Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Anakhazikitsa Pansi Mtima wa Yehova”

“Anakhazikitsa Pansi Mtima wa Yehova”

Yandikirani Mulungu

“Anakhazikitsa Pansi Mtima wa Yehova”

MUNTHU wina anasiya kutsatira malangizo a Mulungu amene anaphunzitsidwa ali mwana. Ponena za nthawi imeneyo iye ananena kuti: “Ndinkangoona kuti ndine wachabechabe.” Koma atayamba kusintha moyo wake, ankaopa kuti mwina Mulungu samukhululukira. Komabe atawerenga nkhani ya Manase yomwe ili pa 2 Mbiri 33:1-17, munthu wolapa ameneyu anazindikira kuti Mulungu angamukhululukire. Ngati mumadziona kuti ndinu wosafunika chifukwa cha machimo amene munachita m’mbuyomu, nanunso nkhani imeneyi ingakulimbikitseni.

Manase anakulira m’banja loopa Mulungu. Bambo ake anali Hezekiya ndipo anali mmodzi mwa mafumu abwino kwambiri a mtundu wa Ayuda. Manase anabadwa patapita zaka zitatu kuchokera pamene Mulungu anawonjezera zaka za moyo wa bambo ake mozizwitsa. (2 Mafumu 20:1-11) Ndi zosachita kufunsa kuti Hezekiya ankaona kuti mwana wawoyu anali ngati mphatso imene Mulungu anawapatsa atawakomera mtima ndipo anayesetsa kumuphunzitsa kuti azikonda kulambira Mulungu m’njira yoyenera. Koma si ana onse a makolo oopa Mulungu amene amatengeradi khalidwe labwino la makolo awo. Chitsanzo cha zimenezi ndi Manase.

Bambo a Manase anamwalira iye asanakwanitse zaka 13. Koma chomvetsa chisoni ndi chakuti, Manase “anachita zoipa pamaso pa Yehova.” (Mavesi 1, 2) Kodi mfumu yachinyamatayi inachita zimenezi chifukwa chotengera alangizi ake amene sankatsatira kulambira koona? Baibulo silinena. Koma limanena kuti Manase anachita zinthu zoipa kwambiri monga kulambira mafano komanso nkhanza. Iye anamangira milungu yonyenga maguwa ansembe, anaotcha ana ake ena aamuna monga nsembe, ankachita zamizimu ndiponso anaika chifaniziro chogoba m’kachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Manase ankakana kumvera malangizo ndipo sanamvere machenjezo obwerezabwereza ochokera kwa Yehova, Mulungu amene anachita chozizwitsa kuti Manaseyo abadwe.​—Mavesi 3-10.

Kenako Yehova analola kuti Manase amangidwe n’kupita naye ku ukapolo ku Babulo. Ali kumeneko, iye anaganizira mozama za moyo wake. Mwina tsopano anatha kuona kuti mafano ake opanda mphamvu komanso opanda moyowo analephera kumuteteza. Mwinanso anakumbukira zimene bambo ake oopa Mulungu anamuphunzitsa ali wamng’ono. Kaya anaganiziladi zimenezi kapena ayi, koma Manase anasintha mtima wake. Baibulo limati: “Anakhazikitsa pansi mtima wa Yehova Mulungu wake ndipo anadzichepetsa kwambiri . . . Manase anayamba kupemphera kwa Mulungu.” * (Mavesi 12, 13) Koma kodi munthu otereyu amene anachita machimo akulu kwambiri Mulungu akanamukhululukiradi?

Yehova anakhudzidwa kwambiri chifukwa Manase analapa mochokera pansi pamtima. Mulungu anamva kuchonderera kwake kuti amuchitire chifundo ndipo “anam’bwezera ku Yerusalemu ku ufumu wake.” (Vesi 13) Posonyeza kuti walapadi, Manase anayesetsa kusiyiratu zolakwa zake. Anasiya kulambira mafano ndipo anauza anthu ake “kuti azitumikira Yehova.”​—Mavesi 15-17.

Ngati mukuona kuti Mulungu sangakukhululukireni chifukwa cha machimo amene munachita, chitsanzo cha Manase chingakulimbikitseni kwambiri. Nkhani yonena za Manase ndi mbali ya Mawu a Mulungu ouziridwa. (Aroma 15:4) N’zodziwikiratu kuti Yehova amafuna kuti tidziwe kuti iye ndi “wokonzeka kukhululuka.” (Salimo 86:5) Munthu akachita tchimo, Mulungu sayang’ana kukula kapena kuchepa kwa tchimolo koma amayang’ana mtima wa munthuyo. Wochimwa akapemphera ndi mtima wolapa, kusiya machimo ake, n’kuyamba kuyesetsa kuchita zinthu zabwino ‘angakhazike pansi mtima wa Yehova,’ ngati mmene Manase anachitira.​—Yesaya 1:18; 55:6, 7.

Mavesi amene mungawerenge mu January:

2 Mbiri 29-36Ezara 1-10

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Baibulo lina linamasulira lembali kuti: “Iye . . . anasangalatsa nkhope ya Mulungu wake Yehova.”​—Young’s Literal Translation.