Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

Anakhalabe Wokhulupirika Ngakhale Kuti Ena Ankachita Zinthu Zopanda Chilungamo

Anakhalabe Wokhulupirika Ngakhale Kuti Ena Ankachita Zinthu Zopanda Chilungamo

ELIYA anali pa ulendo wochokera kuphiri la Horebi, ndipo pamene amafika m’chigwa cha Yorodano, kwawo ku Isiraeli, n’kuti atayenda kwa milungu ingapo. Atafika ku Isiraeliku anaona kuti zinthu zasintha. Mavuto amene anabwera chifukwa cha chilala, chomwe chinatenga nthawi yaitali kwambiri, anali atayamba kutha. Mvula ya chizimalupsa inali itayamba kugwa ndipo alimi ankalima m’minda yawo. Mneneriyu ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri kuona kuti zinthu zayamba kuyenda bwino. Komabe mtima wake unali pa anthu a mtundu wakewa, chifukwa ambiri mwa anthuwa sanali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ambiri anali akulambirabe Baala, choncho Eliya anali ndi ntchito yaikulu yoti agwire. *

Eliya atafika pafupi ndi malo ena otchedwa Abele-mehola, anapeza anthu akulima ndi ng’ombe za pulawo. Panali ng’ombe 24 zimene zinkalima ziwiriziwiri. Munthu amene pulawo yake inali kumbuyo ndi amene Eliya ankafuna kuonana naye. Munthuyu anali Elisa ndipo Yehova anali atamusankha kuti ndiye adzalowe m’malo mwa mneneri Eliya. Poyamba Eliya ankaganiza kuti mtumiki wokhulupirika wa Mulungu amene watsala, ndi iyeyo basi. Choncho ayenera kuti ankafunitsitsadi kuonana ndi Elisa.—1 Mafumu 18:22; 19:14-19.

Kodi n’kutheka kuti Eliya sanagwirizane kwenikweni ndi mfundo yoti pakhale wina woti azigwira naye ntchito yake, kapena zoti wina adzamulowe m’malo? Sitikudziwa, ndiponso sitikudziwa ngati iye anaganizapo n’komwe zimenezi. Koma chomwe tikudziwa n’choti iye anali “munthu monga ife tomwe.” (Yakobo 5:17) Kaya Eliya anali ndi maganizo amenewa kapena ayi, Baibulo limati: “Eliya anapita pamene panali Elisa n’kumuponyera chovala chake chauneneri.” (1 Mafumu 19:19) Chovala chauneneri chimene Eliya ankavala, chomwe chinali chachikopa cha nkhosa kapena mbuzi, chinali chizindikiro choti iye anachita kusankhidwa ndi Yehova kuti akhale mneneri. Choncho zimene anachita, pomuponyera Elisa chovalachi, zinali ndi tanthauzo lalikulu. Zinasonyeza kuti mofunitsitsa anatsatira lamulo la Yehova loti aike Elisa kukhala wodzamulowa m’malo. Eliya ankakhulupirira Mulungu wake ndipo ankamumvera.

Eliya anasonyeza kudzichepetsa povomera kuti Elisa adzalowe m’malo mwake

Nayenso Elisa, yemwe pa nthawiyi anali wachinyamata, anali wofunitsitsa kuthandiza Eliya pa ntchito ya uneneri. Koma sikuti Elisa analowa m’malo mwa Eliya nthawi yomweyo. Kwa zaka 6, Elisa ankayenda ndi mneneri wachikulireyu n’kumamuthandiza, ndipo kenako ankadziwika kuti ndi “amene anali kuthirira Eliya madzi osamba m’manja.” (2 Mafumu 3:11) Eliya ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri kukhala ndi mtumiki womuthandiza wodalirika ameneyu. Amuna awiriwa ayenera kuti anakhala mabwenzi apamtima. Ankalimbikitsana ndipo izi ziyenera kuti zinawathandiza kukhalabe okhulupirika ngakhale kuti m’dzikomo munkachitika zinthu zambiri zopanda chilungamo. Munthu wina amene ankachita zinthu zoipa kwambiri anali Ahabu, yemwe anali mfumu ya Isiraeli.

