Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 YANDIKIRANI MULUNGU

“Makhalidwe a Mulungu Osaoneka ndi Maso Akuonekera Bwino”

“Makhalidwe a Mulungu Osaoneka ndi Maso Akuonekera Bwino”

Kodi mumakhulupirira kuti kuli Mulungu? Ngati mumakhulupirira kuti kuli Mulungu, n’chiyani chimakupangitsani kukhulupirira zimenezi? Pali zinthu zambiri zimene zimatitsimikizira kuti kuli Mulungu yemwe ndi Mlengi wanzeru, wamphamvu komanso wachikondi. Kodi zinthu zimenezi ndi ziti, ndipo zimatitsimikizira bwanji kuti Mulungu alipodi? Kuti tipeze yankho, tiyeni tione mawu amene mtumwi Paulo analemba m’kalata yopita kwa Akhristu a ku Roma.

Paulo ananena kuti: “Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu.” (Aroma 1:20) Pa lembali, Paulo anasonyeza kuti makhalidwe a Mulungu amaonekera pa zimene analenga. Tiyeni tione zimene Paulo ankatanthauza.

Paulo ananena kuti makhalidwe a Mulungu anayamba kuonekera “chilengedwere dziko kupita m’tsogolo.” Mawu a m’Chigiriki akuti “dziko” palembali samatanthauza dziko lapansili koma amatanthauza anthu. * Choncho Paulo ankatanthauza kuti kuyambira pamene anthu analengedwa, anthuwo akhala akuona makhalidwe a Mulungu poona zimene analenga.

Makhalidwe amenewa si obisika ndipo “akuonekera bwino.” Zinthu zing’onozing’ono komanso zikuluzikulu zimene Mulungu analenga zimasonyeza kuti kuli Mlengi komanso kuti ali ndi makhalidwe abwino. Mwachitsanzo, zinthu zimene Mulungu analenga komanso mmene anazilengera zimasonyeza kuti ndi wanzeru. Nyenyezi komanso zinthu zina ngati madzi a m’nyanja zimasonyeza kuti Mulungu ndi wamphamvu ndipo zakudya zokoma komanso kukongola kwa dzuwa likamalowa ndi kutuluka, zimasonyeza kuti Mulungu amakondadi anthu.—Salimo 104:24; Yesaya 40:26.

Maumboniwa ndi osavuta kuwaona moti anthu amene sakhulupirira kuti kuli Mulungu alibe “chifukwa chomveka.” Munthu wina ananena kuti: “Anthu amene sakhulupirira kuti kuli Mulungu amafanana ndi dalaivala yemwe wasankha dala kusamvera chikwangwani chomwe chalembedwa kuti “Tatseka msewu, dutsani msewu wakumanzere.” Ngati wapolisi atamugwira n’kumuuza kuti alipire, kodi zingakhale zomveka kuti dalaivalayo akane kulipira chifukwa chakuti sanaone chikwangwanicho? Chifukwa chakecho sichingakhale chomveka chifukwa chikwangwanicho chili poonekera kwambiri komanso dalaivalayo si wakhungu. Komanso ndi udindo wa dalaivalayo kuona ndi kutsatira zikwangwani za mumsewu. Chilengedwe chili ngati chikwangwani chomwe chili pamalo oonekera. Chimasonyeza mosavuta kuti kuli Mulungu. Choncho palibe amene anganene kuti saona umboni woti kuli Mulungu.

Makhalidwe a Mulungu amaonekera pa zimene analenga

N’zoona kuti chilengedwe chimatiuza zambiri zokhudza Mlengi wathu. Koma pali buku lina lomwe limatiuzanso zambiri. Bukuli ndi Baibulo. Kuwerenga Baibulo kungatithandize kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri ngati awa: Kodi Mulungu analengeranji dziko lapansili? Kodi analengeranji anthu? Kudziwa mayankho a mafunso amenewa kungatithandize kuti tiyandikire Mulungu yemwe ‘makhalidwe ake osaoneka ndi maso akuonekera bwino.’

Mavesi amene mungawerenge mu August

Aroma 1-16

^ ndime 5 Malemba ena m’Baibulo amanena kuti “dziko” ndi lochimwa ndipo lifunika mpulumutsi, zomwe zikusonyeza kuti nthawi zina mawu akuti dziko amatanthauza anthu osati dziko lapansili.—Yohane 1:29; 4:42; 12:47.