwenso amadziwika kuti Beteli. Ku maofesi athu ena kulinso malo achionetsero omwe mukhoza kuona nokha popanda wokutsogolerani.

Kuyambiranso Kuona Malo: M'mayiko ambiri, anthu adzayambiranso kuona malo m'maofesi athu a nthambi kuyambira pa 1 June, 2023. Kuti mudziwe zambiri, lankhulani ndi abale a ku nthambi yomwe mukufuna kukaonayo. Komabe, musapite kukaona malo ngati mwapezeka ndi COVID-19 kapena ngati muli ndi zizindikiro za chimfine kapenanso ngati posachedwapa munakumana ndi munthu amene wapezeka ndi COVID-19.

Denmark

Stenhusvej 28

DK-4300 HOLBAEK

DENMARK

+45 59-45-60-00

Kuona Malo

Lolemba mpaka Lachisanu

9:00 a.m. mpaka 10:30 a.m. ndi 1:30 p.m. mpaka 3:00 p.m.

Nthawi yonse: Ola limodzi ndi hafu

Zimene Timachita

Ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Scandinavia imayang’anira ntchito ya anthu a Mboni za Yehova pafupifupi 50,000. Anthuwa ndi a m’maiko a Denmark, Faeroe Islands, Greenland, Iceland, Norway, ndi Sweden. Ofesiyi imayang’aniranso ntchito yomasulira mabuku ofotokosa nkhani za m’Baibulo m’zinenero 6 komanso m’zinenero zamanja zitatu. Imayang’aniranso nchito yopanga zinthu zomvetsera komanso zoonera monga mavidiyo m’zinenero zina pa zimene tatchulazi.

Koperani pepala losonyeza ofesi yathu.