Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Okonda Mtendere Akuyesetsa Kuti Anthu Asaipitse Mbiri Yawo

Anthu Okonda Mtendere Akuyesetsa Kuti Anthu Asaipitse Mbiri Yawo

UTHENGA WOPITA KWA ANTHU A KU RUSSIA: Nkhani ino ithandiza kuti anthu mamiliyoni ambiri m’mayiko oposa 230 adziwe kuti dziko la Russia likuchita zinthu zankhanza zimene zikuphwanya ufulu wa anthu wolambira momasuka. Nkhaniyi idziwika padziko lonse chifukwa magazini a Nsanja ya Olonda amamasuliridwa ndiponso kufalitsidwa m’zinenero zambiri kuposa magazini ena onse padziko lapansi. Nkhani ino yamasuliridwa m’zinenero 188 ndipo magazini oposa 40 miliyoni afalitsidwa. Tikudziwa kuti akuluakulu ena aboma sasangalala kuti anthu m’mayiko ena adziwe zimene dziko la Russia likuchitira Mboni za Yehova. Koma asaiwale zimene Yesu ananena kuti: “Palibe chobisika chimene sichidzaululika, ndi chinsinsi chimene sichidzadziwika.”​—LUKA 12:2.

M’MWEZI wa December 2009 ndiponso wa January 2010, makhoti akuluakulu awiri a ku Russia ananena kuti a Mboni za Yehova apezeka kuti ndi anthu obweretsa chisokonezo. Komatu aka sikoyamba kuti zimenezi zichitike. Kale boma la Soviet Union likulamulira ku Russia, a Mboni za Yehova ambirimbiri anaimbidwa milandu yabodza yoti ndi oukira boma. Ambiri anathamangitsidwa m’dzikolo, ena anamangidwa ndipo ena ankawagwiritsa ntchito yakalavulagaga. Ulamuliro wankhanzawu utatha, anthuwa anamasulidwa ndipo boma latsopanolo linalengeza kuti milandu imene a Mboni ankaimbidwa inali yabodza. * Koma panopa, boma la Russia likufunanso kuipitsa mbiri ya Mboni za Yehova.

Kumayambiriro kwa chaka cha 2009, boma linakhazikitsa malamulo okhwima amene anachititsa kuti ufulu wolambira wa Mboni za Yehova uziponderezedwa. Mwachitsanzo, m’mwezi wa February wokha apolisi anafufuza milandu yokwana 500 yokhudza a Mboni za Yehova m’madera osiyanasiyana m’dzikolo. Iwo anachita zimenezi n’cholinga choti adziwe ngati a Mboniwo akuchita zinthu zophwanya malamulo. M’miyezi yotsatira, apolisi anasokoneza misonkhano ya Mboni za Yehova imene imachitika mwamtendere m’Nyumba za Ufumu ndiponso m’nyumba za anthu. Iwo ankalanda a Mboniwo mabuku ndiponso zinthu zawo zina. Boma linathamangitsanso m’dzikolo maloya amene ankaimira a Mboni za Yehova ndipo anawalamula kuti asadzalowenso m’dziko la Russia.

Pa October 5, 2009, akuluakulu oona za katundu wolowa ndi kutuluka m’dziko la Russia anagwira magalimoto onyamula mabuku a Mboni za Yehova. Akuluakuluwa anagwira magalimotowo kumalire a dzikoli, kufupi ndi mzinda wa St. Petersburg. Mabukuwa anasindikizidwa m’dziko la Germany ndipo anali oti atumizidwe m’mipingo ya Mboni za Yehova m’dziko la Russia. Magalimoto onyamula mabukuwo anafufuzidwa ndi gulu lapadera limene limaona za katundu woopsa wolowa kapena kutuluka m’dziko la Russia popanda chilolezo. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Chikalata chimene boma linatulutsa chinanena kuti magalimotowo ankawaganizira kuti “anyamula mabuku omwe cholinga chake chinali kuyambitsa chisokonezo pa nkhani zachipembedzo.”

