Kucheza ndi Munthu Wina
Kucheza ndi Munthu Wina
A MBONI ZA YEHOVA amakonda kukambirana ndi anthu nkhani za m’Baibulo. Kodi mumafuna kudziwa zimene Baibulo limanena pa nkhani inayake? Kapenanso kodi mumafuna kudziwa zambiri zokhudza zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira ndiponso chifukwa chake amakhulupirira zimenezo? Ngati ndi choncho, dzafunseni wa Mboni za Yehova aliyense amene mungadzakumane naye. Adzasangalala kukambirana nanu nkhani zimenezi.
Tiyeni tione mmene wa Mboni za Yehova angachezere ndi munthu wina. Tiyerekeze kuti bambo ena a Mboni, dzina lawo a Patrick, afika pakhomo pa a Benard.
Kodi Mulungu Adzalanga Anthu Oipa?
A Patrick: Ndasangalala kuti takumananso.
A Benard: Inenso ndasangalala kuti mwabwera.
A Patrick: Ndakhala ndikuganizira kwambiri za nkhani imene munanena tsiku lijali.
A Benard: Nkhani yake iti?
A Patrick: Munanena kuti munadabwa kwambiri kumva kuti a Mboni za Yehova sakhulupirira zoti Mulungu adzawotcha anthu ochimwa.
A Benard: Zinandidabwitsadi. Kunena zoona, n’zovuta kwa ineyo kumvetsa kuti n’chifukwa chiyani simukhulupirira zimenezi.
A Patrick: Zikomo chifukwa chomasuka kunena zimenezi. Popeza anthu amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhaniyi, kodi inuyo mumakhulupirira zotani?
A Benard: Ndimakhulupirira kuti anthu oipa akafa amapita kumoto ndipo amakazunzika mpaka kalekale.
A Patrick: Zimenezi n’zimenenso anthu ambiri amakhulupirira. Koma n’takufunsani, kodi munakumanapo ndi zinthu zilizonse zoipa pa moyo wanu?
A Benard: Inde. Mchemwali wanga anaphedwa zaka zisanu zapitazo.
A Patrick: Iii, pepani kwambiri. Muyenera kuti mudakali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya mchemwali wanuyo.
A Benard: N’zoona, zimandivutabe kuiwala.
A Patrick: Zoipa zimene zawachitikira anthu ambiri zimawachititsa kuganiza zoti anthu oipa adzalangidwa kumoto. Ndipotu anthu osalakwa amafunitsitsa amene amawachitira zinthu zoipa atalangidwa chifukwa cha zoipa zawozo.
A Benard: Ndi mmenedi ziyenera kukhalira. Ineyo ndimafunitsitsa kuti munthu amene anapha mchemwali wangayo adzalangidwe basi.
A Patrick: Ndi mmene aliyense amamvera. Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu nayenso amakhumudwa kwambiri akamaona osalakwa akuzunzidwa ndi anthu oipa ndipo analonjeza kuti adzalanga anthu oipa. Taonani zimene lemba la Yesaya 3:11 limanena. Lembali limati: “Tsoka kwa anthu oipa! Iwo adzaona zoopsa, chifukwa zimene anachitira ena ndi manja awo, zidzawachitikira iwowo.” Choncho tikhale ndi chikhulupiriro choti Mulungu adzalangadi anthu ochita zoipa.
A Benard: Ndiye ngati mukuti kulibe moto, nanga Mulungu adzawalanga bwanji anthu oipawa?
2 Atesalonika 1:9. Kodi mungawerenge?
A Patrick: Limeneli ndi funso labwino. Yankho losapita m’mbali ndi lakuti, Mulungu adzalanga anthu oipa powawononga moti sadzakhalanso ndi moyo. Tiyeni tione zimene Baibulo limanena palemba ili, laA Benard: Eee, ndikhoza kuwerenga. Likuti: “Amenewa adzawaweruza kuti alandire chilango cha chiwonongeko chamuyaya, kuwachotsa pamaso pa Ambuye.”
A Patrick: Mwaona, lembali likusonyeza kuti anthu oipa alibe chiyembekezo chifukwa Mulungu adzawapatsa chilango ndipo chilango chake n’chakuti sadzawalolanso kuti akhale ndi moyo. Kunena kwina tingati iwo alibe chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha.
