Kodi Mungatani Kuti Mudzakhale Ndi Tsogolo Labwino?
Kodi Mungatani Kuti Mudzakhale Ndi Tsogolo Labwino?
KODI mungatani kuti mudzakhale ndi moyo wabwino? Njira imodzi imene mungachitire zimenezi ndi kuganizira zimene zidzakhale zotsatira za zosankha zimene mukupanga panopa.
Ndi zoona kuti nthawi zina zingakuvuteni kuti mupange zosankha zimene zingakupindulitseni pa moyo wanu mpaka kalekale. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa anthu ambiri amafuna kuti apeze nthawi yomweyo zinthu zimene amazilakalaka. Mwachitsanzo, mwina mukudziwa kuti kutsatira malangizo a m’Baibulo kungakuthandizeni kuti mukhale ndi banja labwino. (Aefeso 5:22–33; 6:1–4) Koma kuti zimenezi zitheke, muyenera kupewa kuthera nthawi yambiri mukugwira ntchito kapena kuchita zosangalatsa. M’malomwake, muyenera kumapeza nthawi kawirikawiri yochita zinthu ndi banja lanu. Nthawi zambiri mumafunika kusankha pakati pa kuchita zinthu zoti zikuthandizeni kupeza zimene mukufuna nthawi yomweyo, kapena kuchita zinthu zoti zidzakupindulitseni kwambiri m’tsogolo. Kodi mungatani kuti muzitha kusankha zinthu mwanzeru? Muzitsatira mfundo zinayi zili m’munsizi.
1. Ganizirani Zotsatira za Zosankha Zanu
Mukamasankha zochita muyenera kuganizira mofatsa phindu la zosankhazo komanso mavuto amene angakhalepo. Baibulo limatilangiza kuti: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Ngati mungaganizire bwinobwino zotsatira za zimene mungasankhe, mungathe kupewa kusankha zinthu zimene zikuoneka kuti zotsatira zake zidzakhala zoipa. Komanso kuganizira mmene zosankha zabwino zingakupindulitsireni, kungakulimbikitseni kupanga zosankha zanzeru.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi zotsatira za zimene ndasankhazi zidzakhala zotani pambuyo pa chaka chimodzi, zaka10 kapena zaka 20? Kodi zimenezi zidzakhudza bwanji maganizo ndiponso thanzi langa? Kodi zimene ndasankhazi zikhudza bwanji banja langa komanso anthu amene ndimawakonda?’ Koposa zonse, dzifunseni kuti: ‘Kodi zimene ndasankhazi n’zosangalatsa Mulungu? Nanga zikhudza bwanji ubwenzi wanga ndi iye?’ Popeza kuti Baibulo linauziridwa ndi Mulungu, lingakuthandizeni kudziwa zinthu zimene iye amakondwera nazo komanso lingakuthandizeni kudziwa zinthu zimene muyenera kuzipewa.—Miyambo 14:12; 2 Timoteyo 3:16.
2. Musamangotengera Zimene Ena Asankha
Anthu ambiri sakonda kusankha zinthu paokha, m’malomwake amangotengera zimene anthu ena akuchita. Koma anthu ambiri akamachita zinthu zinazake si umboni wakuti zinthuzo ndi zaphindu. Choncho, muyenera kusankha nokha zoyenera kuchita, osati kungotengera zimene ena asankha. Mwachitsanzo, mtsikana wina, dzina lake Natalie, * ananena kuti: “Ndinkafuna kudzakhala ndi banja labwino koma ndinkaona kuti zimenezi n’zosatheka chifukwa cha zochita zanga. Ndili ku koleji, ndinali ndi anzanga anzeru okhaokha. Komabe, nthawi zambiri zosankha zimene ankapanga pa moyo wawo sizinkakhala zabwino. Iwo ankangosinthasintha zibwenzi ndipo nanenso ndinali ndi zibwenzi zambiri. Zimene ndinkachitazi zinkandibweretsera mavuto ambiri.”
Natalie anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Iye ananena kuti: “Ndinkaona kuti m’gulu la Mboni za Yehova muli achinyamata osangalala komanso mabanja olimba. M’kupita kwa nthawi ndinasintha mfundo zimene ndinkayendera komanso moyo wanga ngakhale kuti kuchita zimenezi kunali kovuta kwambiri.” Kodi zotsatira zake zinali zotani? Natalie anati: “Ndinkafunitsitsa kudzakwatirana ndi munthu wakhalidwe labwino. Patapita nthawi ndinakwatirana ndi mnyamata amene ankakhulupirira
zofanana ndi zimene ineyo ndimakhulupirira. Ndikuona kuti Mulungu wandipatsa banja labwino kwambiri lomwe sindinkaganiza kuti ndingakhale nalo.”3. Ganizirani Mmene Zosankha Zanuzo Zidzakhudzire Moyo Wanu M’tsogolo
Kuti muzitha kupewa kusankha zinthu pongoganizira zalero, muyenera kuganizira za tsogolo limene mukufuna kudzakhala nalo komanso kukhala ndi pulani ya zimene mungachite kuti mudzakhaledi ndi tsogolo loterolo. (Miyambo 21:5) Musamangoganizira za tsogolo lanu la zaka 70 kapena 80 poganiza kuti zaka zimenezi n’zimene kawirikawiri munthu amakhala ndi moyo. M’malomwake muziganizira mmene mungasangalalire mutakhala ndi moyo wosatha ngati mmene Baibulo limanenera.
