KHALANI MASO
Nkhondo ya ku Ukraine Ikuwonjezera Vuto la Kuchepa Kwa Chakudya Padziko Lonse
Pa 19 May 2022, nthambi ya Bungwe la United Nations yoona za chitetezo, inalandira lipoti kuchokera kwa akuluakulu a boma oposa 75, lonena kuti “vuto la kuchepa kwa chakudya padziko lonse lomwe lakula chifukwa cha mliri wa COVID-19 komanso kusintha kwa nyengo, likukula kwambiri chifukwa cha nkhondo ya ku Ukraine.” Pambuyo pake, nyuzipepala ina inanena kuti, “ngakhale kuti anthu akuvutika kale ndi mavuto ena padzikoli, koma nkhondo ya ku Ukraine ichititsa kuti m’madera ena anthu akhale pa vuto lalikulu lanjala.” (The Economist) Baibulo linaneneratu kale kuti masiku athu ano kudzakhala mavuto a kusowa kwa chakudya. Komabe limatchulanso zomwe tingachite polimbana ndi vutoli.
Baibulo linaneneratu za mavuto a kusowa kwa chakudya
Yesu analosera kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala.”—Mateyu 24:7.
Buku la m’Baibulo la Chivumbulutso limanena za anthu 4 okwera pamahatchi. Wokwera pahatchi wina akuimira nkhondo. Pambuyo pake, palinso wina amene akuimira njala, kutanthauza nthawi imene kudzakhala kovuta kupeza chakudya komanso pomwe chakudya chidzakhala chikugulitsidwa pa mtengo wokwera. Ulosi wa okwera pamahatchiwo umanena kuti: “Ndinapenya ndipo patsogolo panga panali hatchi yakuda! Wokwerapo wake anagwira masikelo awiri m’dzanja lake. Ndinamva chomveka ngati mawu . . . kuti; ‘muyeso umodzi wa tirigu wa malipiro a tsiku limodzi ndi miyeso itatu ya barele wa malipiro a tsiku limodzi.’”—Chivumbulutso 6:5, 6, Chipangano Chatsopano mu Chichewa Cha Lero.
Maulosi amenewa onena za kusowa kwa chakudya, akukwaniritsidwa masiku ano, nthawi imene Baibulo limaitchula kuti “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1) Kuti mudziwe zambiri zokhudza “masiku otsiriza,” komanso za anthu 4 okwera pamahatchi otchulidwa m’buku la Chivumbulutso, onerani vidiyo yakuti Zinthu Padzikoli Zinasintha Kuyambira mu 1914 komanso werengani nkhani yakuti, “Kodi Anthu 4 Okwera Pamahatchi Akuimira Chiyani?”
Mmene Baibulo lingatithandizire
Baibulo lili ndi malangizo abwino kwambiri omwe angatithandize kulimbana ndi mavuto osiyanasiyana, kuphatikizapo a kusowa kapena kukwera mtengo kwa chakudya. Malangizo ena mungawapeze munkhani yakuti, “Zimene Mungachite Ngati Mukupeza Ndalama Zochepa.”
Baibulo limatipatsanso chiyembekezo chakuti zinthu zidzakhala bwino. Limatilonjeza za nthawi imene “padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri” ndipo aliyense adzakhala ndi chakudya chokwanira. (Salimo 72:16) Kuti mudziwe zambiri zomwe Baibulo limalonjeza zokhudza mmene moyo udzakhalire m’tsogolo komanso chifukwa chake tingazikhulupirire, werengani nkhani yakuti, “Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo.”