Tsiku Limene Tinapita Kunyanja
Kalata Yochokera ku Grenada
Tsiku Limene Tinapita Kunyanja
NGATI mudzakhale ndi mwayi wotumikira m’dziko lina monga mmishonale, mudzasangalala kwambiri. Mudzakhala ndi chidwi chachikulu poganizira anthu akumeneko, mmene malo ake alili ndiponso zimene mukakumane nazo mu utumiki wakumunda.
Ine ndi mkazi wanga atatiuza kuti tipite ku Grenada, dziko limene lili ndi magombe pafupifupi 45 okongola kwambiri, sitinachitire mwina koma kumangoganizira za mmene magombewo amaonekera. Posapita nthawi, tinakhala ndi mwayi wosangalala pagombe limodzi mwa magombe amenewa. Chimene chinatisangalatsa kwambiri ndicho anthu osati kuwala kwa dzuwa kapena kusewera panyanja.
Tinanyamuka pa galimoto kuchoka kunyumba kwathu ku Grenada kupita kugombe la Grand Anse. Ulendowu si wautali kwambiri, koma ndi wosangalatsa zedi. Msewu wake ndi wokhotakhota. Chifukwa cha kukhotakhota kwa msewuko tinkatha kuona malo osiyanasiyana okongola kwambiri. Derali lili ndi mapiri a mitengo yobiriwira bwino kwambiri. Tinkati tikakhota timaona mapiri okongola, nkhalango zobiriwira bwino, mathithi ndiponso mbali ina ya nyanja yokongola kwambiri. N’chifukwa chake alendo oona malo ochokera ku mayiko osiyanasiyana amabwera kudzaona malowa. Malo amenewa ndi okongola kwambiri moti woyendetsa galimoto amafunika kukhala wosamala kuti asasokonezeke pochita chidwi ndi kukongola kwa malowa. Misewu yake ndi yokhotakhota komanso yaing’ono kwambiri moti malo ena umadabwa ngati magalimoto awiri angathe kudutsana osagundana.
Kenako tinafika pamalo ochitira msonkhano a Convention Trade Center amene ali m’mphepete mwa msewu, pagombe la Grand Anse. Posapita nthawi, Mboni za Yehova pafupifupi 600 zinasonkhana kuti zisangalale ndi macheza ndiponso malangizo a m’Baibulo. Tsikuli linali lofunika kwambiri makamaka kwa a Lesley ndi akazi awo a Daphne omwe ali ndi zaka za m’ma 70. Pa tsikuli a Lesley amayembekezera kubatizidwa. A Daphne anakhala akuyembekezera tsiku limeneli kwa nthawi yaitali chifukwa iwo anabatizidwa kukhala Mboni ya Yehova mu 1958.
Kwa Mboni za Yehova, ubatizo umenewu, womwe umachitika mwa kumiza munthu m’madzi, ndi wofunika kwambiri. Munthu amabatizidwa akaphunzira choonadi cha m’Baibulo ndiponso akamatsatira zimene waphunzirazo pa moyo wake. Pa ubatizo woterewu m’pamene munthu amasonyezera poyera kuti anadzipereka kwa Yehova Mulungu.
Ndinali nditapemphedwa kuti pamsonkhanowu ndikambe nkhani yofotokoza zimene Malemba amanena pa nkhani ya ubatizo. Nditamaliza kukamba nkhaniyo, a Lesley limodzi ndi anthu ena awiri amenenso amayembekezera kubatizidwa anaimirira. Iwo anali akumwetulira kwambiri atavala malaya oyera ositidwa bwino ndiponso tayi. Kenako, ndinafunsa anthuwo kuti: “Kodi
mwalapa machimo anu ndi kudzipereka kwa Yehova kuti muchite chifuniro chake?” Zinali zoonekeratu kuti anthuwo anali okhulupirika ndi odzipereka pamene anayankha mochokera pansi pa mtima kuti “Inde!”Popeza ndinkadziwa mmene moyo wa a Lesley unalili, zimenezi zinandikhudza kwambiri. Kwa zaka zambiri, sankafuna kuphunzira Baibulo. Kenako iwo ndi akazi awo anapita kukaona malo pachilumba chinachake. Ali kumeneko, iwo anagwirizana kuti aliyense apite kutchalitchi chake. A Lesley anauza akazi awo a Daphne kuti: “Inu mupite kutchalitchi chanu, inenso ndipita kutchalitchi changa.”
A Lesley anatenga akazi awo a Daphne kukawasiya ku Nyumba ya Ufumu ndipo iwo anapita kutchalitchi cha Anglican chimene chinali m’dera lomwelo. Mapemphero a kutchalitchicho atatha, a Lesley anabwerera ku Nyumba ya Ufumu kuti akatenge akazi awo. Atafika ku Nyumba ya Ufumu, anthu okoma mtima ndi ansangala anawalandira ndi manja awiri ngakhale kuti kunali kuyamba kuonana nawo. Zimenezi zinawachititsa chidwi kwambiri a Lesley chifukwa pamene anali kutchalitchi chawo palibe amene anawalankhula. Pambuyo pake, a Lesley anauza a Daphne kuti: “Sindidzapitanso kutchalitchi chimenechi. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anachita nane chidwi, ngakhale wansembe amene. Nditafika, palibe amene anandipatsa moni mpaka kuchokako.” A Lesley atachoka kutchalitchicho anatsimikiza mtima kuti sadzabwererakonso.
Pambuyo pake, a Lesley anayamba kuphunzira Mawu a Mulungu ndi mtima wonse. Tsopano iwo anali atakonzeka kuti abatizidwe. Kenako, anthu ofuna kubatizidwawo ananyamuka kupita kunyanja ndipo ife tinali kuwatsatira. Popeza nyanja inali pafupi kwambiri, panalibe chifukwa chokonzera malo a ubatizo ngati mmene zimakhalira pamisonkhano yambiri ya Mboni za Yehova. Tinangowoloka msewu n’kufika kunyanja.
Gombe la Grand Anse ndi lochititsa chidwi kwambiri. Lili ndi mchenga woyera ndipo madzi ake ooneka buluu amakhala otentha chaka chonse. Gombeli ndi lalitali makilomita atatu. Anthu okaona malo ataona gulu lathu likufika pagombelo anadabwa chifukwa amuna anavala malaya ndi matayi, ndipo akazi anavala madiresi ndi masiketi. Pa nthawiyi a Lesley anali atasintha zovala zawo. Tsopano anali atavala tisheti ndi kabudula. Tangoganizirani mmene a Daphne anamvera ataona amuna awo akubatizidwa patadutsa zaka 50 kuchokera pamene iwo anabatizidwa. A Daphne anamwetulira kwambiri ngati kuwala kwa dzuwa la masana amenewo. Ngakhale anthu odzaona malo anasangalala ndi ubatizowo. Iwo anali kuwomba nawo m’manja munthu akabatizidwa.
Gombeli limapereka ulemerero kwa Mlengi chifukwa cha kukongola kwake. Kumwamba sikukhala mitambo, mchenga wake umakhala woyera ndipo nyanjayi imachita timafunde ting’onoting’ono. Koma gombeli linapereka ulemerero kwambiri kwa Mlengi pamene anthu atatu obatizidwa kumene anatuluka m’nyanja. Kuona obatizidwawo kunatisangalatsa kwambiri kuposa kuona malo. Tsikuli linalidi lapadera. Kwa a Lesley ndi akazi awo a Daphne, tsikuli linali labwino kwambiri kuposa masiku ena onse omwe iwo anapezeka kugombeli.