Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

KODI n’chiyani chinachititsa munthu wina kuti asiye ntchito yolima fodya komanso kuti asinthe chipembedzo chake chomwe ankachikonda kwambiri? Nanga n’chiyani chinathandiza mayi wina yemwe ankamwa mowa mwauchidakwa kuti asinthe moyo wake? Werengani nkhanizi kuti mumve zimene anthu amenewa ananena.

“Ndikusangalala kukhala m’banja lalikulu kwambiri limeneli.”​—DINO ALI

CHAKA CHOBADWA: 1949

DZIKO: AUSTRALIA

POYAMBA: NDINKALIMA FODYA

KALE LANGA: Makolo anga anasamuka ku Albania m’chaka cha 1939 ndipo anakakhala m’tauni yaing’ono ya Mareeba, mumzinda wa Queensland, m’dziko la Australia. Anthu ochokera ku Bosnia, ku Greece, ku Italy, ku Serbia ndi m’madera ena, anasamukiranso m’tauniyi. Zimenezi zinachititsa kuti m’derali muzipezeka anthu a miyambo ndi zikhalidwe zosiyanasiyana. Anthu ambiri a m’tauni ya Mareeba ankalima fodya ndipo nawonso makolo anga anayamba ulimi umenewu.

Mchemwali wanga anabadwa makolo anga atangosamukira kumene m’derali. Kenako kunabadwa achimwene anga awiri ndiponso ineyo. Koma ndili ndi chaka chimodzi, bambo anga anamwalira ndi matenda amtima. Kenako mayi anga anakwatiwanso ndipo anabereka ana ena anayi aamuna. Tonse tinkakhala pafamu ya bambo athu otipezawa.

Ndisanakwanitse zaka 20, ndinasiya kukhala ndi makolo anga. Nditangopitirira zaka 20, ndinakwatira Saime, ndipo ukwati wathu unachitikira mumzikiti wa m’derali popeza tonse tinali Asilamu. Abale anga onse analinso Asilamu. Ndinkakonda kuwerenga Korani komanso buku lina lonena za mbiri ya mneneri Muhammad. Pa nthawi imeneyi ndinkawerenganso Baibulo linalake laling’ono. Korani imanena za aneneri omwenso amatchulidwa m’Baibulo choncho kuwerenga Baibulo kunandithandiza kudziwa nthawi imene aneneri amenewa anakhalapo.

A Mboni za Yehova ankabwera pakhomo pathu ndipo nthawi zambiri ankatisiyira magazini ndi mabuku amene ine ndi Saime tinkakonda kuwerenga. Ndikukumbukira kuti ndinkakambirana nawo nkhani zambiri zosangalatsa zachipembedzo ndipo nthawi zonse iwo ankagwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunso anga m’malo mongofotokoza maganizo awo. Zimenezi zinandichititsa chidwi kwambiri.

A Mboni anandipempha kuti ndiziphunzira nawo Baibulo komanso ankandiitanira ku misonkhano yawo koma nthawi zonse ndinkakana. Chomwe ndinkafunitsitsa pa nthawiyo ndi kukhala ndi famu yangayanga komanso kukhala ndi ana ambiri. Ngakhale kuti sindinakhale ndi famu yangayanga ngati mmene ndinkafunira, ndine wosangalala kuti ndili ndi ana asanu.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Ngakhale kuti panali patatha zaka 9 kuchokera pamene ndinakumana koyamba ndi a Mboni za Yehova, ndinkapitabe kuchipembedzo changa. Koma ndinkasangalalabe kulandira ndi kuwerenga mabuku a Mboni za Yehova. Lamlungu lililonse, ine ndi Saime tinkayesetsa kupeza nthawi yowerenga mabukuwa ndipo tinkasunga magazini onse amene a Mboni ankatipatsa. Magazini amenewa anali ndi mfundo zimene zinkandithandiza kwambiri anthu akamatsutsa zimene ndinayamba kukhulupirira.

Mwachitsanzo, nthawi ina ndinakumana ndi munthu wina wa Evanjeliko yemwe ankandikakamiza kuti ndilandire Yesu monga Mpulumutsi wanga. Iye anali atakwanitsa kukopa mchimwene wa Saime komanso mchimwene wanga wina. Kenako anthu ochokera m’zipembedzo zosiyanasiyana anayamba kundikopa kuti ndilowe m’zipembedzo zawo. Ena ankandipatsa mabuku otsutsa zimene a Mboni za Yehova amaphunzitsa. Ndinawauza anthu amenewa kuti andisonyeze m’Baibulo umboni wa zimene amakhulupirira koma analephera kutero.

Zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe kufufuza zinthu zambiri m’Baibulo pogwiritsa ntchito mabuku amene a Mboni anandipatsa. Nthawi imeneyi ndinaona kuti m’pofunika kuti ndiyambe kutsatira zimene ndinkaphunzira.

