Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
“Uthenga wabwino uwu wa ufumu . . . ”—MATEYU 24:14.
PA ULALIKI wake wa paphiri, womwenso ndi wotchuka kwambiri, Yesu ananena pemphero lachitsanzo. Ena mwa mawu a m’pempheroli ndi akuti: “Ufumu wanu ubwere.” Anthu ambiri analoweza pemphero limeneli ndipo nthawi zambiri amalinena mobwerezabwereza. Buku lina linafotokoza kuti limeneli ndi “pemphero lofunika kwambiri limene Akhristu onse amaligwiritsa ntchito polambira.” Ngakhale zili choncho, anthu ambiri amene amanena pempheroli sadziwa kuti Ufumuwo n’chiyani ndiponso kuti udzachita chiyani ukadzabwera.—Mateyu 6:9, 10.
Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu akafuna kufotokoza kuti Ufumu umenewu ndi chiyani, amanena mfundo zosokoneza, zotsutsana ndiponso zovuta kumvetsa. Mwachitsanzo, m’busa wina analemba kuti Ufumu wa Mulungu ndi “mphamvu inayake ya Mulungu, . . . mgwirizano wamumtima umene umakhala pakati pa munthu ndi Mulungu wamoyo . . . , ubwenzi umene amuna ndi akazi amakhala nawo ndi Mulungu, umene umawathandiza kupeza chipulumutso.” Winanso ananena kuti uthenga wa Ufumu ndi “malangizo onena za tchalitchi.” Ndipo Katekesimu wa Akatolika amanena kuti: “Ufumu wa Mulungu [ndi] chilungamo, mtendere ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.”
Koma patsamba 2 la magazini ino mungapeze tanthauzo lenileni la Ufumu wa Mulungu. Pali mawu akuti: “Ufumu wa Mulungu, umene ndi boma lenileni lakumwamba, posachedwapa udzachotsa zoipa zonse ndi kusandutsa dziko lapansi paradaiso.” Tiyeni tione mmene Baibulo limasonyezera kuti zimenezi ndi zoona.
Kodi Ndani Adzalamulire Dziko Lapansi?
Ufumu ndi boma lolamulidwa ndi mfumu. Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndi Yesu Khristu amene anaukitsidwa. Iye anaikidwa pampando wachifumu kumwamba ndipo zimenezi zinafotokozedwa m’masomphenya amene mneneri Danieli anaona. Danieli analemba kuti: “Ndiyeno m’masomphenya ausikuwo, ndinaonanso wina wooneka ngati mwana wa munthu [Yesu] akubwera m’mitambo. Iye analoledwa kufika kwa Wamasiku Ambiri uja, [Yehova Mulungu] ndipo anamubweretsa pafupi kwambiri ndi Iye. Kenako anamupatsa ulamuliro, ulemerero, ndi ufumu kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira. Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.”—Danieli 7:13, 14.
Buku la m’Baibulo la Danieli limasonyezanso kuti Mulungu adzakhazikitsa Ufumu umene udzawononge maboma onse a anthu ndipo Ufumuwo udzakhalapo mpaka kalekale. Chaputala 2 cha buku la Danieli chimanena za maloto amene Mulungu analotetsa mfumu ya ku Babulo. M’maloto amenewo, mfumuyo inaona fano lalikulu limene linaimira maufumu osiyanasiyana amphamvu kwambiri a padziko lapansi. Potanthauzira malotowo, mneneri Danieli anati: “M’masiku otsiriza . . . Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”—Danieli 2:28, 44.
Koma Mfumu ya Ufumu wa Mulungu sidzalamulira yokha. Pa nthawi imene Yesu ankachita utumiki wake padziko lapansi anauza atumwi ake okhulupirika kuti, iwowo ndiponso anthu ena adzaukitsidwa n’kupita kumwamba ndipo adzakhala m’mipando yachifumu. (Luka 22:28-30) Apa Yesu sankatanthauza mipando yeniyeni chifukwa iye anafotokoza kuti Ufumu umenewu uli kumwamba. Baibulo limafotokoza kuti anthu amene akalamulire limodzi ndi Yesu ndi “ochokera mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse.” Anthu amenewa adzakhala “mafumu ndi ansembe a Mulungu wathu, moti adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.”—Chivumbulutso 5:9, 10.
Kodi N’chifukwa Chiyani Uthenga wa Ufumu Uli Wabwino?
Lemba lija lasonyeza kuti Khristu Yesu adzapatsidwa ufumu kuti alamulire “anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana.” Ndiyeno kodi ndani adzakhale nzika za Ufumu umenewu? Ndi anthu amene amamvera ndi kukhulupirira uthenga wabwino umene ukulalikidwa masiku ano. Enanso ndi anthu amene adzaukitsidwe n’kupatsidwa mwayi wokhala ndi moyo padziko lapansi kwamuyaya.
Baibulo limafotokoza momveka bwino madalitso amene anthu adzakhale nawo mu Ufumu umenewu. Taonani ena mwa madalitso amenewo.
“Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi. Wathyola uta ndi kuduladula mkondo. Ndipo watentha magaleta pamoto.”—Salimo 46:9.
“Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya.”—Yesaya 65:21, 22.
“[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
“Pa nthawi imeneyo, maso a anthu akhungu adzatsegulidwa, ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva. Pa nthawiyo, munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo. Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.”—Yesaya 35:5, 6.
“Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake [a Yesu] ndipo adzatuluka. Amene anali kuchita zabwino adzauka kuti alandire moyo.”—Yohane 5:28, 29.
“Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:11.
Kunena zoona umenewu ndi uthenga wabwinodi. Ndiponso maulosi a m’Baibulo amene akwaniritsidwa kale amasonyeza kuti nthawi yoti Ufumu wa Mulungu uyambe kulamulira mwachilungamo padziko lapansi yatsala pang’ono.