2 Mulungu Satidera Nkhawa—Kodi Zimenezi ndi Zoona?
2 Mulungu Satidera Nkhawa—Kodi Zimenezi ndi Zoona?
Mwina munamvapo izi: “Mulungu akanakhala kuti amakhudzidwa ndi zimene zimachitikira anthu, bwenzi atachotsa zoipa komanso mavuto onse amene ali padzikoli. Ndipo ngakhale atakhala kuti amakondadi anthu, sindikukhulupirira kuti amandikonda ineyo pandekha.”
Zimene Baibulo limaphunzitsa: Yehova Mulungu sachititsa zoipa. (Yakobo 1:13) Mulungu angathetse zoipazi nthawi ina iliyonse, koma iye walola anthu oipa kukhalapobe mpaka pano. Iye wachita zimenezi pofuna kuthetsa nkhani ina yofunika kwambiri yokhudza chabwino ndi choipa imene inayambika anthu atangolengedwa kumene. Mulungu adzathetsa zoipa zonse padzikoli ndipo adzakonza zonse zimene anthu okana ulamuliro wake awononga.—Genesis 3:1-6; Yesaya 65:17. *
Mulungu amadera nkhawa anthu onse, koma amaderanso nkhawa kwambiri munthu aliyense payekha. Lemba la Mateyu 10:29-31 limasonyeza kuti Mulungu amadziwa chilichonse chimene chimatichitikira, ngakhalenso zina zoti ifeyo sitidziwa. Lembali limati: “Kodi mpheta ziwiri si paja amazigulitsa kakhobidi kamodzi kochepa mphamvu? Komatu palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa. Ndipotu tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliwerenga. Choncho musachite mantha: Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.”
Kodi kudziwa zoona pa nkhaniyi kungakuthandizeni bwanji? Nthawi zambiri timapewa anthu omwe ndi ankhanza komanso sadera nkhawa za ena. Choncho n’zosadabwitsa kuti bodza lakuti Mulungu satidera nkhawa anthufe limachititsa anthu ambiri kuti asamakhale ndi chidwi choti amudziwe. Nthawi zina anthu amenewa amangopemphera kwa iye akaona kuti asowa pogwira. Koma kudziwa kuti Yehova Mulungu amadera nkhawa anthufe kungakuchititseni kuti mufune kudziwa zambiri za iyeyo komanso kuti mukhale naye pa ubwenzi wolimba.
Mwachitsanzo, mwina nthawi ina munapempherapo kwa Mulungu koma n’kumakayikira ngati Mulungu akumvetsera kapena ngati angayankhe pemphero lanu. Baibulo limatitsimikizira kuti nthawi zonse Yehova, yemwe ndi “Wakumva pemphero,” amamvetsera mapemphero a anthu amene amapemphera kwa iye ndi mtima wonse.—Salimo 65:2.
Yehova amafuna kuti ‘muzimutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’ (1 Petulo 5:7) Ngakhale pamene tili pa mavuto aakulu, tingakhale ndi chikhulupiriro choti amatidera nkhawa popeza Mawu ake amati: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—Salimo 34:18.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu walola kuti zoipa zizichitikabe, werengani mutu 11 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Ngati Mulungu satidera nkhawa, n’chifukwa chiyani amatiuza kuti tizipemphera kwa iye?