Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI BAIBULO LILI NDI UTHENGA WOTANI?

Zimene Zinachitika Kuti Tizikumana ndi Mavuto

Zimene Zinachitika Kuti Tizikumana ndi Mavuto

Buku la Genesis, lomwe ndi loyamba m’Baibulo, limafotokoza mwachidule koma momveka bwino chimene chinachitika kuti dzikoli likhalepo. Limati: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Mulungu atalenga nyama ndi zomera, analenga anthu awiri oyamba, omwe ndi Adamu ndi Hava. Anthuwa anali osiyana ndi zinyama chifukwa anali ndi ena mwa makhalidwe amene Mulungu ali nawo, kuphatikizapo ufulu wosankha zochita. Choncho, zinthu zikanawayendera bwino kapena ayi potengera zimene asankha. Ngati akanasankha kutsatira zimene Mulungu anawauza, akanatha kukhala makolo oyamba a anthu angwiro omwe akanadzaza padziko lonse lapansi. Iwo akanakhala mwamtendere mpaka kalekale mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.

Koma mngelo wina anali ndi maganizo olakwika ndipo kuti zomwe amafunazo zitheke, anagwiritsa ntchito anthu oyambawo. Choncho mngelo ameneyu anadzayamba kutchedwa Satana, kutanthauza “Wotsutsa.” Satana analankhula ndi Hava kudzera mwa njoka ndipo anam’pusitsa pomuuza kuti zinthu zikhoza kumuyendera bwino ngati atamachita zinthu mosatsogoleredwa ndi Mulungu. Adamu ndi Hava anatsatira maganizo a Satana ndipo zimenezi zinachititsa kuti asakhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Mlengi wawo. Zimene anachitazi zinachititsa kuti asakhalenso ndi moyo mpaka kalekale, ndipo anatipatsira tonse uchimo komanso imfa.

Nthawi yomweyo Mulungu ananeneratu kuti akufuna kukonzanso zinthu komanso kupatsa ana a Adamu mwayi wodzakhala ndi moyo kosatha. Mulungu analosera zoti “mbewu,” idzawononga Satana komanso idzathetsa mavuto onse amene anayamba chifukwa cha Satana, Adamu ndiponso Hava. (Genesis 3:15) Patapita nthawi zinadziwika kuti “mbewu” imeneyi ndi ndani.

Mbewuyi isanadziwike, Satana anayesetsa kulepheretsa cholinga chabwino chimene Mulungu anali nacho. Iye anachititsa kuti anthu oipa achuluke kwambiri. Kenako Mulungu anakonza zobweretsa chigumula n’cholinga choti awononge anthu oipa onse. Mulungu anauza Nowa, yemwe anali wolungama, kuti akonze chingalawa choti adzapulumukiremo iyeyo, banja lake komanso zinyama zina zimene anauzidwa kuti adzazilowetse m’chingalawamo. Chingalawacho chinali ngati chibokosi chachikulu.

Nowa ndi banja lake anatuluka m’chingalawamo patadutsa chaka chathunthu kuchokera pamene chigumulacho chinayamba ndipo pa nthawiyi anthu onse oipa anali atawonongedwa. Koma “mbewu” ija inali isanadziwikebe.

Nkhaniyi yachokera m’mabuku a Genesis chaputala 1 mpaka 11; Yuda 6, 14, 15; Chivumbulutso 12:9.