Yandikirani Mulungu
“Mudzalakalaka Ntchito ya Manja Anu”
ZIMAKHALA zopweteka kwambiri kuona wachibale wako kapena munthu amene umamukonda kwambiri akuvutika ndi matenda, kenako n’kumwalira. Mwachibadwa timamva chisoni kwambiri ndi zimenezi. Komabe n’zolimbikitsa kudziwa kuti Mlengi wathu Yehova Mulungu, amamvetsa mmene timamvera zimenezi zikachitika. Kuwonjezera pamenepo, iye amafunitsitsa kugwiritsa ntchito mphamvu zake zopanda malire kuukitsa anthu amene anamwalira. Mawu amene Yobu ananena opezeka palemba la Yobu 14:13-15 angakulimbikitseni.
Taganizirani zimene zinachititsa kuti Yobu alankhule mawu amenewa. Iye ankakhulupirira kwambiri Mulungu koma anakumana ndi mayesero aakulu. Chuma chake chinatha, ana ake onse anafa ndiponso iyeyo anadwala matenda owawa kwambiri. Atathedwa nzeru, iye anapemphera kwa Mulungu kuti: “Zikanakhala bwino mukanandibisa m’Manda.” (Vesi 13) Yobu ankaona kuti munthu akapita ku Manda ndiye kuti wasiyana ndi mavuto. Ankaona kuti ku Mandako akakhala ngati chuma chimene Mulungu wachibisa ndipo sakakhalanso ndi mavuto komanso sadzikamvanso ululu. *
Kodi ndiye kuti Yobu akanakhalabe ku Mandako mpaka kalekale? Yobu sanaganize choncho. Iye anapitiriza kupemphera kuti: “Zikanakhala bwino . . . mukanati mundiikire nthawi n’kudzandikumbukira.” Yobu ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti sadzakhala ku Mandako mpaka kalekale chifukwa Yehova adzamukumbukira. Iye anayerekezera nthawi imene adzakhale m’Manda ndi “ntchito yokakamiza,” kutanthauza kuti adzakakamizika kudikirira mpaka adzaukitsidwe. Koma kodi anafunika kudikira kwa nthawi yaitali bwanji? Iye anati: “Mpaka mpumulo wanga utafika.” (Vesi 14) Mpumulo umenewu ukutanthauza kuukitsidwa ku Manda.
Kodi n’chifukwa chiyani Yobu ankakhulupirira kuti adzaukadi? Chifukwa iye ankadziwa mmene Mlengi wathu wachikondi amamvera akaganiza za atumiki ake okhulupirika amene anamwalira. Yobu anati: “Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha. Mudzalakalaka ntchito ya manja anu.” (Vesi 15) Yobu ankadziwa kuti iyeyo anali ntchito ya manja a Mulungu. Mulungu ndi amene anatipatsa moyo ndipo ndi amenenso anachititsa kuti moyo wa Yobu uyambike m’mimba mwa mayi ake. Choncho Iye ndi amenenso adzaukitse Yobu.—Yobu 10:8, 9; 31:15.
Zimene Yobu ananena zikutiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri yokhudza Yehova. Mfundo yake ndi yakuti, iye amakonda kwambiri anthu amene amamudalira ngati mmene ankachitira Yobu. Anthu amenewa amalola kuti Yehova awaumbe kukhala anthu amakhalidwe amene Mulungu amasangalala nawo. (Yesaya 64:8) Yehova amaona kuti atumiki ake okhulupirika ndi anthu amtengo wapatali kwambiri. Choncho iye ‘amalakalaka’ kuonanso anthu okhulupirika amene anamwalira. Katswiri wina wa Baibulo ananena kuti, mawu achiheberi amene palembali anawamasulira kuti ‘kulakalaka,’ “ndi amodzi mwa mawu amphamvu amene amafotokoza mmene munthu amamvera akakhala kuti akufunitsitsa chinachake.” Sikuti Yehova amangokumbukira atumiki ake, koma amalakalakanso atawaukitsa kuti akhalenso ndi moyo.
Yehova anaona kuti n’zoyenera kwambiri kutchula cholinga chake chodzaukitsa anthu amene anamwalira. Ndipo tikuyamikira kwambiri kuti iye anatchula cholinga chakecho m’buku la Yobu, lomwe ndi limodzi mwa mabuku a m’Baibulo oyambirira kulembedwa. * Yehova akufuna kuti inuyo mudzaonanenso ndi abale anu kapena anzanu amene anamwalira. Mfundo imeneyi ingatithandize kuti tipirire chisoni chimene timakhala nacho munthu akamwalira. Choncho, tikukupemphani kuti muphunzire zambiri zokhudza Mulungu wachikondi ameneyu komanso za mmene angakuthandizireni kusintha makhalidwe anu kuti mukhale m’gulu la anthu amene adzaone iye akukwaniritsa cholinga chake.
Mavesi amene mungawerenge mu March:
^ ndime 2 Buku lina limanena kuti mawu a Yobu akuti “mukanandibisa,” ayenera kuti ankatanthauza kuti “munditeteze ngati chuma chamtengo wapatali.” Komanso buku lina limanena kuti pamenepa Yobu ankatanthauza kuti “mundibise ngati chuma chamtengo wapatali.”
^ ndime 6 Baibulo limalonjeza kuti anthu adzaukitsidwa n’kukhala m’dziko latsopano lolungama. Kuti mudziwe zambiri za zimenezi, werengani mutu 7 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.