Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULUNGU AMAGWIRIZANA NDI ZOTI ANTHU AZIMENYA NKHONDO?

Kodi Mulungu Ankagwirizana Ndi Zoti Anthu Azimenya Nkhondo M’nthawi ya Atumwi?

Kodi Mulungu Ankagwirizana Ndi Zoti Anthu Azimenya Nkhondo M’nthawi ya Atumwi?

Mofanana ndi Aisiraeli, Ayuda a m’nthawi ya atumwi ankaponderezedwa kwambiri ndi ulamuliro wa Roma. N’zosakayikitsa kuti nawonso ankapemphera mobwerezabwereza kuti Mulungu awathandize. Popeza kuti anali atamva za Yesu, yemwe ena ankakhulupirira kuti ndi Mesiya, n’kutheka kuti ‘ankayembekezera kuti munthu ameneyu ndi amene adzapulumutse Isiraeli’ ku ulamuliro woponderezawu. (Luka 24:21) Komabe zinthu sizinasinthe moti mu 70 C.E., asilikali a Roma anawononga mzinda wa Yerusalemu limodzi ndi kachisi wake.

Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu sanawathandize ngati mmene anachitira ndi Aisiraeli aja? Nanga n’chifukwa chiyani sanawalamule kuti amenye nkhondo n’cholinga choti adzipulumutse? Kodi Mulungu anali atasintha maganizo? Ayi. Tikutero chifukwa pa nthawiyi, Ayuda anali atasiya kumvera Mulungu ndipo anakana kuti Yesu ndi Mesiya. (Machitidwe 2:36) Choncho Yehova anali atasiya kuwaona kuti ndi anthu ake apadera.—Mateyu 23:37, 38.

Mulungu anali atasiya kuteteza Ayuda ndipo sankawathandiza akamamenya nkhondo. Yesu ananeneratu kuti chifukwa choti mtunduwu unali wosamvera, Mulungu adzasankha mtundu wina watsopano kuti uwalowe m’malo. Baibulo limatchula mtundu watsopanowu kuti “Isiraeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16; Mateyu 21:43) Akhristu amene anadzozedwa ndi mzimu woyera m’nthawi ya atumwi, analinso m’gulu limeneli. N’chifukwa chake anauzidwa kuti: “Tsopano ndinu mtundu wa anthu a Mulungu.”—1 Petulo 2:9, 10.

Popeza Akhristu odzozedwawa anali “anthu a Mulungu,” kodi Mulunguyo akanawamenyera nkhondo kuti Aroma asiye kuwapondereza? Kapena akanawalamula kuti amenyane nawo? Ayi, sanawalamule kuti achite zimenezi. Chifukwa chiyani? Monga taonera m’nkhani yapita ija, Mulungu ndi amene ankasankha nthawi yoyenera yoti anthu amenye nkhondo. Choncho tinganene kuti Mulungu anasankha kuti asamenye nkhondo m’nthawi ya atumwi.

Mofanana ndi Aisiraeli akale, Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankafunika kudikira mpaka nthawi itakwana yoti Mulungu awononge anthu oipa komanso opondereza ena. Pa nthawiyi Mulungu sanawalamule kuti amenye nkhondo. Ndipotu Yesu Khristu sankaphunzitsa otsatira ake kuti azimenya nkhondo, koma anawauza kuti: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.” (Mateyu 5:44) Komanso pa nthawi imene ankaneneratu za kuwonongedwa kwa mzinda wa Yerusalemu, Yesu sanauze ophunzira ake kuti adzamenye nkhondo, koma kuti adzathawire kumapiri. Ophunzira akewo anatsatiradi malangizowa.—Luka 21:20, 21.

Nayenso mtumwi Paulo analemba kuti: “Musabwezere choipa, . . . Pakuti Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine, watero Yehova.’” (Aroma 12:19) Zimene Paulo analembazi n’zofanana ndi zimene Mulungu anauza Aisiraeli kale kwambiri pa lemba la Levitiko 19:18 komanso pa Deuteronomo 32:35. Monga taonera m’nkhani yapita ija, Mulungu ankathandiza Aisiraeli akamalimbana ndi adani awo. Choncho, zimene Paulo ananenazi zikusonyeza kuti Mulungu sanasinthe maganizo pa nkhani ya nkhondo. Pa nthawiyi ankaonabe kuti nkhondo ndi njira yabwino yochotsera anthu oipa komanso yothandizira atumiki ake kuti asiye kuponderezedwa. Komabe mofanana ndi m’nthawi ya Aisiraeli, Mulungu ndi yemwe ankasankha woti amenye nkhondo komanso nthawi yoyenera kumenya nkhondoyo.

Apatu n’zoonekeratu kuti Mulungu sanalamule Akhristu a m’nthawi ya Atumwi kuti azimenya nkhondo. Nanga bwanji masiku ano? Kodi pali gulu linalake limene Mulungu walilamula kuti lizimenya nkhondo? Kapena akumathandiza atumiki ake powamenyera nkhondo? Nkhani yotsatirayi itithandiza kudziwa mayankho a mafunsowa.