N’chifukwa Chiyani Mabanja Ambiri Akutha?
N’chifukwa Chiyani Mabanja Ambiri Akutha?
“Afarisi anabwera kwa [Yesu], ndipo pofuna kumuyesa anamufunsa kuti: ‘Kodi n’kololeka kuti mwamuna asiye mkazi wake pa chifukwa chilichonse?’”—Mateyu 19:3.
ANTHU ena a m’nthawi ya Yesu ankakayikira mfundo yakuti anthu akakwatirana ayenera kukhalira limodzi moyo wawo wonse. Iwo ankaonanso kuti zimenezo n’zosatheka. Choncho Yesu anawauza kuti: “Kodi simunawerenge kuti amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi n’kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’? Chotero salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” * (Mateyu 19:4-6) Ndiyetu ndi zachidziwikire kuti Mulungu amafuna kuti mabanja asamathe.
M’mayiko ambiri masiku ano okwatirana ambiri ‘akulekana’ kapena kuti kusudzulana. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti malangizo a m’Baibulo okhudza ukwati ndi achikale moti sakugwiranso ntchito masiku ano? Kodi n’kutheka kuti mabanja amatha chifukwa n’zosatheka kuti mwamuna ndi mkazi azikhala limodzi kwa moyo wawo wonse?
Taganizirani chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti mabanja awiri agula galimoto zofanana. Banja lina likusamalira bwino galimoto yawo ndipo amaiyendetsa mosamala kwambiri. Choncho galimotoyo siikuwonongeka. Koma banja linali silisamalira galimoto yawo ndiponso saiyendetsa mosamala. Kenako galimotoyo ikuwonongeka ndipo eni akewo ainyanyala. Kodi pamenepa vuto n’chiyani, galimotoyo kapena eni akewo? N’zosachita kufunsa kuti vuto lalikulu ndi eni ake a galimotoyo.
Mofanana ndi zimenezi, kutha kwa mabanja ambiri sikutanthauza kuti dongosolo loti mwamuna ndi mkazi azikwatirana lili ndi vuto. Tikutero chifukwa pali mabanja ambirimbiri amene akuyenda bwino. Mabanja oterewa amachititsa kuti anthu a m’banjamo komanso anthu akuderalo azikhala osangalala ndiponso azikhala ndi mtendere wa m’maganizo. Koma monga mmene zilili ndi galimoto, ukwati kuti usathe umafunika kuusamalira bwino nthawi zonse.
Kaya mwangokwatirana kumene kapena munakwatirana kalekale, malangizo a m’Baibulo okhudza zimene mungachite kuti ukwati wanu ukhale wolimba angakuthandizeni. Werengani ena mwa malangizowa m’nkhani yotsatirayi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Baibulo limanena kuti ukwati ukhoza kutha ngati mwamuna kapena mkazi wachita chigololo.—Mateyu 19:9.