Kodi Tingapeze Bwanji Anzathu Abwino?
Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena
Kodi Tingapeze Bwanji Anzathu Abwino?
Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kusankha anzathu mosamala?
Anthu ambiri amafuna kuti azikondedwa ndi ena. Kawirikawiri mtima umenewu umatichititsa kuti tizitengera zochita za ena. Choncho timatengera kwa anzathu makhalidwe osiyanasiyana, amene amayambira mumtima. Zimenezi zikusonyeza kuti anthu amene tingasankhe kuti akhale anzathu angatichititse kuti tikhale ndi makhalidwe enaake.—Werengani Miyambo 4:23; 13:20.
Davide, yemwe analemba nawo Baibulo, ankasankha mwanzeru anthu ocheza nawo. Iye ankacheza ndi anthu amene anamuthandiza kuti azitumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika. (Salimo 26:4, 5, 11, 12) Mwachitsanzo, Davide ankasangalala kucheza ndi Yonatani chifukwa ankamulimbikitsa kuti azikhulupirira Yehova.—Werengani 1 Samueli 23:16-18.
2. Kodi mungatani kuti mukhale bwenzi la Mulungu?
Ngakhale kuti Yehova ndi wamphamvuyonse, n’zotheka kukhala naye pa ubwenzi. Mwachitsanzo, Abulahamu ankamvera ndi kukhulupirira Yehova, moti Yehovayo anayamba kuona Abulahamu kuti ndi bwenzi lake. (Genesis 22:2, 9-12; Yakobo 2:21-23) Nafenso tingakhale pa ubwenzi ndi Yehova ngati timamukhulupirira ndi kuchita zimene iye amatiuza kuti tizichita.—Werengani Salimo 15:1, 2.
3. Kodi anzanu abwino angakuthandizeni bwanji?
Anthu omwe ndi anzanu enieni amakhala okhulupirika ndipo amakuthandizani kuti muzichita zinthu zabwino. (Miyambo 17:17; 18:24) Mwachitsanzo, mwina Yonatani anali wamkulu zaka 30 kuposa Davide, ndipo anayenera kudzatenga ufumu wa Isiraeli kuchokera kwa bambo ake. Ngakhale zinali choncho, Yonatani anathandiza Davide mokhulupirika popeza anazindikira kuti Davideyo wasankhidwa ndi Mulungu kuti adzakhale mfumu. Komanso anzanu enieni amalimba mtima n’kukuuzani kuti musinthe ngati aona kuti mwayamba kuchita zinthu zina zoipa. (Salimo 141:5) Choncho ngati anzanu amene mumacheza nawo amakonda Mulungu, angakuthandizeni kuti nanunso mukhale ndi makhalidwe abwino.—Werengani 1 Akorinto 15:33.
Mungapeze anthu omwe amakonda zabwino ngati amenewo, ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Kumalo amenewa mudzapeza anzanu omwe angakulimbikitseni pamene mukuyesetsa kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu.—Werengani Aheberi 10:24, 25.
Komabe, nthawi zina anzathu, ngakhale omwe amakonda Mulungu, angatikhumudwitse. Zikatero, musafulumire kukwiya. (Mlaliki 7:9, 20-22) Musaiwale kuti palibe munthu wangwiro, komanso anzathu omwe amakonda Mulungu ndi amtengo wapatali. Ndipotu Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti tizinyalanyaza zofooka za Akhristu anzathu.—Werengani Akolose 3:13.
4. Kodi mungatani ngati anthu amene amati ndi anzanu ayamba kukutsutsani?
Anthu ambiri akayamba kuthandizidwa kuti amvetse Mawu a Mulungu, kawirikawiri anzawo ena amayamba kuwatsutsa. Mwina anzanuwo angachite zimenezi chifukwa sakumvetsa malangizo othandiza a m’Baibulo, kapenanso sakuzindikira kuti malonjezo a m’Baibulo amene inuyo mukuphunzira ndi odalirika. Ngakhale zili choncho, mwina mungathe kuwathandiza.—Werengani Akolose 4:6.
Nthawi zina anthu omwe amati ndi anzanu angayambe kunyoza uthenga wabwino wa m’Mawu a Mulungu. (2 Petulo 3:3, 4) Ena angamakunyozeni chifukwa choti mukuyesetsa kuchita zinthu zabwino. (1 Petulo 4:4) Zimenezi zikakuchitikirani mungafunike kusankha chinthu chimodzi, kaya kukhalabe pa ubwenzi ndi anthuwo kapena kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Ngati mungasankhe kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu, ndiye kuti mwasankha mnzanu wabwino kwambiri kuposa wina aliyense.—Werengani Yakobo 4:4, 8.
Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 12 ndi 19 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.