Kodi inuyo munayamba mwachitiridwapo zinthu zopanda chilungamo? Ambirife zinatichitikirapo, chifukwa zimenezi n’zofala m’dziko loipali. Koma kukhala ndi bwenzi limene limakonda kwambiri Mulungu, kungakuthandizeni kukhalabe wokhulupirira zoterezi zikamachitika. Mungaphunzirenso zambiri pa chikhulupiriro cha Eliya.

 “NYAMUKA, PITA . . . UKAKUMANE NDI AHABU”

Eliya ndi Elisa anagwira ntchito mwakhama kuthandiza anthu kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Iwo ayeneranso kuti ankatsogolera pa ntchito yophunzitsa aneneri ena, ndipo n’kutheka kuti panali sukulu zomwe ankaphunzitsirako aneneri oterewa. Komabe patapita nthawi, Yehova anapatsa Eliya ntchito ina yoti agwire. Anamuuza kuti: “Nyamuka, pita ku Samariya ukakumane ndi Ahabu.” (1 Mafumu 21:18) Kodi Ahabu anali atachita chiyani?

Mfumu Ahabu inali itayamba mpatuko ndipo pa nthawiyo, panalibe mfumu ina ya Isiraeli yomwe inachita zoipa ngati Ahabu. Iye anakwatira Yezebeli, yemwe sankalambira Yehova, ndiponso anachititsa kuti Aisiraeli ambiri azilambira Baala. Ahabu nayenso ankachita nawo zimenezi. (1 Mafumu 16:31-33) Polambira Baala, anthu ankachita miyambo yokhudza kubereka, uhule komanso kupereka nsembe ana. Komanso Ahabu sanamvere lamulo la Yehova loti aphe Beni-hadadi, mfumu yoipa ya Siriya. N’zodziwikiratu kuti Ahabu anachita zimenezi n’cholinga choti apeze ndalama. (1 Mafumu chaputala 20) Pa nthawiyi, dyera, kukonda chuma komanso khalidwe lachiwawa la Ahabu ndi Yezebeli, zinali zitafika poipa kwambiri.

Ahabu anali ndi nyumba yachifumu yaikulu kwambiri ku Samariya. Koma analinso ndi nyumba ina yachifumu ku Yezereeli, mtunda wa makilomita 37 kuchokera ku Samariya. Pafupi ndi nyumba ya ku Yezereeliyi panali munda wa mpesa, womwe unali wa munthu wina dzina lake Naboti. Ahabu ankasirira kwambiri munda umenewu ndipo ankalakalaka utakhala wake. Tsiku lina, Ahabu anaitana Naboti n’kumuuza kuti amugulitse mundawu kapena asinthane ndi munda wina. Koma Naboti anayankha kuti: “Sindingachite zimenezo pamaso pa Yehova, kupereka cholowa cha makolo anga kwa inuyo.” (1 Mafumu 21:3) Kodi Naboti anachita zimenezi chifukwa choti anali wovuta basi? Ambiri amaganiza zimenezi. Komatu Naboti anachita izi chifukwa choti ankamvera lamulo la Yehova, lomwe linkaletsa Aisiraeli kugulitsa mpaka kalekale malo omwe anali cholowa cha banja lawo. (Levitiko 25:23-28) Naboti ankaona kuti sangachite zimene Ahabu ankafunazo. Iye anali munthu wachikhulupiriro komanso wolimba mtima, n’chifukwa chake sanalimbane ndi Ahabu, koma anangomuuza kuti sangamugulitse mundawo, chifukwa lamulo linkaletsa zimenezo.

Koma Ahabu sankaganizira n’komwe za lamulo la Yehova. Choncho anapita kunyumba kwake “ali wachisoni ndi wokhumudwa” chifukwa choti sanapeze zimene ankafuna. Baibulo limati: “Anakagona pabedi lake n’kutembenukira kukhoma, ndipo sanadye chakudya.” (1 Mafumu 21:4) Apatu Ahabu anachita zinthu ngati mwana. Yezebeli ataona zimenezi, nthawi yomweyo anaganiza zochita chiwembu chopha Naboti ndi ana ake, n’cholinga choti Ahabu apeze zimene ankafunazo.

