Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

MTSIKANA wina anali pa ntchito yapamwamba koma analibe chidwi ndi za Mulungu. Kodi n’chiyani chinathandiza mtsikana ameneyu kuti ayambe kukonda za Mulungu? Nanga ndi zinthu ziti zokhudza imfa zimene mnyamata wina, yemwe anali wakatolika, anaphunzira zomwe zinam’thandiza kuti asinthe moyo wake? Komanso kodi ndi zinthu ziti zokhudza Mulungu zimene mnyamata wina, yemwe sankasangalala ndi moyo, anaphunzira zomwe zinachititsa kuti asinthe n’kukhala wa Mboni? Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene anthuwa ananena.

“Kwa zaka zambiri ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu anatilengeranji anthufe?’”​—ROSALIND JOHN

  • CHAKA CHOBADWA: 1963

  • DZIKO: BRITAIN

  • POYAMBA: NDINALI PA NTCHITO YAPAMWAMBA

KALE LANGA:

Ndinabadwira kudera la Croydon, ku South London. M’banja mwathu tilipo ana 9 ndipo ine ndine wa nambala 6. Makolo anga kwawo ndi kuchilumba cha Caribbean cha ku St. Vincent. Mayi anga ankapita ku tchalitchi cha Methodist. Koma ineyo ndinalibe chidwi ndi za Mulungu ngakhale kuti mwachibadwa ndinkakonda kuwerenga kuti ndidziwe zinthu zosiyanasiyana. Nthawi zambiri ndikakhala pa holide ndinkapita kunyanja ndipo ndinkakonda kuwerenga mabuku osiyanasiyana amene ndinkabwereka kulaibulale.

Nditamaliza sukulu, ndinayamba kuganizira mmene ndingathandizire anthu ovutika. Choncho ndinayamba kuthandiza anthu osowa pokhala komanso olumala. Kenako ndinayamba kuchita maphunziro azachipatala. Nditamaliza maphunziro apamwambawa, ndinakhala ndi mwayi wogwira ntchito zapamwamba zosiyanasiyana ndipo ndinkakhala moyo wawofuwofu. Ngakhale kuti ntchito yanga inali ya ndalama zambiri ndipo ndinkagwirira ntchito makampani komanso mabungwe osiyanasiyana ngati mlangizi, inali yofewa moti ndinkangogwiritsa ntchito kompyuta ya laputopu komanso Intaneti. Ndinkapita kumayiko akunja pa ndege n’kukakhala milungu ingapo kuhotelo yodula ndi yokongola komanso yokhala ndi malo ochitira masewera olimbitsa thupi. Kunena zoona moyo unkandikomera kwambiri. Komabe sindinaiwale cholinga changa chofuna kuthandiza anthu ovutika.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Kwa zaka zambiri ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu anatilengeranji anthufe, nanga cholinga cha moyo n’chiyani?’ Koma ndinali ndisanayesepo kupeza mayankho a mafunso amenewa m’Baibulo. Tsiku lina mu 1999, mchemwali wanga dzina lake Margaret ndi mnzake wina, omwe ndi a Mboni za Yehova anabwera kudzandiona. Mnzakeyo anali wachikondi komanso wokoma mtima ndipo anandipempha kuti ayambe kundiphunzitsa Baibulo. Ndinavomera, komabe ndinalibe chidwi kwenikweni ndi phunziroli chifukwa ntchito yanga komanso moyo umene ndinkakhala zinkapangitsa kuti ndisamakhale ndi nthawi yokwanira yophunzira.

