Kodi Tingatani Kuti Tisamade Nkhawa Kwambiri?
Mukamada nkhawa kwambiri mukhoza kudwala komanso kuvutika maganizo. Mwina kungakubweretsereni mavuto aakulu kuposa amene anakudetsani nkhawa poyamba.
Zinthu zimene zingachepetse nkhawa
Musamawerenge kapena kumvetsera nkhani zambiri zoipa. Simuyenera kudziwa zonse zokhudza zinthu zoipa zimene zachitika. Kudziwa zambiri zokhudza zinthuzi kungakuchititseni kuda nkhawa kwambiri komanso kuchita mantha.
Mfundo ya m’Baibulo: “Mtima wosweka umaumitsa mafupa.”—Miyambo 17:22.
“Ambirife timakonda kumva nkhani zatsopano zomwe n’zodabwitsa koma zimenezi n’zosathandiza. Ndikamapewa kuwerenga kapena kumvetsera nkhani pafupipafupi, nkhawa zanga zimachepa.”—John.
Zoti muganizire: Kodi mumafunika kudziwa nkhani zatsopano nthawi zonse?
Muzikhala ndi ndandanda. Muziyesetsa kudzuka, kudya, kugwira ntchito zapakhomo komanso kugona pa nthawi yofanana tsiku lililonse. Kukhala ndi ndandanda kungakuthandizeni kuti musamade nkhawa kwambiri.
Mfundo ya m’Baibulo: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.”—Miyambo 21:5.
“Mliri wa COVID-19 utayamba ndinasiyiratu kutsatira ndandanda yanga n’kuyamba kugwiritsa ntchito nthawi yambiri pochita zosangalatsa. Koma ndinkafuna kugwiritsa ntchito bwino nthawi yanga choncho ndinapanga ndandanda yochitira zinthu tsiku ndi tsiku.”—Joseph.
Zoti muganizire: Kodi muli ndi ndandanda imene imakuthandizani kukwaniritsa zimene muyenera kuchita tsiku ndi tsiku?
Muziganizira zinthu zabwino. Kuganizira kwambiri zinthu zoipa zimene mwina zingadzachitike kumangokuchititsani kuda nkhawa. M’malomwake, muziganizira zinthu ziwiri kapena zitatu zimene mumayamikira.
Mfundo ya m’Baibulo: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.”—Akolose 3:15.
“Kuwerenga Baibulo kumandithandiza kuganizira zinthu zabwino n’kumapewa kumva nkhani zoipa. Mwina mungaone kuti sizingathandize kwenikweni koma zimathandizadi.”—Lisa.
Zoti muganizire: Kodi mumakonda kuganizira zinthu zoipa zimene zakuchitikirani n’kumaiwala zabwino zimene zachitika?
Muziganizira anthu ena. Nthawi zambiri, tikamada nkhawa kwambiri timafuna kungokhala patokha. Koma m’malo mochita zimenezi, muziyesetsa kuganizira zimene mungachite pothandiza anthu ena.
Mfundo ya m’Baibulo: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”—Afilipi 2:4.
“Ndimasangalala ndikamathandiza anthu ena. Zimene ndimawachitira zimawasangalatsa komanso zimandithandiza kuchepetsa nkhawa. Ndimatanganidwa kwambiri pochita zimenezi moti ndilibe nthawi yodera nkhawa.”—Maria.
Zoti muganizire: Pa anthu onse amene mumawadziwa, kodi ndi ndani amene angafunike kuthandizidwa kwambiri? Nanga kodi mungamuthandize bwanji?
Muziyesetsa kukhala wathanzi. Muzichita masewera olimbitsa thupi komanso kupuma mokwanira. Muzidya chakudya chopatsa thanzi. Kuchita zinthu zimenezi kungakuthandizeni kukhala ndi maganizo abwino komanso kumapewa nkhawa.
Mfundo ya m’Baibulo: “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.”—1 Timoteyo 4:8.
“Ine ndi mwana wanga sitingachite zambiri panja ngati mmene tikufunira. Choncho timayesetsa kuchita masewera olimbitsa thupi m’nyumba. Zimenezi zatithandiza kuti tizimva bwino komanso kugwirizana.”—Catherine.
Zoti muganizire: Kodi mumafunika kusintha zimene mumadya komanso mmene mumachitira masewera olimbitsa thupi kuti mukhale wathanzi?
Kuwonjezera pa kuchita zinthu zimene tatchulazi, anthu ambiri achepetsa nkhawa zawo pophunzira malonjezo a m’Baibulo okhudza zinthu zabwino zimene zidzachitike m’tsogolo. Onani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Chiyani?