Kodi Mukudziwa?
Kodi Mukudziwa?
Kodi ndi zoona kuti nyerere zimakonza chakudya m’chilimwe ndiponso kusonkhanitsa chakudya m’nthawi yokolola?
▪ Lemba la Miyambo 6:6-8 limati: “Pita kunyerere, waulesi iwe, penya njira zawo nuchenjere; zilibe mfumu, ngakhale kapitawo, ngakhale mkulu; koma zitengeratu zakudya zawo m’malimwe; nizituta dzinthu zawo m’masika.”
Ndi zoona kuti nyerere zambiri zimasungadi chakudya chawo. Ndipo nyerere zimene Solomo anazitchula ziyenera kuti zili m’gulu la nyerere zina (Messor semirufus) zimene zimatutira mbewu kuuna. Nyererezi zimapezeka kwambiri ku Israel masiku ano.
Buku lina limanena kuti “nyerere zimenezi zimatuluka m’zisa zawo za pansi pa nthaka tsiku lililonse ngati kunja kwacha bwino kukafunafuna chakudya . . . [ndipo] m’miyezi yonse ya m’chilimwe zimakhala zikututa mbewu.” Nyerere zimenezi zimatola mbewu ku zomera kapena pansi. Ndipo zimamanga zisa zawo kumene kumapezeka mbewu zambiri monga m’minda, pafupi ndi nkhokwe kapena pafupi ndi malo opunthirapo mbewu.
Zikakhala m’chisa, nyererezi zimasunga chakudya chawo m’zipinda zosanjikizana zolumikizidwa ndi tinjira tambirimbiri. Zipinda zimenezi zimakhala zazikulu masentimita 12 ndipo kuchoka pansi kupita m’mwamba zimakhala sentimita imodzi. Nyererezi zikakhala ndi chakudya chambiri m’zisa zawo zimatha kukhala “miyezi inayi kapena kuposa, osatuluka panja kukafuna chakudya china kapena madzi.”
Kodi ntchito ya munthu woperekera chikho kwa mfumu inali yotani?
▪ Nehemiya anali woperekera chikho kwa Mfumu Aritasasta ya ku Perisiya. (Nehemiya 1:11) Kalekale m’nyumba zachifumu za ku Isiraeli ndi madera ena oyandikana nawo, ntchito yoperekera chikho kwa mfumu sinali ntchito wamba, koma unali udindo waukulu. Mabuku akale ndiponso zithunzi zakale kwambiri za operekera chikho, zimatithandiza kudziwa bwino ntchito imene Nehemiya ankagwira kunyumba yachifumu ya ku Perisiya.
Woperekera chikho ankalawa vinyo asanakapereke kwa mfumu pofuna kuteteza mfumuyo kuti isamwe vinyo wothira poizoni. Choncho mfumu inkadalira kwambiri munthu woperekera chikho. Katswiri wolemba mbiri yakale, dzina lake Edwin M. Yamauchi, analemba kuti: “Tikaona kuchuluka kwa ziwembu zimene zinkachitika m’nyumba zachifumu za ku Perisiya, tingaone kuti woperekera chikho ankafunika kukhala munthu wokhulupirika kwambiri.” Zikuoneka kuti woperekera chikho ankakondedwa kwambiri ndi mfumu ndipo mfumu inkamumvera. Popeza kuti ankakhala pafupi ndi mfumu tsiku ndi tsiku, iye ndi amene anali ndi udindo wololeza kapena kukaniza anthu kuonana ndi mfumu.
Mwina n’chifukwa chake Nehemiya atapempha kuti abwerere ku Yerusalemu kukamanganso mpanda wa mzindawo, mfumu inamulola mosavuta. Nehemiya ayenera kuti ankakondedwa kwambiri ndi mfumu chifukwa buku lina limanena kuti iye atapempha kuti apite ku Yerusalemu, “Mfumu inangomuyankha kuti, ‘Ubwerako liti?’”—Nehemiya 2:1-6, The Anchor Bible Dictionary.
[Chithunzi patsamba 9]
Zithunzi Zakunyumba Yachifumu ya ku Pesepoli, ku Perisiya
[Chithunzi]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Woperekera Chikho
Kalonga Wolowa Ufumu Dzina Lake Sasta
Dariyo Wamkulu
[Mawu a Chithunzi]
© The Bridgeman Art Library International