M’chaka cha 2002, ndinasamukira kum’mwera chakumadzulo kwa England. Kumeneko, ndinayambanso sukulu ina n’cholinga choti ndiwonjezere maphunziro anga kuti ndipezenso digiri ina yapamwamba. Ine ndi mwana wanga tinayamba kusonkhana ndi Mboni za Yehova mlungu uliwonse ku Nyumba ya Ufumu. Ngakhale kuti ndinkasangalala ndi zimene ndinkaphunzira kuyunivesite, ndinkaona kuti kuphunzira Baibulo kunkandithandiza kumvetsa mavuto amene timakumana nawo pa moyo komanso zimene tingachite tikakumana ndi mavutowo. Ndinazindikira kuti mfundo ya palemba la Mateyu 6:24, yoti sungatumikire ambuye awiri, ndi yoona. Uyenera kusankha kutumikira Mulungu kapena chuma. Choncho ndinaona kuti ndiyenera kusankha zinthu mwanzeru.

M’chaka cha 2001, ndinkakonda kukasonkhana ku kagulu ka phunziro la Baibulo ka Mboni za Yehova komwe tinkaphunzira buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You? * Ndinayamba kukhulupirira kuti ndi Mlengi yekha Yehova, amene angathetse mavuto a anthu. Koma kusukulu kuja ankatiphunzitsa kuti moyo wabwino sumadalira Mlengi. Zimenezi zinandikwiyitsa kwambiri. Choncho nditangophunzira miyezi iwiri yokha ndinaganiza zosiya kuphunzira kuyunivesiteko kuti ndizikhala ndi nthawi yokwanira yochitira zinthu zauzimu.

Lemba limene linandithandiza kwambiri kuti ndisinthe moyo wanga ndi la Miyambo 3:5, 6, limene limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.” Ndinaona kuti ndinapeza madalitso ambiri chifukwa chophunzira za Mulungu wachikondi kuposa kukhala ndi chuma kapena kutchuka chifukwa cha maphunziro apamwamba. Pamene ndinapitiriza kuphunzira za cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansi komanso zimene Yesu anachita popereka moyo wake chifukwa cha anthufe, m’pamenenso ndinkafuna kudzipereka kuti ndiyambe kutumikira Mlengi wathu Yehova. Ndipo mu April 2003, ndinabatizidwa. Nditabatizidwa ndinayamba kusintha zina ndi zina pa moyo wanga.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Ndimaona kuti ubwenzi wanga ndi Yehova ndi chinthu cha mtengo wapatali. Kudziwa Yehova komanso kusonkhana ndi a Mboni anzanga kwandithandiza kuti ndikhale ndi mtendere wamumtima komanso kuti ndikhale wosangalala.

Zimene ndimaphunzira m’Baibulo komanso pamisonkhano ya Mboni zimandithandiza kupeza zosowa zanga zauzimu. Ndimasangalalanso ndikamaphunzitsa ena za Yehova. Ntchito yothandiza anthu kudziwa za Yehova, ndimaitenga ngati ntchito yanga. Panopo ndimaona kuti ndikuthandizadi anthu chifukwa ntchito imeneyi imawathandiza kukhala ndi moyo wabwino panopo ndiponso kukhala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano. Kuyambira mu June 2008, ndakhala ndikuthera nthawi yambiri ndikugwira ntchito yotumikira Mulungu ndipo ndikuona kuti zimenezi zapangitsa kuti ndikhale wosangalala kwambiri kuposa kale. Tsopano ndapeza cholinga chenicheni cha moyo ndipo ndimayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha zimenezi.

“Imfa ya mnzanga inandikhudza kwambiri.”—ROMAN IRNESBERGER

  • CHAKA CHOBADWA: 1973

  • DZIKO: AUSTRIA

  • POYAMBA: NDINKATCHOVA JUGA

KALE LANGA:

Ndinakulira m’tawuni ina yaing’ono yotchedwa Braunau, ku Austria. Anthu a m’dera limeneli anali olemera kwambiri ndipo m’derali simunkachitikachitika zachiwawa. Banja lathu linali lakatolika ndipo inenso ndinali wakatolika.

Zimene zinachitika ndili wamng’ono zinandikhudza kwambiri. Tsiku lina mu 1984 ndili ndi zaka 11, ndinkasewera mpira ndi mnzanga. Koma masana a tsiku lomwelo, mnzangayo anafa pa ngozi yagalimoto. Imfa ya mnzangayu inandikhudza kwambiri. Kwa zaka zambiri chichitikireni ngozi imeneyi, ndinkadzifunsa kuti kodi chidzandichitikire n’chiyani ndikadzamwalira?