Pa nthawiyi n’kuti ndisakuphunzira Baibulo ndi wa Mboni aliyense, koma ndinangoyamba kupita ku misonkhano yawo. Poyamba, ndinkachita manyazi komanso mantha ndikapita ku misonkhanoyi. Komabe ku misonkhanoyi ndinkakumana ndi anthu ambiri ochezeka komanso ndinkasangalala ndi zimene ndinkaphunzira. Ndinaona kuti ndiyenera kukhala wa Mboni za Yehova choncho mu 1981 ndinabatizidwa posonyeza kudzipereka kwa Mulungu.

Mkazi wanga sanatsutse zimene ndinasankhazi ngakhale kuti nthawi zina ankaganiza kuti ndasocheretsedwa. Komabe iye anabwera kudzaonerera ubatizo wanga. Ndinapitiriza kumufotokozera mfundo za m’Baibulo zimene ndinkaphunzira. Tsiku lina tikuchokera ku holide, ndinasangalala kwambiri Saime atandiuza kuti nayenso akufuna kukhala wa Mboni. Pa nthawiyi n’kuti patadutsa pafupifupi chaka chimodzi kuchokera pamene ineyo ndinabatizidwa ndipo iye anabatizidwa mu 1982.

Tinafunika kusintha zina ndi zina pa moyo wathu koma kuchita zimenezi sikunali kophweka. Ndinasiya ntchito yanga yolima fodya chifukwa ndinazindikira kuti ndi yosagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. (2 Akorinto 7:1; Yakobo 2:8) Panatenga nthawi yaitali kuti tipeze ntchito yabwino komanso yodalirika. Izi zinachititsanso kuti kwa nthawi yaitali abale athu ena asiye kutiyendera. Komabe tinkayesetsa kuwachitirabe zabwino komanso kuwakonda mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Koma m’kupita kwa nthawi zinthu zinasintha ndipo panopa abale athu anasiya kutisala.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Pa moyo wanga ndakumana ndi mavuto ngati kutsutsidwa ndi abale anga, mavuto azachuma komanso kuchita manyazi. Izi zandiphunzitsa kuti Yehova Mulungu ndi woleza mtima chifukwa anandithandiza kuthana ndi mavuto amenewa. Mwachitsanzo, panopa ndine mkulu mu mpingo ndipo zimenezi zimachititsa kuti ndiziima kutsogolo kawirikawiri. Koma kuchita zimenezi kumandivutabe chifukwa ndikakhala ndi mantha ndimachita chibwibwi. Komabe, nthawi zonse ndimapemphera kwa Yehova kuti andithandize ndipo chifukwa cha zimenezi ndimatha kuchita utumiki umenewu bwinobwino.

Panopa ine ndi mkazi wanga timakondana kwambiri. Ngakhale kuti tinkalakwitsa zinthu zina polera ana athu, tinayesetsabe kuwaphunzitsa choonadi cha m’Baibulo chimene tinaphunzira. (Deuteronomo 6:6-9) Panopa mwana wanga wamwamuna akutumikira monga mmishonale limodzi ndi mkazi wake.

Ndikukumbukira zimene ndinachita tsiku lina titangoyamba kumene kupita ku misonkhano ya Mboni monga banja. Nditaimika galimoto n’kuona gulu la anthu amene anali m’Nyumba ya Ufumu, ndinafunsa mkazi ndi ana anga kuti: “Kodi mwawaona anthu amene ali mkatimu?” Mu Nyumba ya Ufumuyo munali anthu a zikhalidwe komanso zinenero zosiyanasiyana. Munali anthu a ku Albania, Croatia, Australia komanso anthu amene anayambirira kukhala m’dzikolo. Anthu onsewa ankachita zinthu mogwirizana. Ndikusangalala kukhala m’banja lalikulu kwambiri la abale ndi alongo auzimu amenewa. Banja limeneli lili padziko lonse, osati ku Australia kokha.​—1 Petulo 5:9.

“Mchemwali wanga sanataye mtima.”​—YELENA VLADIMIROVNA SYOMINA

CHAKA CHOBADWA: 1952

DZIKO: RUSSIA

POYAMBA: NDINALI CHIDAKWA KOMANSO NTHAWI INA NDINKAFUNA KUDZIPHA

KALE LANGA: Ndinabadwira mumzinda waung’ono, wotchedwa Krasnogorsk, womwe uli pafupi ndi mzinda wa Moscow. Makolo anga anali aphunzitsi. Ndinkakhoza bwino m’kalasi ndipo ndinachita maphunziro a zoimba moti ndinkaona kuti ndili ndi tsogolo labwino.