A Benard: Ndamvetsa tanthauzo la lembali. Komabe ndikuona kuti pamenepa palibe chilungamo. Ndikutero chifukwa anthu abwino ndi oipa omwe amafa. Ndiye kodi sizingakhale bwino kuti anthu oipa alandire chilango choposa kungofa basi?
Yehova Ndi Mulungu Wachilungamo
A Patrick: Ndaona kuti mumakonda chilungamo.
A Benard: Kwambiri.
A Patrick: Mumachita bwino. Anthufe timafuna zinthu zizichitika mwachilungamo chifukwa ndi mmene Mulungu anatilengera. Nayenso amakonda kwambiri chilungamo. Koma atsogoleri achipembedzo akamaphunzitsa kuti Mulungu amalanga anthu kumoto, amakhala akusonyeza kuti Mulungu ndi wopanda chilungamo.
A Benard: Mukutanthauza chiyani pamenepa?
A Patrick: Mwina ndikupatseni chitsanzo. Ndikukhulupirira kuti mukuidziwa bwino nkhani ya m’Baibulo yonena za Adamu ndi Hava.
A Benard: Eee, ndikuidziwa bwino nkhani imeneyi. Mulungu anawaletsa kuti asadye chipatso cha mtengo winawake, koma iwo sanamvere.
A Patrick: Mwafotokoza bwino. Tiyeni tiwerengere limodzi lemba la Genesis 2:16, 17 kuti tione zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. Lembali likuti: “Yehova Mulungu anapatsa munthuyo lamulo lakuti: ‘Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.’” Kodi Mulungu anati n’chiyani chomwe chidzachitikire Adamu akadya chipatso choletsedwacho?
A Benard: Ananena kuti adzafa.
A Patrick: Mwayankha bwino. Ndiye tangoganizani, tchimo la Adamu linachititsa kuti anthu onse padzikoli azibadwa ochimwa. * Komabe, kodi Mulungu anamuuza kuti adzamulanga kumoto chifukwa cha zimenezi?
A Benard: Ayi.
A Patrick: Koma kodi zikanakhala kuti Adamu ndi Hava adzawotchedwa kumoto akadya chipatso chija, Mulungu sakanawauziratu zimenezo? Kodi Mulungu akanapanda kuwauziratu chikanakhala chilungamo?
A Benard: Ndikuona kuti ayi.
A Patrick: Komanso tiyeni tione zimene Mulungu ananena Adamu ndi Hava atachimwa. Kodi mungawerenge lemba la Genesis 3:19?
A Benard: Lembali likuti: “Udzadya chakudya kuchokera m’thukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa. Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”
A Patrick: Zikomo kwambiri. Malinga ndi zimene Mulungu ananenazi, kodi Adamu atafa anapita kuti?
A Benard: Anakhalanso fumbi.
A Patrick: Mwayankha bwino. Ndiye kodi mukamamuuza munthu kuti abwerere kumalo enaake, si ndiye kuti munthuyo anali kumalowo poyamba?
A Benard: Eee, ndi choncho.
A Patrick: Ndiye kodi Mulungu asanalenge Adamu, Adamuyo anali kuti?
A Benard: Ndiye kuti anali fumbi.
A Patrick: Mwayankha bwino. Ndipo monga taonera palembali, Mulungu popereka chiweruzo kwa Adamu sanatchulepo za moto. Kodi chikanakhala chilungamo ngati Mulungu akanauza Adamu kuti adzabwerera kufumbi, koma zoona zake zili zoti adzapita kukalangidwa kumoto?
A Benard: Ayi, chimenecho sichikanakhala chilungamo.
Kodi Mdyerekezi Amachita Zofuna za Mulungu?
A Patrick: Palinso mfundo ina yofunika kuiganizira pa nkhani ya chiphunzitso choti anthu amalangidwa kumoto.
A Benard: Mfundo yotani?
A Patrick: Kodi anthu ambiri amakhulupirira kuti anthu oipa akapita kumoto, ndani amene amawawotcha?
A Benard: Satana Mdyerekezi.