Kenako nkhanza zoterezi zinafika poipa kwambiri. Makhoti Akuluakulu a ku Russia komanso a kudera la Altay Republic (lomwe ndi mbali ya Russia) anagamula kuti mabuku ena a Mboni za Yehova, kuphatikizapo magazini imene mukuwerengayi, cholinga chake n’kuyambitsa chisokonezo. A Mboni za Yehova anachita apilo ndipo mayiko ambiri anadzudzula boma la Russia, koma zonsezi sizinathandize ngakhale pang’ono. Akuluakulu aboma anakanitsitsa kusintha maganizo moti tikunena pano lamulo loletsa Mboni za Yehova kuitanitsa ndiponso kugawira mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo lidakalipobe m’dziko la Russia.

Kodi a Mboni za Yehova akanatani kuti mbiri yawo isapitirize kuipitsidwa komanso kuti apitirizebe kugwira ntchito yawo mwaufulu? Nanga zimene makhotiwa anagamula zikusonyeza chiyani pa nkhani ya ufulu wachipembedzo ku Russia?

Ntchito Yogawira Timapepala

Lachisanu pa February 26, 2010 a Mboni za Yehova okwana 160,000 m’dziko lonse la Russia anayamba kugawira kapepala kapadera ka mutu wakuti, Kodi Nkhanza Zikuyambiranso? Funso limene anthu a ku Russia Ayenera Kudzifunsa? (Could It Happen Again? A Question for the Citizens of Russia) Iwo anagawira timapepala tokwana 12 miliyoni. Mwachitsanzo, mmene nthawi inkakwana 5:30 m’mawa, n’kuti a Mboni za Yehova ambiri atasonkhana m’misewu mumzinda wa Usol’ye-Sibirskoye ku Siberia. Ena mwa anthu amenewa anali amene anathawira ku Siberia mu 1951 chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Iwo anadzipereka kugwira ntchitoyi ngakhale kuti kunja kunkazizira kwambiri moti mpaka madzi anaundana ndipo anagawira timapepala tawo tonse tokwana 20,000.

Pofuna kudziwitsa anthu za ntchito yapadera yogawira timapepalati, a Mboni za Yehova anapangitsa msonkhano wa atolankhani mumzinda wa Moscow, womwe ndi likulu la dziko la Russia. Ena mwa anthu amene anaitanidwa kuti adzalankhule pa msonkhanowu, anali a Lev Levison, omwe ndi katswiri wa bungwe lina loona za ufulu wa anthu. (Human Rights Institute) A Levinson anafotokoza mwachidule zinthu zopanda chilungamo ndiponso nkhanza zimene zinachitikira a Mboni za Yehova mu ulamuliro wa Nazi ku Germany komanso ku Soviet Union. Anafotokozanso kuti pamapeto pake akuluakulu aboma ananena kuti a Mboni za Yehova anali osalakwa. A Levinson ananenanso kuti: “Pulezidenti Yeltsin analamula kuti anthu onse amene anazunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo mu ulamuliro wa Soviet Union amasulidwe. Analamulanso kuti awabwezere katundu yense amene anawalanda. Koma popeza a Mboni za Yehova analibe katundu aliyense m’nthawi ya ulamuliro wa Soviet Union woti n’kuwabwezera, anangowabwezera mbiri yawo yabwino.”

Komabe panopa, anthu akufunanso kuwononga mbiri ya Mboni za Yehova ku Russia. A Levinson anapitiriza kunena kuti: “Koma dziko lomweli, limene linanena kuti a Mboni za Yehova ndi osalakwa, panopa likuzunzanso kwambiri anthuwa popanda zifukwa zomveka.”