Nditakwatiwa, ine ndi mwamuna wanga tinasamukira kudera lina kumene anthu ambiri ankakonda kutukwana, kuledzera komanso kusuta. Sindinkadziwa kuti m’kupita kwa nthawi nanenso ndiyamba kuchita zimene anthu amenewa ankachita. Poyamba, ndinkapita kumaphwando kuti ndikangoimbako nyimbo ndiponso gitala. Koma kumeneko anthu ankandinyengerera kuti ndizisuta fodya komanso kumwa nawo mowa. Zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe kumwa mwauchidakwa.

Kumwa mowa mwauchidakwa kunayamba kusokoneza kwambiri moyo wanga. Zinkanditengera nthawi yaitali kuti ndiledzere koma ndikaledzera, ndinkakanika ndi kudya komwe. Sindinkasangalala ndi moyo moti ndinkangolakalaka nditafa. Pa nthawi ina ndinayesapo kudzipha koma zinakanika. Panopa ndimaona kuti zinakhala bwino kuti sindinafe.

Pa nthawi yonse imene zimenezi zinkachitika, mchemwali wanga ankabwera pafupipafupi kudzandiona. Iye anali atakhala wa Mboni za Yehova ndipo ankayesetsa kundifotokozera mmene Baibulo lingandithandizire. Koma sindinkakonda chilichonse chokhudza Baibulo choncho ndinamuuza kuti asiye zobwera kunyumba kwanga. Koma mchemwali wanga sanataye mtima. Iye anali woleza mtima komanso wachikondi moti pamapeto pake ndinavomera kuti azindiphunzitsa Baibulo.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Nditayamba kuphunzira Baibulo, ndinatsimikiza zosiya kumwa mowa. Pasanapite nthawi, bambo wina woyandikana naye nyumba yemwe anali ataledzera anandimenya. Bamboyu anandivulaza kwambiri moti ndinagonekedwa m’chipatala. Anandithyola nthiti zinayi komanso anandivulaza diso. Komabe, kukhala m’chipatalaku kunandithandiza kuti ndizolowere kukhala osamwa mowa.

Pa nthawi imene ndinali m’chipatalayi, ndinkapemphera pafupipafupi. Lemba la m’Baibulo limene linkandilimbikitsa kwambiri linali la Maliro 3:55, 56, lomwe limati: “Inu Yehova, ndaitana dzina lanu mofuula ndili m’dzenje lakuya kwambiri. Mumve mawu anga. Musatseke khutu lanu pamene ndikupempha mpumulo ndiponso pamene ndikulirira thandizo.”

Ndimaona kuti Yehova anayankha mapemphero anga. Iye anandithandiza kuti ndisayambirenso moyo wanga wakale. Nthawi zina maganizo olakwika oti ndiyambirenso kumwa mowa ankandibwerera. Koma ndine wosangalala kuti sindinagonjere mayesero amenewa.

Kuphunzira Baibulo kunandithandiza kuzindikira kuti ndinafunika kugonjera mwamuna wanga monga mutu wa banja. (1 Petulo 3:1, 2) Zimenezi zinali zovuta chifukwa ndinkakonda kumulamulira. Choncho ndinapemphera kuti Yehova andithandize. Zinatenga nthawi yaitali kuti ndisinthe komabe m’kupita kwa nthawi ndinayamba kugonjera mwamuna wanga.

Mwamuna wanga anadabwa kwambiri ndi kusintha kumeneku. Nthawi imeneyo sankakonda zinthu zokhudza Baibulo. Koma nditamuuza kuti ndikufuna kusiya kusuta fodya, iye anati: “Ngati usiye kusuta fodya, inenso ndiyamba kuphunzira Baibulo.” Tonse tinasiya kusuta fodya tsiku limodzi.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Mwamuna wanga anayambadi kuphunzira Baibulo monga analonjezera. Panopa timawerengera limodzi Baibulo tsiku lililonse, kusinkhasinkha zimene tawerenga komanso kuyesetsa kuzigwiritsa ntchito pa moyo wathu.

Panopa banja lathu likuyenda bwino kwambiri komanso ndikuona kuti kuphunzira Baibulo kwandithandiza ineyo pandekha. Ndikuyamikira kwambiri Yehova chifukwa chondikokera kwa iye. (Yohane 6:44) Ndikuyamikiranso mchemwali wanga amene anachita khama kundithandiza. Zimenezi zachititsa kuti nditsimikize zoti Baibulo limasinthadi anthu.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Ndinaona kuti m’pofunika kuti ndiyambe kutsatira zimene ndinkaphunzira

[Mawu Otsindika patsamba 13]

Mchemwali wanga anali woleza mtima komanso wachikondi moti pamapeto pake ndinavomera kuti azindiphunzitsa Baibulo