Ukamawerenga nkhaniyi, umachita kuoneratu kuti zimene zinachitika ndi zinthu zopanda chilungamo. Yezebeli ankadziwa kuti lamulo la Mulungu linkanena kuti ngati munthu akuimbidwa mlandu waukulu, pankafunika mboni ziwiri. (Deuteronomo 19:15) Choncho, analemba makalata m’dzina la Ahabu n’kuwatumiza kwa akulu ndi anthu olemekezeka a ku Yezereeli kuti apeze amuna awiri, amene angathe kupereka umboni wabodza woti Naboti wanyoza Mulungu. Mlandu woterewu chilango chake chinkakhala imfa. N’zomvetsa chisoni kuti chiwembu chakechi chinathekadi. “Anthu awiri opanda pake,” anaperekadi umboni wabodza wonena za Naboti ndipo izi zinachititsa kuti Naboti aponyedwe miyala mpaka kufa. Koma chiwembuchi sichinathere pompo  chifukwa ana aamuna a Naboti anaphedwanso. * (1 Mafumu 21:5-14; Levitiko 24:16; 2 Mafumu 9:26) N’zomvetsa chisoni kuti Ahabu analola kuti mkazi wake achite zimenezi, zomwe zinaphetsa anthu osalakwa.

Taganizirani mmene Eliya anamvera Yehova atamuululira zimene Ahabu ndi mkazi wake anachitazi. Zimakhala zokhumudwitsa kwambiri ukaona kuti anthu oipa akonzera chiwembu anthu osalakwa, chiwembucho n’kuthekadi. (Salimo 73:3-5, 12, 13) Masiku anonso zinthu zopanda chilungamo zili ponseponse ndipo nthawi zina amachita zimenezi ndi anthu audindo amene amanena kuti akuimira Mulungu. Komabe zimene Yehova anachita, n’zolimbikitsa kwabasi. Zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi, zimatikumbutsanso kuti Yehova amaona zonse zimene zimachitika. (Aheberi 4:13) Kodi Mulungu amachita chiyani akaona anthu ena akuchita zinthu zopanda chilungamo?

“WANDIPEZA KODI MDANI WANGA?”

Pamene Yehova anauza Eliya kuti apite kwa Ahabu, anamuuza kuti: “Iye ali m’munda wa mpesa wa Naboti.” (1 Mafumu 21:18) Yezebeli atauza Ahabu kuti munda uja tsopano ndi wake, Ahabu anasangalala kwambiri ndipo anadzuka n’kupita kumundako. Sanaganize n’komwe kuti Yehova ankaona zimene zinkachitikazo. Taganizirani mmene anasangalalira atafika kumundako, n’kumauyendera uku akuganizira mbewu zosiyanasiyana zomwe amafuna kudzala m’mundawo. Koma mwadzidzidzi, Eliya anatulukira. Ahabu atangoona Eliya, nkhope yake inasinthiratu, moti anakhumudwa kwambiri n’kunena kuti, “Wandipeza kodi mdani wanga?”—1 Mafumu 21:20.

“Wandipeza kodi mdani wanga?”

Mawu a Ahabuwa akusonyeza maganizo awiri olakwika amene iyeyo anali nawo. Choyamba, pouza Eliya kuti “Wandipeza kodi?” Ahabu ankaganiza kuti Yehova sakuona zimene iye ankachitazo. Komatu Yehova anali ‘atam’peza’ kale, kapena kuti atadziwa kale zimene iye anachitazi. Yehova anaona kuti Ahabu anagwiritsa ntchito molakwika ufulu wake wosankha komanso ankasangalala ndi zotsatira za chiwembu cha Yezebeli. Yehova anaonanso kuti Ahabu ankaona kuti kukhala ndi mundawu n’kofunika kwambiri kuposa kukhala ndi makhalidwe monga chifundo ndi chilungamo. Chachiwiri, pouza Eliya kuti “mdani wanga,” Ahabu anasonyeza kuti ankadana naye. Komatu Eliya anali bwenzi la Yehova Mulungu ndipo akanathandiza Ahabu kukonzanso ubwenzi wake ndi Yehova.

