Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

KODI mayi wina wa ku Russia, amene sali pa banja koma ali ndi ana, anasiya bwanji kumwa mankhwala osokoneza bongo? Nanga anatani kuti azikhala mosangalala ndi ana ake? Kodi n’chiyani chinathandiza mwamuna wina amene ankagona m’misewu ya mumzinda wa Kyoto ku Japan, kusintha khalidwe lake limene linamuchititsa kukhala wosauka chonchi? Nanga n’chiyani chinathandiza munthu wina ku Australia, amene anali woweta ng’ombe, kuti asiye kumwa mowa mwauchidakwa? Tamvani zimene anthuwa ananena.

“Ndinazindikira kuti ndili ndi udindo wopeza zosowa zanga.”​—NELLY BAYMATOVA

ZAKA: 45

DZIKO: RUSSIA

POYAMBA: ANKAKONDA KUMWA MANKHWALA OSOKONEZA BONGO

KALE LANGA: Ndinakulira mumzinda wa Vladikavkaz, likulu la dziko la Republic of North Ossetia (limene tsopano limatchedwa Alania). Kuyerekezera ndi mabanja ena, banja lathu linali lolemera. Koma ngakhale zinali choncho, sindinali munthu wosangalala. Ndili ndi zaka 34, ndinali nditakwatiwapo kawiri konse. Panthawi imeneyi, ndinali woti ndakhala ndikumwa mankhwala osokoneza bongo kwa zaka 10. Chifukwa cha vuto limeneli anandigoneka kawiri konse m’chipatala. Ngakhale ndinali ndi ana awiri, sindinkawakonda komanso sindinkagwirizana kwenikweni ndi azinzanga komanso abale anga.

Mayi anga anali atakhala a Mboni za Yehova, ndipo nthawi zambiri ndinali kuwamva akulira ndi kupempha Yehova kuti andithandize kusintha khalidwe langa. Mumtima ndinkangonena kuti: ‘Amayi nawonso! Palibe chimene akudziwa. Yehova sangandithandize.’ Ndinayesetsa ndithu kuti ndisiye kumwa mankhwala osokoneza bongo, koma ndinalephera. Nthawi ina ndinakhala masiku awiri osamwa mankhwalawo. Kenako ndinaganiza zotuluka m’nyumbamo ndipo ndinangodumpha kuchokera pawindo. Koma ndinaiwala kuti ndili m’chipinda chapamwamba cha nyumba yosanjikizana. Choncho ndinathyoka mkono ndi mwendo komanso ndinavulala msana. Ndinakhala ndili chigonere kwa mwezi umodzi milungu ingapo.

Panthawi imene ndinali kudwala, mayi anga anandisamalira ndipo sanandidzudzule pa zimene ndinachitazo. Iwo ankadziwa kuti ndikuvutika maganizo kwambiri ndipo mutu wanga sukuyenda bwino. Ngakhale zinali choncho, anandisiyira magazini a Galamukani! * pambali pa bedi langa. Ndinawerenga magazini onsewo ndipo ndinaona kuti munali mfundo zosangalatsa komanso zothandiza. Kenako ndinaganiza kuti ndiziphunzira Baibulo ndi a Mboni.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Chimodzi mwa zinthu zimene Baibulo linandiphunzitsa ndi kukumbukira kuti ndili ndi udindo wodzipezera zosowa zanga komanso za ana anga, m’malo modalira mayi anga. Kwa nthawi yaitali ndinkangochita zofuna zanga basi, choncho zinali zovuta kuti ndizolowere kugwira ntchito.

Komanso malangizo amene ali pa Deuteronomo 6:5-7 anandithandiza kwambiri. Lembali limauza makolo kuti aziphunzitsa ana awo za Mulungu. Ndinazindikiranso kuti ndidzakhala ndi mlandu kwa Mulungu ngati sindilera bwino ana anga. Choncho kudziwa zimenezi kunandilimbikitsa kuti ndiyambe kucheza nawo ndiponso kuwakonda.

Zinandikhudza mtima kwambiri kuona kuti Yehova anandilola kuti ndimudziwe bwino. Choncho ndinadzipereka kwa iye ndipo ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Poyamba ndinali wamtima wapachala koma ndinaphunzira kuugwira mtima. Zimenezi zinathandiza kuti ndiyambe kugwirizana ndi mayi anga. Ana anganso ndimakhala nawo bwino kuposa kale.

Popeza kuti ndinayamba kudana ndi zinthu zoipa, ambiri mwa mavuto amene ndinali nawo kale anatha. Masiku ano ndimasangalala kwambiri ndikamathandiza ena kudziwa Yehova, Mulungu wathu wachikondi.

“Ndikuona kuti ndikanafa kalekale.”​—MINORU TAKEDA

ZAKA: 54

DZIKO: JAPAN

POYAMBA: ANKAGONA M’MISEWU

KALE LANGA: Ndinakulira mumzinda wa Yamaguchi. Ndinkakhala ndi bambo anga komanso agogo anga aakazi, koma amayi anga sindinawaonepo. Agogo angawo anamwalira ndili ndi zaka 19 ndipo ndinapitiriza kukhala ndi bambo anga. Ndinkagwira ntchito yophika ndipo bambo anga ankagwiranso ntchito ngati yomweyi. Koma popeza nthawi zathu zogwira ntchito zinali zosiyana, sitinkaonana kawirikawiri. Kenako ndinayamba kugwira ntchito kwa maola ambiri komanso kumwa mowa ndi azinzanga.

