Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

John Moore/Getty Images

NTCHITO YAPADERA YOLALIKIRA

Thandizo la Zaumoyo—Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?

Thandizo la Zaumoyo—Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?

 “Ngakhale kuti anthu padziko lonse sakudwala kwambiri matenda a COVID-19 ngati mmene zinalili poyamba, sizikutanthauza kuti mliriwu wasiya kupereka chiopsezo pa moyo wa anthu padziko lonse. . . . Sitikukayikira kuti m’tsogolomu mukhoza kubwera mliri wina ndipo tifunika kukhala okonzeka.”​—Dr. Tedros Adhanom Ghebreyesus, mkulu woyang’anira Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse, May 22, 2023.

 Mliri wa COVID-19 wachititsa kuti anthu ambiri azikumanabe ndi mavuto osiyanasiyana okhudza thanzi lawo komanso maganizo. Kodi maboma ndi mabungwe azaumoyo ndi okonzeka kuthana ndi mavuto amene tingakumane nawo ngati kutabwera mliri wina komanso kutithandiza pa mavuto okhudza thanzi lathu amene tikukumana nawo panopa?

 Baibulo limatiuza kuti pali boma limene lidzatipatse thandizo la zaumoyo lomwe tikufunikira. Limatiuza kuti “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu” kapena kuti boma. (Danieli 2:44) Boma limeneli likadzayamba kulamulira padziko lapansi, “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: “Ine ndikudwala.”” (Yesaya 33:24) Aliyense adzakhala ndi thanzi labwino ndiponso mphamvu ngati achinyamata.​—Yobu 33:25.