Baibulo limanena kuti kudzera mu nsembe ya dipo ya Khristu Yesu, Mulungu anapereka mwayi woti anthu adzakhale ndi moyo wosatha. (Mateyu 20:28; Aroma 6:23) Mulungu akulonjeza kuti posachedwapa cholinga chake chokhudza anthu ndi dziko lapansi chikwaniritsidwa. Anthu amene amakonda Mulungu adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha m’dziko lapansi lokongola ngati mmene linalili poyamba. (Salimo 37:11; Chivumbulutso 21:3-5) Inunso mungathe kudzakhalapo pa nthawiyo ngati panopa mumasankha zinthu zimene zingakuthandizeni kudzakhala ndi tsogolo labwino.
4. Yesetsani Kukwaniritsa Zolinga Zanu
Kodi mungatani kuti mudzakhale m’dziko lapansi limene Mulungu walonjeza? Choyamba, muyenera kuphunzira za Mulungu. (Yohane 17:3) Kudziwa zoona zimene Baibulo limanena kungakuthandizeni kukhala ndi chikhulupiriro chakuti zimene Mulungu analonjeza zidzachitikadi. Chikhulupiriro chimenechi n’chimene chingakuthandizeni kusintha moyo wanu kuti muzichita zimene Mulungu amakondwera nazo.
Taganizirani chitsanzo cha mnyamata wina, dzina lake Michael. Iye anati: “Ndili ndi zaka 12 ndinayamba kumwa mowa kwambiri komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ndinalowa m’gulu la zigawenga ndipo ndinkaganiza kuti ndikhoza kufa ndisanakwanitse zaka 30. Ndinkakhala wokwiya komanso ndinkaona kuti zinthu sizikundiyendera. Zimenezi zinapangitsa kuti maulendo angapo ndifune kudzipha. Ndinkalakalaka nditakhala ndi moyo wosangalala koma sizinkatheka.” Michael adakali pa sukulu, mnzake wina amenenso anali m’gulu la zigawenga lija, anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Nayenso Michael anavomera kuyamba kuphunzira Baibulo.
Zimene Michael anaphunzira m’Baibulo zinamuchititsa kusintha mmene ankaonera tsogolo lake. Iye anati: “Ndinaphunzira kuti dziko lapansi lidzakhalanso paradaiso ndipo anthu adzakhala mwamtendere komanso opanda nkhawa. Ndinayamba kulakalaka nditadzakhala ndi moyo pa nthawi imeneyo. Ndinali ndi cholinga chokhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, koma nthawi zina ndinkalephera kuchita zinthu zokondweretsa Yehova. Mwachitsanzo, ndinaledzerapo kangapo konse nditayamba kale kuphunzira Baibulo. Komanso nthawi ina ndinagonapo ndi mtsikana.”
Kodi n’chiyani chinamuthandiza Michael kuthana ndi zinthu zimene zinkamulepheretsa kupita patsogolo mwauzimu komanso kusintha khalidwe lake? Iye anati: “Munthu amene ankandiphunzitsa Baibulo anandilimbikitsa kuti ndiziwerenga Baibulo tsiku lililonse komanso ndizicheza ndi anthu amene amafuna kukondweretsa Mulungu. Ndinazindikira kuti anzanga a m’gulu la zigawenga lija ankachititsa kuti ndizichitabe zinthu zoipa. Ngakhale kuti anthu amenewa ndinkawatenga ngati abale anga, ndinasiya kucheza nawo.”
Michael anadziikira zolinga zing’onozing’ono zimene zinamuthandiza kuti akwaniritse cholinga chake chachikulu choti akhale ndi moyo wogwirizana ndi mfundo za Mulungu. Nanunso mungachite chimodzimodzi. Lembani cholinga chachikulu chimene mukufuna kukwaniritsa komanso zolinga zing’onozing’ono zimene zingakuthandizeni kukwaniritsa cholinga chachikulucho. Muzikambirana zolinga zimene muli nazo ndi anthu amene angakuthandizeni kuti mukwaniritse zolinga zanuzo ndiponso muziwapempha kuti azikuthandizani kuona ngati mukuyesetsa kuzikwaniritsa.
Yambani panopo kuphunzira za Mulungu ndiponso kutsatira malamulo ake. Muzichita zinthu zimene zingakuthandizeni kuti muzikonda Mulungu komanso Mawu ake, Baibulo. Ponena za munthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo, Mawu a Mulungu amati: “Zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.”—Salimo 1:1-3.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Tasintha mayina a m’nkhaniyi.