Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Samalani Kuti Musamapusitsike Ndi Nkhani Zabodza

Samalani Kuti Musamapusitsike Ndi Nkhani Zabodza

 Masiku ano, n’zosavuta kupeza nkhani zosiyanasiyana kuposa kale, kuphatikizapo zimene zingakuthandizeni kuti mukhale otetezeka komanso athanzi. Koma mukamafufuza nkhani, muyenera kusamala ndi zinthu izi:

  •   Nkhani zosocheretsa

  •   Malipoti abodza

  •    Mphekesera

 Mwachitsanzo, pa nthawi ya mliri wa COVID-19, mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations anachenjeza kuti nkhani zabodza zafalikira kwambiri. Iye anati: “Malangizo abodza okhudza mankhwala akufala kwambiri. Tikumamva nkhani zambiri zabodza pa TV komanso wailesi. Anthu akufalitsa nkhani zopanda umboni pa intaneti. Komanso anthu akulimbikitsa kwambiri tsankho chifukwa chosiyana chikhalidwe, mitundu ndi zinthu zina.”

 Nkhani zabodza zakhala zikufalikira kuyambira kalekale. Komabe, Baibulo linaneneratu kuti m’masiku otsiriza ano, “anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe. Iwo azidzasocheretsa ena ndiponso azidzasocheretsedwa.” (2 Timoteyo 3:1, 13) Panopa intaneti yachititsa kuti tizitha kulandira komanso kufalitsa mosadziwa nkhani zabodza mwamsanga ndiponso mosavuta kuposa kale. Chifukwa cha zimenezi, maimelo, mameseji komanso nkhani zina zimene timalandira zimaoneka ngati zolondola koma zili zabodza.

 Kodi mungatani kuti musamapusitsidwe ndi mphekesera komanso nkhani zosocheretsa? Tiyeni tione mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.

  •   Musamakhulupirire zinthu zonse zimene mwaona kapena kumva

     Zimene Baibulo limanena: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”​—Miyambo 14:15.

     Ngati sitingasamale, tikhoza kupusitsidwa mosavuta. Mwachitsanzo, taganizirani za timavidiyo kapena zithunzi zokhala ndi mawu ofotokozera zomwe anthu akumatumizirana pamalo ochezera a pa intaneti. Nthawi zambiri anthu amachita zimenezi pongofuna kuseketsa anthu. Komabe, zithunzi ndi mavidiyowa zingasinthidwe kapenanso sizingasonyeze nkhani yonse. Nthawi zina, anthu amapanga mavidiyo a anthu ena akuchita kapena kunena zinthu zimene sanazichite kapena kuzinena n’komwe.

     “Nthawi zambiri, nkhani zimene anthu ochita kafukufuku amapeza pa intaneti zimakhala zoti zinasinthidwa kapena kupotozedwa komanso zoti sizikufotokoza nkhani yonse.”​—Axios Media.

     Dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhaniyi ndi yoona kapena ndi yabodza?’

  •   Muzifufuza kumene nkhaniyo yachokera komanso zimene ikufotokoza

     Zimene Baibulo limanena: “Tsimikizirani zinthu zonse.”​—1 Atesalonika 5:21.

     Musanakhulupirire nkhani inayake kapena kuitumiza, ngakhale imene ndi yodziwika kapena imene yalengezedwa pa nyuzi, muzitsimikizira kaye kuti ndi yoona. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

     Muzifufuza kuti mudziwe ngati nkhaniyo yachokera kwa anthu odalirika. Makampani kapena mabungwe ofalitsa nkhani akhoza kusintha nkhanizo chifukwa cha maganizo awo andale kapena pofuna kutsatsa malonda. Mukamva nkhani inayake yochokera kwa ofalitsa nkhani, muziyerekezera ndi zimene ena alemba pa nkhani yomweyo. Nthawi zina, anzanu angakutumizireni mameseji abodza kapena kutumiza zinthu pamalo ochezera a pa intaneti mosadziwa. Choncho musamakhulupirire nkhani iliyonse musanatsimikizire kumene yachokera.

     Muzitsimikiziranso kuti nkhaniyo ndi yatsopano komanso yoona. Muziona madeti, mfundo zotsimikizirika komanso umboni wamphamvu wosonyeza kuti nkhaniyo ndi yoona. Muzisamala kwambiri ngati nkhani ikufotokoza zinthu zovuta m’njira yosavuta kwambiri kapena ngati yalembedwa mokufikani pamtima kwambiri.

     “Zikuoneka kuti kutsimikizira nkhani n’kofunika kwambiri masiku ano mofanana ndi kusamba m’manja.”​—Sridhar Dharmapuri, yemwe amagwira ntchito yoona za zakudya zopatsa thanzi ku Bungwe la United Nations.

     Dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhaniyi ikufotokoza maganizo a anthu ngati kuti ndi mfundo zoona kapena ikungofotokoza mbali imodzi?’

  •   Muzikhulupirira mfundo zimene n’zoona osati zongokusangalatsani

     Zimene Baibulo limanena: “Munthu wodalira mtima wake ndi wopusa.”​—Miyambo 28:26.

     Anthufe sitimakayikira nkhani zomwe zikugwirizana ndi zimene ifeyo tikufuna kukhulupirira. Nthawi zambiri, makampani a Intaneti amatumiza nkhani zogwirizana ndi zimene mumakonda komanso zimene mwakhala mukufufuza. Koma si nthawi zonse pamene nkhani zomwe timakonda kumva zimakhaladi zimene tikufunikira kumva.

     “N’zoona kuti anthufe timatha kuchita zinthu moganiza bwino. Koma nthawi zambiri zimene timakonda, kufuna komanso kuopa, zimachititsa kuti tiziona kuti nkhani inayake ndi yoona chifukwa choti ndi yogwirizana ndi zimene tikufuna kukhulupirira.”​—Peter Ditto, katswiri wa maphunziro amaganizo.

     Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikukhulupirira nkhaniyi chifukwa choti ikugwirizana ndi zimene ndimakonda?’

  •   Musamafalitse nkhani zabodza

     Zimene Baibulo limanena: “Usafalitse nkhani yabodza.”​—Ekisodo 23:1.

     Muzikumbukira kuti nkhani zimene mungatumize kwa anthu ena zikhoza kukhudza mmene amaganizira komanso mmene amachitira zinthu. Ngakhale mutatumiza nkhani zabodza mosadziwa kapena mwangozi, zotsatirapo zake zingakhale zoipa.

     “Chofunika kwambiri n’chakuti muziima kaye n’kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikudziwa kuti nkhaniyi ndi yoona moti ndikhoza kuitumiza kwa ena?’ Ngati aliyense atamachita zimenezi, nkhani zabodza zimene zimafalitsidwa pa intaneti zingachepe kwambiri.”​—Peter Adams, wachiwiri kwa woyang’anira bungwe la News Literacy Project.

     Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikutumiza nkhaniyi chifukwa choti ndikudziwa kuti ndi yoona?’