Tingaphunzire zambiri pa zimene Ahabu anachitazi. Tisamaiwale kuti Yehova amaona chilichonse. Popeza iye ndi Atate wathu wachikondi, tikayamba kuchita zoipa amadziwa ndipo amafuna kuti tisinthe n’kuyamba kuchita  zabwino. Pofuna kutithandiza, amagwiritsa ntchito mabwenzi ake okhulupirika ngati Eliya, kuti atilangize pa zimene talakwitsa. Kungakhaletu kulakwa kwambiri kuona mabwenzi a Yehova ngati adani athu.—Salimo 141:5.

Ndiyeno yerekezerani kuti mukumva Eliya akumuyankha kuti: “Inde ndakupezani.” Eliya analidi atam’peza Ahabu, kutanthauza kuti anali atadziwa kuti Ahabuyo ndi munthu wakuba, wokupha, komanso anali atapandukira Yehova Mulungu. Eliya ayenera kuti anafunika kulimba mtima kuti alankhule ndi Ahabu. Kenako anamuuza mawu amene Yehova ananena. Yehova ankadziwa zoipa zonse zimene banja la Ahabu linkachita, komanso mmene zinkakhudzira anthu ena. Choncho Eliya anauza Ahabu kuti Mulungu ‘adzaseseratu’ mzere wonse wachifumu wa banja lake. Ananenanso kuti Yezebeli nayenso adzalandira chilango.—1 Mafumu 21:20-26.

Masiku ano, ena amaganiza kuti anthu oipa angathe kumangopitirizabe kuchita zinthu zopanda chilungamo popanda kulandira chilango chifukwa cha zoipa zawozo. Koma Eliya ankadziwa kuti zimenezi si zoona. Nkhani ya m’Baibulo imeneyi imatikumbutsa kuti Yehova Mulungu amaona zoipa zomwe zimachitika. Imatikumbutsanso kuti, nthawi yake amaonetsetsa kuti chilungamo chachitika. Mawu ake amatitsimikizira kuti posachedwapa adzathetsa zinthu zonse zopanda chilungamo. (Salimo 37:10, 11) Koma mwina mungadabwe kuti, ‘Kodi nthawi zonse Mulungu akaweruza anthu, amangowapatsa chilango basi? Nanga kodi pali nthawi zina pamene amawachitira chifundo?’

“KODI WAONA MMENE AHABU WADZICHEPETSERA?”

Mwina Eliya anadabwa kwambiri ndi zimene Ahabu anachita atamva za chiweruzo cha Yehova. Nkhaniyi imati: “Ahabu atangomva mawu amenewa, anang’amba zovala zake n’kuvala chiguduli. Iye anayamba kusala kudya, kugona pachiguduli ndipo anali kuyenda mwachisoni.” (1 Mafumu 21:27) Kodi Ahabu analapadi n’kusiya zoipa zimene ankachita?

Zikuoneka kuti iye anamva chisoni ndi zimene anachita. Tikutero chifukwa choti, ngakhale kuti Ahabu anali wonyada komanso wodzikuza, pa nthawiyi anadzichepetsa pamaso pa Yehova. Koma kodi Ahabu analapadi kuchokera pansi pa mtima? Taganizirani kusiyana kwa zimene Ahabu anachita ndi zimene Manase, yemwe pa nthawi ina analinso mfumu ya Isiraeli, anachita. Yehova atapereka chilango kwa Manase, Manaseyo anadzichepetsa ndipo anapempha Yehova kuti amuthandize. Koma sanalekere pomwepo. Iye anasiya makhalidwe ake oipa ndipo anachotsa mafano ake onse n’kuyamba kutumikira Yehova. Analimbikitsanso anthu ake kuchita chimodzimodzi. (2 Mbiri 33:1-17) Kodi zimene Manase anachitazi zikufanana ndi zimene Ahabu anachita atapatsidwa chilango? N’zomvetsa chisoni kuti Ahabu sanachite zimenezi.

