Kodi Ndibwerekedi Ndalama?
Pa Chichewa pali mawu akuti, “Ngongole imakoma potenga, koma pobweza imawawa.”
MAWU amenewa ndi odziwika bwino ndipo amasonyeza maganizo amene anthu ambiri amakhala nawo pa nkhani ya ngongole. Kodi inunso mumaona kuti ngongole imakoma potenga? Ngakhale kuti nthawi zina zimaoneka kuti kubwereka ndalama n’kothandiza, kodi ndi bwinodi kuputa ngongole? Nanga kodi kubwereka ndalama kuli ndi mavuto otani?
Palinso mawu ena ofala amene amafotokoza kuipa kwa ngongole. Mawuwa amati: “Ngongole kudanitsa.” N’zoonadi kuti ngongole ikhoza kudanitsa anthu amene poyamba amagwirizana. Nthawi zina munthu akhoza kubwereka ndalama n’cholinga chabwino. Akhozanso kuganiziratu zimene achite kuti adzabweze ngongoleyo, koma zinthu n’kumusokonekera. Ndiye nthawi imene anagwirizana kuti abweza ikadutsa, mwiniwake wa ndalamayo angayambe kukhumudwa. Zoterezi zingathe kuyambitsa chidani pakati pa wobwereka ndi wobwereketsayo komanso pakati pa mabanja awo. Choncho popeza ngongole ingathe kuyambanitsa anthu, si bwino kuti tikakhala ndi mavuto a zachuma, tizingothamangira kuputa ngongole.
Kubwereka ndalama kukhozanso kuwononga ubwenzi wa munthu ndi Mulungu. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Baibulo limanena kuti munthu amene amabwereka ndalama n’kukana dala kubweza, ndi woipa. (Salimo 37:21) Limanenanso kuti, “wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsayo.” (Miyambo 22:7) Munthu amene wabwereka ndalama ayenera kudziwa kuti ali ndi mlandu kwa munthu amene wam’bwerekayo ndipo udzatha akadzabweza ngongoleyo. Zimenezi n’zogwirizana ndi mwambi wina wa ku Africa umene umati: “Ukabwereka miyendo ya munthu, umapita kulikonse kumene iyeyo akufuna.” Apa mfundo ndi yakuti munthu amene ali ndi ngongole zambiri sakhala ndi ufulu wochita zimene akufuna.
Choncho, munthu akabwereka ndalama ayenera kuyesetsa kuti abweze ndalamazo mwamsanga. Apo ayi, zikhoza kubweretsa mavuto. Kukhala ndi ngongole zambiri kungapangitse kuti munthu azikhala ndi nkhawa, azisowa tulo komanso azidzipanikiza kugwira ntchito n’cholinga choti apeze ndalama. Kuipa kwinanso kwa ngongole n’koti, munthu akhoza kumakangana ndi mwamuna kapena mkazi wake, banja likhoza kutha, akhoza kutengeredwa kukhoti ngakhalenso kumangidwa kumene. N’chifukwa chake lemba la Aroma 13:8 limati: “Anthu inu musamakhale ndi ngongole iliyonse kwa munthu aliyense, kusiyapo kukondana.”
KODI NDIKUFUNIKADI KUBWEREKA NDALAMA?
Poganizira mfundo zimenezi, tiziganiza mofatsa tisanapute ngongole. Ndi bwino kudzifunsa kuti: Kodi ndikufunikadi kubwereka ndalama? Kodi ndikufuna kubwereka ndalamazo n’cholinga choti ndisamalire banja langa ndipo zinthu zikhoza kuipa nditapanda kubwereka? Kapena ndikuchita zimenezi chifukwa chongolakalaka kukhala ndi zinthu zapamwamba komanso kusafuna kukhala moyo wotsika? Nthawi zambiri, ndi bwino kumakhutira ndi zomwe muli nazo m’malo moputa ngongole n’cholinga choti muzikhala moyo wapamwamba.
N’zoona kuti nthawi zina zinthu zimavuta moti sitingachitire mwina koma kubwereka ndalama basi. Mwachitsanzo, munthu wina wa m’banja lathu akhoza kudwala mwadzidzidzi, koma n’kupezeka kuti tilibiretu ngakhale 1 tambala. Ngati tasankha kubwereka ndalama pa nthawi zoterezi, tiyenerabe kuchita zinthu moona mtima komanso kubweza ngongoleyo. Kodi tingachite bwanji zimenezi?