Nditasiya sukulu ndinayamba kugwira ntchito ya zamagetsi. Ngakhale kuti ndinkakonda kutchova juga ndipo nthawi zina ndinkaluza ndalama zambiri, sindinkasowa ndalama. Ndinkakondanso kwambiri masewera komanso ndinayamba kukonda nyimbo zaphokoso kwambiri za mawu otukwana. Ndinkangokhalira kupita kumalo azisangalalo, kumapate komanso ndinkakonda kuchita zachiwerewere. Ndinkachita zonsezi kuti ndizisangalala koma sizinandithandize kukhala wosangalala.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Mu 1995, bambo ena achikulire a Mboni anafika panyumba panga ndipo anandipatsa buku limene linali ndi yankho la m’Baibulo la funso lakuti, Kodi n’chiyani chimachitika munthu akamwalira? Chifukwa choti ndinkaganizirabe za imfa ya mnzanga uja, ndinalandira bukuli. Ndinawerenga buku lonse osati mutu wokha umene unali ndi nkhani yokhudza imfa.

Zimene ndinawerenga zinayankha mafunso anga okhudza imfa. Komanso ndinaphunzira zambiri m’bukuli. Popeza ndinakulira m’banja lakatolika, ndinkakhulupirira kwambiri Yesu ndipo ndinkamuona ngati Mulungu. Koma kuphunzira Baibulo kunandithandiza kuti ndikhale pa ubwenzi ndi Yehova Mulungu, yemwe ndi Atate wa Yesu. Ndinasangalala kwambiri nditadziwa kuti Yehova sadzibisa ndipo aliyense amene akufuna kumudziwa akhoza kumudziwa. (Mateyu 7:7-11) Ndinaphunziranso kuti Yehova amasangalala kapena kukhumudwa ndi zochita zathu komanso kuti iye amakwaniritsa zimene walonjeza. Zimenezi zinachititsa kuti ndizichita chidwi kwambiri ndi maulosi a m’Baibulo komanso kuti ndiyambe kufufuza mmene maulosi ena anakwaniritsidwira. Zimene ndinapeza, zinachititsa kuti ndizikhulupirira kwambiri Mulungu.

Pasanapite nthawi ndinazindikira kuti a Mboni za Yehova okha ndi amene amathandiza anthu kumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa. Ndinkawerenga m’Baibulo langa lachikatolika mavesi amene ndinkawapeza m’mabuku a Mboni ndipo ndikamachita zimenezi m’pamenenso ndinkaona kuti ndapezadi choonadi.

Zimene ndinaphunzira m’Baibulo zinandithandiza kudziwa kuti Yehova amafuna kuti ndizitsatira mfundo za m’Baibulo. Nditawerenga lemba la Aefeso 4:22-24 ndinaona kuti ndiyenera kuvula “umunthu wakale” umene ‘unkagwirizana ndi khalidwe langa lakale,’ ndipo ndiyenera “kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.” Choncho ndinasiya khalidwe langa lachiwerewere. Ndinaonanso kuti ndiyenera kusiya juga chifukwa imachititsa munthu kukhala wokonda ndalama komanso wadyera. (1 Akorinto 6:9, 10) Koma ndinazindikira kuti zimenezi zingatheke pokhapokha nditasiya kucheza ndi anzanga akale n’kuyamba kucheza ndi anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo.

Koma sizinali zophweka kuti ndisinthe. Komabe ndinayamba kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova ndiponso ndinayamba kucheza ndi a Mboniwo. Ndinapitirizanso kuphunzira Baibulo pandekha. Zonsezi zinandithandiza kuti ndisiye kumvetsera nyimbo zoipa zija, ndisinthe zolinga zanga pa moyo komanso kaonekedwe kanga. M’chaka cha 1995, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Panopa ndimaona ndalama ndi chuma moyenera. Komanso poyamba ndinali wosachedwa kupsa mtima koma pano ndinasintha. Tsopano sindideranso nkhawa kwambiri za m’tsogolo.