A Patrick: Komatu Mdyerekezi ndi mdani wamkulu wa Mulungu. Ngati Mulungu amapititsa anthu oipa kumoto kuti akazunzidwe ndi Mdyerekezi, kodi zimenezi sizingasonyeze kuti nthawi zina Mdyerekezi amachita zofuna za Mulungu?
A Benard: Ndinali ndisanaiganizirepo mfundo imeneyi.
A Patrick: Kuti mumvetse mfundo imeneyi, paja muli ndi ana, eti?
A Benard: Ndili ndi mnyamata yemwe wangokwanitsa kumene zaka 15.
A Patrick: Tiyerekezere kuti mwana wanuyo sakukumverani ndipo wayamba kuchita zinthu zoipa zomwe zimakukhumudwitsani kwambiri. Kodi mungatani?
A Benard: Ndingamulangize kuti asiye khalidwe loipalo.
A Patrick: Ndikudziwa kuti ndi zimenedi mungachite. Mungayesetse kumuthandiza kuti asinthe.
A Benard: Ndithudi ndingachite zimenezi.
A Patrick: Ndiyeno tiyerekeze kuti mwachita zonse zomuthandiza kuti asinthe, koma iye akukana malangizo anu. Kenako mukuona kuti simungachitirenso mwina koma kumulanga.
A Benard: Angafunikedi chilango mwana wotereyu.
A Patrick: Ndiye kodi mungatani mutamva kuti munthu wina ndi amene akuphunzitsa mwana wanuyo kuchita zoipa?
A Benard: Ndingakwiye kwambiri.
A Patrick: Ndiye tandiuzani, popeza mwadziwa kuti munthu wina woipa ndi amene akuchititsa kuti mwana wanu asamakumvereni, kodi mungauze munthu yemweyo kuti akulangireni mwana wanuyo?
A Benard: Sindingachite zimenezo chifukwa sizingathandize kuti mwanayo asinthe.
A Patrick: Ndiye kodi mukuona kuti n’zomveka kunena kuti Mulungu angauze Satana Mdyerekezi, yemwe amachititsa anthu kuchita zoipa, kuti alange anthuwo?
A Benard: Ndikuona kuti sangachite zimenezo.
A Patrick: Komanso ngati Mulungu amafuna kuti anthu oipa alangidwe, kodi mukuganiza kuti Mdyerekezi, yemwe ndi mdani wamkulu wa Mulungu, angachite zofuna za Mulungu polanga anthuwo?
A Benard: Zimenezinso ndinali ndisanaziganizirepo.
Yehova Adzathetsa Zoipa Zonse
A Patrick: Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti Mulungu sadzalanga anthu ochita zoipa. Muyenera kudziwa kuti Mulungu adzawononga anthu onse oipa amene sakufuna kusintha. Mwina tiwerenge lemba lomaliza limene likutsindika mfundo imeneyi. Lemba lake ndi la Salimo 37:9. Kodi mungawerenge lembali?
A Benard: Ndikhoza kuwerenga. Likuti: “Ochita zoipa adzaphedwa. Koma oyembekezera Yehova ndi amene adzalandire dziko lapansi.”
A Patrick: Zikomo kwambiri. Kodi lembali likuti Yehova Mulungu adzawatani ochita zoipa?
A Benard: Likuti, adzawapha.
A Patrick: Mwayankha bwino. Lembali likutanthauza kuti Mulungu adzawapha anthu amenewa ndipo sadzakhalakonso. Koma anthu ochita zabwino, kapena kuti “oyembekezera Yehova,” adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Komabe mwina zimenezi zingapangitse kuti mukhale ndi mafunso ena. Mwachitsanzo, kodi n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azichita zoipa? Komanso ngati iye wakonzadi zodzalanga anthu oipa, n’chifukwa chiyani sanawalangebe mpaka pano?
A Benard: Ndi mafunso abwinodi amenewa.
A Patrick: Ndikadzabweranso, tidzakambirana mayankho a m’Baibulo a mafunso amenewa. *
A Benard: Mudzabweredi, ndikufuna kudziwa mayankho a mafunso amenewa.
^ ndime 35 Onani Aroma 5:12.
^ ndime 79 Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 11 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.