Patapita nthawi, ntchito imene ndinkagwira inayamba kunditopetsa. Ndinkakangana kwambiri ndi bwana wanga ndipo ndinayamba kumwa kwambiri. Ndili ndi zaka pafupifupi 30, ndinachoka panyumba n’kuyamba kumangoyendayenda madera osiyanasiyana. Ndalama zitandithera, ndinayamba kugwira ntchito pamalo ena otchovera njuga. Kenako ndinapeza chibwenzi ndipo tinakwatirana. Koma patangopita zaka ziwiri ndi theka, banja lathu linatha.

Ndinali wokhumudwa kwambiri ndi mmene zinthu zinalili pamoyo wanga ndipo ndinkalephera kudziletsa pa zinthu zambiri. Komanso ndinali ndi ngongole zambiri ndi anthu opanga bizinesi yokongoza ndalama. Ndinathawa angongole n’kumakakhala kwathu ndi abambo. Ndili kumeneko ndinanamiza bambo anga zinazake ndipo zimenezi zinachititsa kuti tisamagwirizane. Ndinawabera ndalama ndipo kwa kanthawi ndinkatchova njuga kuti ndizipeza zofuna zanga pa moyo. Patapita nthawi ndinasaukiratu ndipo ndinayamba kukhala pamalo ena okwerera sitima yapamtunda. Nditachoka kumeneko ndinasamukira m’tawuni ya Hakata kenako mumzinda wa Himeji ndipo pomaliza pake ndinasamukira mumzinda wa Kyoto. Kwa zaka zingapo ndinalibe pokhala, choncho ndinkagona m’misewu.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Tsiku lina mu 1999, azimayi awiri Amboni anandipeza pamalo ena ochezera pafupi ndi mtsinje wa Kamogawa mumzinda wa Kyoto. Mmodzi wa azimayiwo anandifunsa kuti: “Kodi mungafune kuphunzira Baibulo?” Ndinavomera, ndipo Akhristu ena okhwima mwauzimu a mumpingo wina wapafupi wa Mboni za Yehova anayamba kundiphunzitsa Baibulo. Anandithandizanso kuzindikira kufunika kotsatira mfundo za m’Baibulo. Iwo anandiuza kuti zingakhale bwino nditapeza ntchito ndi nyumba. Pongofuna kuwasangalatsa ndinapita kukachita intavyu kumalo awiri, koma poyamba ndinalibe chidwi chenicheni. Komabe patapita nthawi, ndinayamba kupemphera kuti Yehova andithandize kupeza ntchito ndipo ndinaipezadi.

Pemphero linandithandizanso kupirira vuto lina lalikulu. Angongole aja anandifunafuna mpaka anandipeza n’kundiuza kuti ndiwapatse ndalama zawo. Zimenezi zinachititsa kuti ndikhale ndi nkhawa kwambiri. Popeza kuti ndinkawerenga Baibulo tsiku lililonse, tsiku lina ndinapeza lemba la Yesaya 41:10. Palembali, Mulungu analonjeza atumiki ake okhulupirika kuti: “Ndithu ndikuthandiza.” Lonjezo limeneli linandipatsa mphamvu ndiponso linandilimbikitsa kwambiri. Ndinayamba kulimbikira ntchito ndipo patapita nthawi ndinabweza ngongole zonse. M’chaka cha 2000 ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Zimene ndinaphunzira m’Baibulo zinandilimbikitsa kuti ndiyesetse kugwirizananso ndi bambo anga choncho anandikhululukira zonse zimene ndinawachitira m’mbuyomo. Iwo anasangalala kwambiri chifukwa choti ndinali kutsatira mfundo za m’Baibulo. Ndikuona kuti ndikanafa kalekale zikanakhala kuti sindinayambe kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wanga.

Komanso panopo ndimagwira ntchito kuti ndipeze zofunika pa moyo. (Aefeso 4:28; 2 Atesalonika 3:12) Kuwonjezera pamenepa ndinapezanso anthu abwino ocheza nawo mumpingo wachikhristu. (Maliko 10:29, 30) Ndikuthokoza Yehova kuchokera pansi pamtima pa zonse zimene wandiphunzitsa.

“Zinali zovuta kwambiri kuti ndisinthe.”​—DAVID HUDSON

ZAKA: 72

DZIKO: AUSTRALIA

POYAMBA: ANALI CHIDAKWA

KALE LANGA: Makolo anga anali Willie ndi Lucy ndipo m’banja mwathu ineyo ndinali mwana wa nambala 11. Tinkakhala m’tawuni yotchedwa Aurukun, kumpoto kwenikweni kwa chigawo cha Queensland. Anthu ochuluka m’tauni imeneyi tinali a mtundu wa Aborijini. Tawuni ya Aurukun inali m’mphepete mwa mwa mtsinje wa Archer, kufupi ndi nyanja. Makolo athu anatiphunzitsa anafe kusaka nyama ndi kupha nsomba kuti tizipeza zofunika pa moyo. Panthawi imeneyo, boma silimalola kuti Aaborijinife tizipatsidwa malipiro athu onse, ndipo tinalibe ufulu wosankha kokhala. M’malomwake boma linatipatsa malo apadera oti tizikhala.