Ndikusangalala kwambiri kukhala m’gulu la anthu amene akutumikira Yehova. Pa anthu amenewa, pali ena omwe ali ndi mavuto osiyanasiyana koma akupitirizabe kutumikira Mulungu mokhulupirika. Ndimasangalala kwambiri chifukwa panopa ndikugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zanga potumikira Yehova ndi kuchitira ena zabwino osati pokwaniritsa zofuna zanga basi.

“Tsopano ndinapeza cholinga cha moyo wanga.”​—IAN KING

  • CHAKA CHOBADWA: 1963

  • DZIKO: ENGLAND

  • POYAMBA: SINDINKASANGALALA NDI MOYO

KALE LANGA:

Ndinabadwira ku England, koma ndili ndi zaka 7 banja lathu linasamukira ku Australia. Tinakakhala kudera lina lotchedwa Gold Coast, m’chigawo cha Queensland. Kuderali kumapita alendo ambiri okaona malo. Ngakhale kuti banja lathu silinali lolemera, sitinkasowa zinthu zofunika pa moyo.

Ngakhale kuti sindinakule movutika, sindinkasangalala ndi moyo. Bambo anga anali chidakwa chadzaoneni. Sindinkawakonda chifukwa cha khalidwe lawoli komanso chifukwa choti ankachitira nkhanza amayi anga. Nditakula ndinamva zimene bambo anga anakumana nazo pa nthawi imene anali msilikali ku Malaya, ndipo zimenezi zinandithandiza kuti ndimvetse chifukwa chake anali chidakwa komanso ankhanza.

Nditayamba maphunziro a ku sekondale, inenso ndinayamba kumwa mowa mwauchidakwa. Ndili ndi zaka 16 ndinasiya sukulu ndipo ndinalowa m’gulu la asilikali apanyanja. Ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kusuta kwambiri fodya. Ndipo sindinkatha kukhala popanda kumwa mowa. Poyamba ndinkamwa kumapeto kwa mlungu basi, koma tsopano ndinayamba kumwa tsiku lililonse.

Ndili ndi zaka pafupifupi 20 ndinayamba kukayikira ngati Mulungu alikodi. Ndinkaganiza kuti: ‘Ngati kulidi Mulungu, n’chifukwa chiyani amalola kuti anthu azivutika?’ Ndinafika mpaka polemba ndakatulo yoimba mlandu Mulungu chifukwa cha zoipa zimene zili padzikoli.

Ndili ndi zaka 23, ndinachoka m’gulu la asilikali lija. Kenako ndinagwira ntchito zosiyanasiyana ndipo mpaka ndinapita kunja komwe ndinakakhalako kwa chaka chimodzi, koma sindinkasangalalabe ndi moyo. Ndinalibe cholinga chilichonse pa moyo wanga ndipo palibe chomwe chinkandisangalatsa. Ndinalibe nazo ntchito zoti ndikhale ndi nyumba yangayanga, ndipeze ntchito yokhazikika kapena ndikwezedwe pa ntchito. Zimene ndinkaona ngati zikundisangalatsako zinali kumwa mowa komanso kumvetsera nyimbo basi.

Ndimakumbukira nthawi imene ndinalakalaka nditadziwa cholinga cha moyo. Ndinali ndili ku Poland pamene ndinapita kundende ina yotchedwa Auschwitz, imene inkadziwika kuti ankazunzako anthu. Ndinali nditawerenga nkhani zosiyanasiyana zonena za zinthu zoipa zimene zinkachitika pandendeyi. Koma nditafika kundendeyi n’kuona kukula kwake komanso zimene zinkachitika, zinandikhudza kwambiri. Sindinamvetse kuti n’chifukwa chiyani anthu ankachitira nkhanza anthu anzawo choncho. Ndikukumbukira kuti pomwe ndinkayenda n’kumaona zimene zinkachitika pandendeyi, misozi inkangotsika ndipo ndinkadzifunsa kuti ‘Kodi n’chifukwa chiyani zinthu zimenezi zikuchitika?’

