MFUNDO ZAKALE KOMA ZOTHANDIZABE MASIKU ANO
Muzikhululuka Ndi Mtima Wonse
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Pitirizani . . . kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.”—Akolose 3:13.
Kodi mfundoyi imatanthauza chiyani? Baibulo limayerekezera tchimo ndi ngongole ndiponso kukhululuka ngati kuuza munthu kuti asabwezenso ngongoleyo. (Mateyu 18:21-27) Buku lina limanena kuti mawu achigiriki omwe anawamasulira kuti “kukhululuka” amatanthauza “kusakumbutsanso ngongole, n’kuiiwaliratu.” Choncho, ngati takhululukira munthu wina amene watilakwira, timakhala kuti taiwaliratu zimene munthuyo watichitira. Komatu kukhululukira munthu wina sikutanthauza kuti zimene munthuyo watichitira sizinatipweteke kapena kuti tikuchepetsa choipa chimene watichitira. Koma zimangotanthauza kuti sitikufuna kusunga zifukwa ngakhale titakhala ndi ‘chifukwa chomveka chodandaulira.’
Kodi mfundoyi ndi yothandiza masiku ano? Tonsefe si angwiro ndipo timalakwitsa nthawi zonse. (Aroma 3:23) Choncho n’zofunika kwambiri kuti tizikhululukira anzathu chifukwa ifenso nthawi ina tidzafuna kuti anzathu atikhululukire. Komanso pali phindu lina ngati timakhululukira anzathu.
Timadzipweteka tokha tikamasunga zifukwa komanso tikamalephera kukhululukira anzathu. Kuchita zimenezi kungachititse kuti tisamasangalale, tizikhala opanikizika komanso tizisowa mtendere wamumtima. Zingachititsenso kuti tidwale matenda oopsa. Lipoti lina lomwe linalembedwa pakoleji ina yoona za matenda a mtima linanena kuti: “Zikuoneka kuti anthu ambiri aukali komanso omwe amakonda kukwiya, amadwala matenda a mtima.”—Journal of the American College of Cardiology.
Koma tikamakhululuka, timakhala pa mtendere ndi ena ndipo zimatithandiza kuti tizigwirizana ndi anzathu. Komanso tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tikutsanzira Mulungu amene amakhululukira munthu amene walapa. Ndipotu Mulungu amafuna kuti ifenso tizikhululukira anzathu.—Maliko 11:25; Aefeso 4:32; 5:1.