Makolo anga anayesetsa kundiphunzitsa khalidwe labwino komanso kuphunzitsa ana tonsefe kulemekeza anthu achikulire. Chifukwa cha zimenezi tinkaona achikulire onse m’dera lathu ngati amayi, abambo, azakhali ndi amalume athu. Anatiphunzitsanso kukhala opatsa ngakhale kuti tinali osauka.

Bambo anga anamwalira ndili ndi zaka 7 ndipo tinasamukira kumudzi winawake wa Aaborijini okhaokha ku Mapoon. Kuchokera ku Aurukun kukafika ku mudzi umenewu, unali ulendo wa makilomita 150. Nditakwanitsa zaka 12 ndinayamba kuphunzira kuweta mahachi ndi ng’ombe ndipo ndinagwira ntchito imeneyi kwa anthu osiyanasiyana mpaka nditatsala pang’ono kukwanitsa zaka 50. Ambiri ogwira ntchito imeneyi anali ndi makhalidwe oipa ndipo inenso ndinkamwa mowa kwambiri. Chifukwa cha moyo wangawu, ndinakumana ndi mavuto ambiri.

Tsiku lina nditaledzera kwambiri, ndinayenda modzandira kutuluka mu hotelo. Nditalowa mumsewu galimoto inandigunda. Pa zaka ziwiri zotsatira ndinakhala ndikuyendera kuchipatala, moti ndinasiya ntchito yanga yoweta ng’ombe.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Panthawi imene ndimalandira chithandizo, mayi wina amene ndinkacheza naye anandibweretsera magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kuti ndiwerenge. Komabe popeza kuti sukulu sindinapite nayo patali, sindinkatha kuwerenga bwinobwino. Ndiyeno tsiku lina kunabwera bambo ena ake azaka 83. Kunja kunali kukutentha kwambiri, choncho ndinawaitanira m’nyumba kuti amweko madzi ozizira. Iwo anandipatsa mabuku ofotokoza Baibulo ndipo anandipempha kuti adzabwerenso kudzandifotokozera bwinobwino zimene zili m’mabukuwo. Kenako anayamba kundiphunzitsa Baibulo nthawi zonse moti ndinayamba kuona kuti pali zinthu zimene ndiyenera kusintha pa moyo wanga kuti ndikondweretse Mulungu.

Zinali zovuta kwambiri kuti ndisinthe. Koma chifukwa cha zimene mayi anga anandiphunzitsa, ndinkalemekeza kwambiri bambo wachikulire amene ankandiphunzitsa Baibulo, komanso ndinkalemekeza mfundo za choonadi zimene anali kundiphunzitsa. Ngakhale zinali choncho, sindinkafuna kudzipereka kwa Mulungu. Ndinali kuona kuti ndisanabatizidwe, ndiyenera kudziwa kaye china chilichonse chimene chinalembedwa m’Baibulo.

Kenako, mnzanga wina amene ndimagwira naye ntchito anandithandiza kusintha maganizo anga pa nkhani imeneyi. Iye anali wa Mboni za Yehova ndipo anandionetsa mfundo yolimbikitsa yomwe ili pa lemba la Akolose 1:9, 10. Lembali limati tiyenera ‘kuwonjezera kudziwa kwathu Mulungu molondola.’ Mnzangayu anandithandiza kuona kuti pali zambiri zoti ndiziphunzire. Choncho, ndinaona kuti sindiyenera kulola kuti kusadziwa zinthu zambiri kundilepheretse kudzipereka kwa Yehova.

Nditayamba kusonkhana ndi Mboni za Yehova, ndinachita chidwi ndi zimene ndinaona. Anthu a zikhalidwe ndi mitundu yosiyanasiyana anali kupembedza Mulungu mogwirizana. Kugwirizana kumeneku ndi kumene kunanditsimikira kuti ndapezadi chipembedzo choona. Choncho mu 1985 ndinabatizidwa, n’kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Panopo ndimatha kuwerenga bwinobwino moti mlungu uliwonse ndimathera nthawi yaitali kuthandiza anthu ena kuti aphunzire kuwerenga komanso kuti aphunzire Baibulo. Kuwonjezera pamenepa, mayi uja amene ndinkacheza naye ndipo anandipatsa magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! anayambanso kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Kenako anabatizidwa ndipo tsopano ndi mkazi wanga. Tonse tikusangalala kwambiri kuthandiza Aaborijini anzathu kuti aphunzire za Yehova Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 21]

Ineyo ndi mkazi wanga tikusangalala kwambiri kuthandiza Aaborijini anzathu kuti aphunzire za Yehova Mulungu