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

M’chaka cha 1993, nditabwereranso ku Australia, ndinayamba kuwerenga Baibulo kuti ndipeze yankho la funso limeneli. Pasanapite nthawi, a Mboni za Yehova awiri anafika panyumba panga ndipo anandiitanira kumsonkhano wawo womwe unachitikira kusitediyamu yapafupi. Ndinaganiza zopita kumsonkhanowu.

Miyezi ingapo m’mbuyomo, ndinalinso pasitediyamu yomweyi kuonera mpira, koma zimene ndinaona pa nthawi ya msonkhanowu zinali zosiyana kwambiri. Ndinaona kuti a Mboni anali anthu aulemu komanso anavala bwino ndipo ana awo anali akhalidwe labwino. Komanso ndinadabwa kwambiri ndi zimene ndinaona pa nthawi yopuma. Anthu ambiri amene anali pamsonkhanowu anadyera pagalaundi koma pamene chigawo chamasana chinkayamba, pagalaundipo panalibe ngakhale chinyalala chimodzi. Chomwe chinandichititsa chidwi kwambiri n’choti anthuwa ankaoneka kuti ali ndi chimwemwe komanso mtendere wamumtima, zinthu zomwe ineyo ndinkazilakalaka kwa nthawi yaitali. Sindikumbukira nkhani iliyonse imene inakambidwa pamsonkhanowu, koma sindidzaiwala khalidwe labwino lomwe a Mboni anasonyeza.

Tsiku limenelo ndinakumbukira msuwani wanga amene ankawerenga Baibulo komanso kufufuza zokhudza zipembedzo zosiyanasiyana. Zaka zingapo m’mbuyomo iye anandiuza kuti Yesu ananena kuti tingathe kuzindikira chipembedzo choona malinga ndi zipatso zake. (Mateyu 7:15-20) Ndinaganiza zofufuza zimene zimachititsa kuti a Mboni akhale osiyana ndi ena onse. Zotsatira zake zinali zoti, kwa nthawi yoyamba, ndinayamba kuona kuti ndingathe kukhala ndi tsogolo labwino.

Mlungu wotsatira, a Mboni amene anandiitanira kumsonkhano aja anabweranso kunyumba kwathu. Ndinavomera atandipempha kuti ndiziphunzira nawo Baibulo. Ndinayambanso kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova.

Nditayamba kuphunzira Baibulo, maganizo anga pa nkhani yokhudza Mulungu anasintha kwambiri. Ndinaphunzira kuti Mulungu si amene amachititsa mavuto padzikoli ndipo iye sasangalala anthu akamachita zoipa. (Genesis 6:6; Salimo 78:40, 41) Sindinkafuna kuchitanso zinthu zokhumudwitsa Yehova koma ndinkafunitsitsa kumusangalatsa. (Miyambo 27:11) Ndinasiya kumwa mowa mwauchidakwa, kusuta fodya komanso kuchita zachiwerewere. M’March 1994, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Panopa ndine wosangalala komanso wokhutira ndi zimene ndikuchita. Sindimwanso mowa pofuna kuti ndiiwale mavuto chifukwa ndinaphunzira kupemphera kwa Yehova kuti azindithandiza ndikakhala ndi nkhawa.—Salimo 55:22.

Zaka 10 zapitazo ndinakwatira mkazi wokongola yemwenso ndi wa Mboni, dzina lake Karen. Ine ndi mkazi wangayu timasangalala kulera mwana wanga wopeza, dzina lake Nella. Tonse timatha nthawi yathu yambiri tikulalikira komanso kuthandiza anthu kuti adziwe Mulungu. Ndikuona kuti panopa ndinapeza cholinga cha moyo wanga.

^ ndime 11 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.