Anthu Ambiri Anasangalala Ndi Kapepalaka

Kodi ntchito yapadera yogawira kapepala kameneka inakwaniritsa cholinga chake? A Levinson ananena kuti: “Pamene ndimabwera ku msonkhano kuno, ndaona anthu atakhala pamalo okwerera sitima akuwerenga kapepala kamene a Mboni za Yehova akugawira lero m’dziko lonse la Russia. . . . Anthu akuwerenga kapepalaka ndipo akuchita nako chidwi kwambiri.” * Taonani zitsanzo izi:

Mayi wina wachikulire amene amakhala m’chigawo chapakati m’dziko la Russia, kumene kuli Asilamu ambiri, atapatsidwa kapepalaka anafunsa cholinga cha kapepalako. Atauzidwa kuti kakunena za ufulu wobadwa nawo wa anthu a ku Russia, mayiyu ananena kuti: “Zakhala bwino kuti tsopano munthu wina waganiza zolankhulapo pa nkhani zimenezi. Chifukwatu dziko la Russia likungokhala ngati lili m’masiku a ulamuliro wa Soviet Union. Zikomo kwambiri chifukwa cha ntchito yabwino imene mukugwirayi. Chonde pitirizani.”

Pamene a Mboni ena mumzinda wa Chelyabinsk ankafuna kupatsa mayi wina kapepalaka, iye ananena kuti: “Ndalandira kale ndipo ndakawerenga. Ndikugwirizana ndi zimene mukuchitazi. Sindikudziwa ngati pali chipembedzo chinanso chimene chimaikira kumbuyo chikhulupiriro chawo mwadongosolo ngati inuyo. Anthu inu mumandisangalatsanso ndi mmene mumavalira ndipo mumachita zinthu mosamala kwambiri. Zikuchita kuonekeratu kuti simukayikira ngakhale pang’ono kuti zimene mumakhululupirira ndi zoona. Ndiponso ndimaona kuti Mulungu ali nanu.”

Mumzinda wa St. Petersburg bambo wina, yemwe anali atalandira kale kapepalaka, atafunsidwa ngati wasangalala ndi zimene wawerengazo, anayankha kuti: “Zandisangalatsa kwambiri. Pamene ndinayamba kuwerenga thupi langa linatuluka tsembwe chifukwa chokhudzidwa ndipo ndinagwetsa misozi. Agogo anga aakazi anazunzidwa [mu ulamuliro wa Soviet Union] ndipo anandiuzanso za anthu ena amene anali nawo m’ndende. Anandiuza kuti panali anthu ambiri amene anamangidwa chifukwa choswa malamulo, koma panalinso ena osalakwa amene anangomangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ndikuona kuti mukugwira ntchito yabwino chifukwa aliyense afunika adziwe zimene zinachitika.”

Sizikudziwika Kuti Zitha Bwanji ku Russia

A Mboni za Yehova ku Russia akuyamikira chifukwa cha ufulu womwe akhala nawo zaka 20 zapitazi. Komabe iwo akudziwa kuti ufulu umatha nthawi ina iliyonse. Sitikudziwa ngati zimene boma la Russia likuchitira Mboni za Yehova zikusonyeza kuti m’dzikoli zinthu zibwereranso ngati mmene zinalili mu ulamuliro wa Soviet Union. Tiona kutsogoloku zimene zichitike.

Koma a Mboni za Yehova atsimikiza mtima kuti zivute zitani, iwo apitirizabe kugwira ntchito yawo yolalikira uthenga wa m’Baibulo wonena za mtendere ndiponso zinthu zabwino zimene zikubwera kutsogoloku. Kapepala kapadera kamene agawiraka kakunena mwachidule maganizo a Mboni za Yehova pa nkhaniyi. Dziko la Russia lidziwe kuti: “Sitisiya ntchito yathu ngakhale titazunzidwa chotani. Sitileka kulalikira za Yehova Mulungu ndiponso zinthu zimene zili m’Mawu ake, Baibulo. Koma tizichita zimenezi mosamala komanso mwaulemu. (1 Petulo 3:15) Sitinasiye ntchito yathu pamene tinkazunzidwa mu ulamuliro wa chipani cha Nazi ku Germany, sitinasiye pamene tinkazunzidwa ndi ulamuliro wankhanza wa Soviet Union ndipo panopa sitisiyanso.​—Machitidwe 4:18-20.”

^ ndime 13 Patatsala maola ochepa kuti msonkhanowu uyambe, a Mboni za Yehova ku Moscow anali atayamba kale kugawira kapepalaka.