Kodi Mkazi Amene Kaini Anakwatira Anachokera Kuti?
Zimene Owerenga Amafunsa . . .
Kodi Mkazi Amene Kaini Anakwatira Anachokera Kuti?
▪ “Ngati Adamu ndi Hava anali ndi ana aamuna awiri okha, Kaini ndi Abele, nanga mkazi wa Kaini anachokera kuti?” Kawirikawiri amene amafunsa funso limeneli amakhala anthu okayikira Baibulo pofuna kusokoneza anthu. Koma Baibulo lili ndi mfundo zina zotithandiza kuyankha funsoli.
M’machaputala 3 ndi 4 a Genesis muli mfundo izi: (1) Hava anali “amake wa amoyo onse.” (2) Panapita nthawi yaitali kuchokera pamene Kaini anabadwa kukafika pamene Mulungu anakana nsembe imene iye anapereka. (3) Kaini atapitikitsidwa n’kukhala “wothawathawa ndi woyendayenda” anada nkhawa kuti mwina ‘aliyense amene angakumane naye,’ angamuphe. (4) Mulungu anaika Kaini chizindikiro pofuna kumuteteza. Zimenezi zikusonyeza kuti abale ake kapena achibale ake ena akanatha kumupha. (5) “Patapita nthawi,” (NW) Kaini anagona ndi mkazi wake kumalo amene iye anathawirako.—Genesis 3:20; 4:3, 12, 14-17.
Kuchokera pa mfundo zimenezi, tingathe kunena kuti mkazi wa Kaini anali mbadwa ya Hava ngakhale kuti sitikudziwa nthawi imene anabadwa. Lemba la Genesis 5:4 limasonyeza kuti m’zaka 930 zimene Adamu anakhala ndi moyo, “anabala ana aamuna ndi aakazi.” Ngakhale zili choncho, Baibulo silinena mwachindunji kuti mkazi wa Kaini anali mwana wa Hava. Popeza akutchulidwa pambuyo poti Kaini wayamba moyo wothawathawa, zikusonyeza kuti panali patapita nthawi yaitali moti n’kutheka kuti mkaziyo anali mmodzi mwa zidzukulu za Adamu ndi Hava. N’chifukwa chake Baibulo lina limanena kuti mkazi wa Kaini anali “mbadwa ya Adamu.”—The Amplified Old Testament.
Katswiri wina wa Baibulo, wa m’zaka za m’ma 1800, dzina lake Adam Clarke, ananenapo maganizo ake pa nkhaniyi. Iye ananena kuti Mulungu anaika Kaini chizindikiro chomuteteza chifukwa kunali kale mbadwa za Adamu zambirimbiri, “zokwanira kupanga midzi yambiri,” ndipo ena mwa anthu amenewa akanatha kumupha.
Anthu ena masiku ano angaone kuti n’zosatheka kuti Kaini anakwatira mlongo wake kapena mdzukulu wina wa Adamu. Nthawi zambiri amakhala ndi maganizo amenewa chifukwa cha zimene amakhulupirira komanso chifukwa amaganiza kuti munthu atakwatira mlongo wake, angamabereke ana olumala. Komabe, F. LaGard Smith analemba kuti: “Zikuoneka kuti kale munthu ankatha kukwatira mlongo wake ngakhale kuti masiku ano anthu ambiri amaona kuti zimenezi n’zosayenera.” (The Narrated Bible in Chronological Order) Tiyeneranso kukumbukira kuti panalibe lamulo loletsa anthu kugonana pachibale mpaka pamene Mulungu anapatsa Aisiraeli malamulo kudzera mwa Mose m’chaka cha 1513 B.C.E.—Levitiko 18:9, 17, 24.
Panopa papita zaka zambiri kuchokera pamene makolo athu oyambirira anali angwiro. Choncho matenda amene ana amabadwa nawo masiku ano chifukwa chakuti makolo awo anakwatirana pachibale kunalibe nthawi imeneyo. Komanso zotsatira za kafukufuku wina zimene zinalembedwa m’magazini ina, zinasonyeza kuti si kawirikawiri kuti anthu amene akwatirana pachisuweni abereke ana olumala. Zimenezi n’zosiyana ndi zimene anthu ambiri amaganiza. (Journal of Genetic Counseling) N’zoonekeratu kuti limeneli silinali vuto pa nthawi imene Adamu anali ndi moyo kapenanso nthawi ya Nowa isanafike. Choncho tinganene kuti mkazi amene Kaini anakwatira anali mmodzi wa achibale ake.