Komabe Yehova anaona kuti Ahabu akumva chisoni ndi zinthu zoipa zimene anachita. Choncho anauza Eliya kuti: “Kodi waona mmene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga? Popeza wadzichepetsa chifukwa cha ine, sindidzabweretsa tsokali m’masiku ake. M’malomwake, ndidzalibweretsa panyumba yake m’masiku a mwana wake.” (1 Mafumu 21:29) Kodi apa Yehova ankatanthauza kuti wamukhululukira Ahabu? Ayi, chifukwa Yehova amakhululukira munthu pokhapokha ngati munthuyo walapadi kuchokera pansi pa mtima. (Ezekieli 33:14-16) Koma popeza Ahabu anasonyeza kuti akumva chisoni ndi zimene anachita, Yehova anamusonyezanso chifundo mogwirizana ndi zimenezo. Choncho Yehova ananena kuti amuchitira chifundo ndipo sadzawononga anthu a m’nyumba yake m’masiku ake.

Komabe Yehova sanasinthe chilango chimene ananena kuti adzamupatsa. Kenako Yehova anakambirana ndi angelo ake kuti apeze njira yabwino yopusitsira Ahabu kuti apite kunkhondo kumene akaphedwe. Pasanapite nthawi, zimene Yehova ananena kuti zidzachitikira Ahabu zinachitikadi. Ahabu anapita kunkhondo ndipo anavulazidwa kwambiri ndi adani ake. Iye anakwera galeta lake magazi ali chuchuchu, ndipo kenako anafa. Nkhaniyi imati, pamene anthu ankatsuka galetalo, agalu ankanyambita magazi a Ahabu omwe anadonthera pansi. Izi zinakwaniritsa mawu a Yehova amene Eliya anauza Ahabu akuti: “Pamalo amene agalu ananyambita magazi a Naboti, pomweponso agalu adzanyambita magazi ako, a iweyo.”—1 Mafumu 21:19; 22:19-22, 34-38.

Kwa Eliya, Elisa komanso anthu ena okhulupirika, zimene zinachitikira Ahabuzi zinawatsimikizira kuti Mulungu sanaiwale kukhulupirika komanso kulimba mtima kwa Naboti. Yehova ndi Mulungu wachilungamo ndipo nthawi zonse amapereka chilango kwa anthu oipa. Koma amachita zimenezi pa nthawi yake. Komabe akamapereka chiweruzo chake, amasonyezanso chifundo ngati pakufunika kutero. (Numeri 14:18) Izi zinali zolimbikitsa kwambiri kwa Eliya, chifukwa kwa zaka zambiri anatumikira Yehova mokhulupirika pa nthawi yonse ya ulamuliro wa mfumu yoipayi. Kodi inunso anthu ena anakuchitiranipo zinthu zopanda chilungamo? Kodi mumalakalaka Yehova atakonza zinthu? Mungachite bwino kutsanzira chikhulupiriro cha Eliya. Iye limodzi ndi Elisa, mtumiki wake wokhulupirika, anapitirizabe kuuza anthu uthenga wochokera kwa Mulungu komanso anakhalabe wokhulupirika ngakhale kuti anthu ena ankachita zinthu zopanda chilungamo.

^ ndime 3 Yehova anali atachititsa kuti m’dzikoli mugwe chilala kwa zaka zitatu ndi hafu, n’cholinga choti anthu adziwe kuti Baala anali mulungu wopanda mphamvu. Anthu amene ankalambira Baala ankakhulupirira kuti ndi mulungu wogwetsa mvula komanso wothandiza kuti nthaka ikhale ndi chonde. (1 Mafumu chaputala 18) Onani nkhani zakuti, “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo” mu Nsanja ya Olonda ya January 1 ndi April 1, 2008.

^ ndime 13 Naboti ataphedwa, n’kutheka kuti Yezebeli anaganiza kuti mundawo upita kwa ana ake, choncho mwina anakonzanso kuti ana aamuna a Naboti aphedwenso. Kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu amalola kuti anthu osauka aziponderezedwa, werengani nkhani yakuti “Zimene Owerenga Amafunsa” patsamba 11.