Choyamba, si bwino kuganiza kuti palibe chifukwa chobwezera ndalamayo chifukwa munthu amene anatibwerekayo ndi wolemera. Tisamaganize kuti munthu akakhala wolemera ndiye kuti ali ndi udindo wotithandiza pa nkhani ya ndalama. Komanso tizidziwa kuti tikabwereka ndalama, ngakhale kwa munthu wotereyu, timakhalabe ndi udindo wochita zinthu moona mtima. Si bwino kuchitira nsanje anthu amene akuoneka kuti ali ndi ndalama, n’kuyamba kuganiza kuti tikhoza kuwadyera masuku pamutu.—Miyambo 28:22.
Chachiwiri, tizionetsetsa kuti tabweza ngongole yomwe tili nayo ndipo tizichita zimenezi mwamsanga. Ngati wotibwereka ndalamayo sananene nthawi yoti tidzabweze, ifeyo tiyenera kutchula nthawi yomwe tidzabweze ndipo tisunge pangano. Ndi bwinonso kulemba ndi kusainirana zokhudza ngongoleyo, pofuna kupewa kusamvana. (Yeremiya 32:9, 10) Ngati n’zotheka, ndi bwino kubweza ngongoleyo pamasom’pamaso kuti muthe kumuthokoza munthuyo. Kuyesetsa kubweza ngongole, komanso pa nthawi yake, kumathandiza kuti musadane. Pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anati: “Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.” (Mateyu 5:37) Komanso kumbukirani kuti: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”—Mateyu 7:12.
MALANGIZO OTHANDIZA A M’BAIBULO
M’Baibulo muli malangizo amene angatithandize kupewa chizolowezi chobwereka ndalama. Limati: “Ndithudi, kukhala wodzipereka kwa Mulungu kumeneko limodzi ndi kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo, ndi njiradi yopezera phindu lalikulu.” (1 Timoteyo 6:6) Mawu amenewa akutanthauza kuti ndi bwino kukhutira ndi zomwe tili nazo, chifukwa zimenezi zingapangitse kuti tipewe mavuto amene amabwera chifukwa chobwereka ndalama. N’zoona kuti si zophweka kukhutira ndi zomwe uli nazo chifukwa dzikoli limalimbikitsa moyo wofuna zinthu zapamwamba. Koma “kukhala wodzipereka kwa Mulungu” kungatithandize kuti tizikhutira ndi zomwe tili nazo.
Taganizirani chitsanzo cha banja lina la ku Asia. Atangokwatirana kumene ankasirira mabanja omwe anali ndi nyumba zawozawo zabwino. Choncho anagula nyumba ndi ndalama zomwe anasunga komanso zomwe anabwereka kubanki ndi kwa achibale awo. Koma pasanapite nthawi, anaona kuti akuvutika kwambiri kubweza ngongole mwezi uliwonse. Pofuna kuti azipeza ndalama zobweza ngongoleyo, anayamba kugwira ntchito ina kwa maola ambiri, ndipo izi zinkapangitsa kuti azikhala ndi nthawi yochepa yocheza ndi ana awo. Mwamuna wa banjali anati: “Ndinkakhala ndi nkhawa, ndinkasowa tulo komanso ndinkakhala wotopa kwambiri. Ndinkangomva ngati ndasenza chimwala chachikulu.”
“Ukamakhutira ndi zomwe uli nazo, umakhala wosangalala komanso umapewa mavuto ambiri”
Patapita nthawi, banjali linakumbukira mawu a pa 1 Timoteyo 6:6 ndipo linaona kuti njira yabwino inali kugulitsa nyumbayo basi. Panadutsa zaka ziwiri akulipirabe ngongole ija. Kodi anaphunzirapo chiyani pa zomwe zinawachitikirazi? Iwo anati: “Ukamakhutira ndi zomwe uli nazo, umakhala wosangalala komanso umapewa mavuto ambiri.”
Anthu ambiri amaona kuti mawu oti, “ngongole imakoma potenga, koma pobweza imawawa” aja ndi oona. Komabe zimenezi sizilepheretsa anthu kuputa ngongole. Ndiyetu, poganizira malangizo a m’Baibulo omwe takambirana m’nkhaniyi, tisanabwereke ndalama ndi bwino kudzifunsa kuti: Kodi ndibwerekedi ndalama?