Yandikirani Mulungu
“Ine Sindidzakuiwala”
KODI Yehova amakondadi anthu ake? Ngati amawakonda, kodi chikondi chakecho n’chachikulu bwanji? Tingadziwe mayankho a mafunso amenewa kuchokera m’zimene Mulungu mwiniwakeyo ananena. Nkhani zopezeka m’Baibulo zimatithandiza kudziwa mmene Yehova amakondera anthu. Tiyeni tikambirane mawu a pa Yesaya 49:15.
Pofuna kutithandiza kudziwa mmene amakondera anthu ake, Yehova anauzira Yesaya kuti alembe chitsanzo chogwira mtima kwambiri. Iye anayamba ndi kufunsa funso lofunika kuliganizira bwino ili: “Kodi mayi angaiwale mwana wake woyamwa, osamvera chisoni mwana wochokera m’mimba mwake?” Kupanda kuliganizira bwino funso limeneli, yankho lake lingaoneke ngati lodziwikiratu chifukwa n’zosatheka kuti mayi aiwale mwana wake woyamwa. Mwana amadalira mayi ake pa chilichonse ndipo amalira akafuna kuti mayi akewo amusamalire. Komatu tingaphunzire zambiri pa funso la Yehova limeneli.
Kodi mayi amasamalira mwana wake chifukwa chiyani? Kodi iye amangochita zimenezi n’cholinga choti mwanayo asalire? Ayi. Mwachibadwa, mayi amakhala ndi “chisoni” pa “mwana wochokera m’mimba mwake.” Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “chisoni” amatanthauzanso “kusonyeza chifundo.” (Ekisodo 33:19; Yesaya 54:10) Mawu achiheberiwo angatanthauzenso kuchitira chifundo munthu amene alibe womuthandiza. Chikondi cha mayi pa mwana wake woyamwa chimakhala champhamvu kwambiri kuposa chikondi chamtundu wina uliwonse.
Koma chomvetsa chisoni n’chakuti si azimayi onse amene amamvera chisoni mwana wawo wamng’ono pa nthawi imene mwanayo amadalira iwowo pa chilichonse. Yehova ananena kuti “amayi amenewa akhoza kuiwala” mwana wawo. M’dzikoli, amuna ndi akazi ambiri ndi “osakhulupirika [komanso] osakonda achibale awo.” (2 Timoteyo 3:1-5) Nthawi zambiri timamva nkhani zonena za azimayi amene sasamala ana awo komanso za azimayi amene amazunza kapena kutaya ana awo ongobadwa kumene. Pothirira ndemanga mawu a palemba la Yesaya 49:15, buku lina lofotokoza Baibulo linanena kuti: “Chifukwa chakuti anthu onse ndi ochimwa, nthawi zina azimayi akhoza kukhala opanda chikondi chifukwa cha makhalidwe awo oipa. Zimenezi zikusonyeza kuti nthawi zina chikondi cha mayi chikhoza kutha.”
Koma Yehova akutitsimikizira kuti: “Koma ine sindidzakuiwala.” Tsopano tikuona chifukwa chake Yehova anafunsa funso limene lili pa Yesaya 49:15 lija. Palembali Yehova sakudziyerekezera ndi mayi, koma akunena za kusiyana kwa chikondi chake ndi chikondi cha mayi. Mosiyana ndi amayi opanda ungwiro amene nthawi zina amalephera kumvera chisoni mwana wawo, Yehova salephera kapena kuiwala kusonyeza chikondi kwa atumiki ake. Chifukwa cha zimenezi, buku limene talitchula lija linanenanso za mawu a pa Yesaya 49:15 kuti: “M’chipangano Chakale chonse, tingati lembali ndi limene limafotokoza bwino kwambiri za chikondi chachikulu chimene Mulungu ali nacho pa anthu.”
Kodi sizolimbikitsa kudziwa za “chifundo chachikulu cha Mulungu wathu” chimenechi? (Luka 1:78) Tikukulimbikitsani kuphunzira zimene mungachite kuti muyandikire Yehova. Mulungu wachikondi ameneyu akutsimikizira anthu amene amamulambira kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”—Aheberi 13:5.
Mavesi amene mungawerenge mu February: