Dziwani Zoona Zake pa Nkhani ya Tchimo
Dziwani Zoona Zake pa Nkhani ya Tchimo
KODI munthu wodwala malungo anganene kuti sakudwala chifukwa chakuti wakana kulandira mankhwala? Ayi, sangatero. Mofanana ndi zimenezi, ngakhale kuti anthu ambiri saona tchimo mofanana ndi mmene Mulungu amalionera, sizikutanthauza kuti tchimolo palibe. Mawu ake, Baibulo, ali ndi mfundo zambiri pa nkhani imeneyi. Komano, kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani kwenikweni pa nkhani ya tchimo?
Tonse Timachimwa
Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, mtumwi Paulo ananena modandaula kuti, ‘zinthu zabwino zimene ankafuna kuchita sanachite, koma choipa chimene sankafuna kuchita ndi chimene ankachita.’ (Aroma 7:19) Tonse tikhoza kuvomereza kuti zimenezi zimatichitikiranso. Mwina timafuna kutsatira Malamulo Khumi kapena mfundo zina zamakhalidwe abwino, koma kaya tifune kapena tisafune, palibe amene angatsatire zimenezo popanda kulakwitsa. Sikuti timachita kufuna kuti tisamvere lamulo linalake, koma kungoti timalephera. Kodi n’chifukwa chiyani zimakhala chonchi? Paulo ananena chifukwa chake. Iye anati: “Tsopano ngati zimene sindifuna ndi zimene ndikuchita, amene akuchita zimenezo si inenso ayi, koma uchimo umene ukukhala mwa ine.”—Aroma 7:20.
Monga Paulo, tonse mwachibadwa timachita zinthu zina molakwitsa ndipo zimenezi zimasonyeza kuti tinabadwa ochimwa ndiponso opanda ungwiro. N’chifukwa chake mtumwi Paulo anati: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” Kodi chinachititsa n’chiyani kuti tikhale operewera pa ulemerero wa Mulungu? Paulo anapitiriza kuti: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo, imfayo nifalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’—Aroma 3:23; 5:12.
Ngakhale kuti anthu amakana mfundo yakuti kuchimwa kwa makolo athu oyambirira kunatipangitsa kuti tisakhale pa ubwenzi ndi Mulungu komanso kuti tisakhale angwiro, zimenezi n’zimene Baibulo limaphunzitsa. Yesu anasonyeza kuti ankakhulupirira nkhani ya Adamu ndi Hava chifukwa anagwira mawu chaputala choyamba cha Genesis.—Genesis 1:27; 2:24; 5:2; Mateyo 19:1-5.
Imodzi mwa mfundo zofunika kwambiri m’Baibulo ndi yakuti Yesu anabwera padziko lapansi kudzawombola anthu omukhulupirira ku uchimo. (Yohane 3:16) Kuti tidzakhale ndi moyo wosatha tiyenera kukhulupirira ndiponso kuyamikira njira imene Yehova wakonza kuti apulumutsire anthu ku mavuto amene amakumana nawo mwachibadwa. Koma ngati sitiona tchimo mofanana ndi mmene Mulungu amalionera, sitingadziwe komanso sitingayamikire njira imene iye wakonza kuti atipulumutse ku uchimowo.
Chifukwa Chake Nsembe ya Yesu ndi Yofunika
Yehova anapatsa munthu woyambirira, Adamu, mwayi wokhala ndi moyo kosatha. Zimenezi zikanatheka akanamvera Mulungu. Koma Adamu sanamvere Mulungu, ndipo anachimwa. (Genesis 2:15-17; 3:6) Adamu anachita zinthu zosiyana ndi zimene Mulungu ankafuna, analephera kukhala wangwiro ndipo anasokoneza ubwenzi wake ndi Mulungu. Atachimwa chifukwa chosamvera lamulo la Mulungu, iye anayamba kukalamba ndipo mapeto ake anamwalira. Zachisoni ndi zakuti ana onse a Adamu, kuphatikizaponso ifeyo, tinabadwa ochimwa amene chilango chake ndi imfa. Chifukwa chiyani zili choncho?
Yankho la funso limeneli n’losavuta. Makolo opanda ungwiro sangabereke ana angwiro. Ana onse a Adamu anabadwa ochimwa, ndipo malinga ndi zimene mtumwi Paulo ananena, “malipiro a uchimo ndiwo imfa.” (Aroma 6:23) Komabe kumapeto kwa lembali kumasonyeza kuti tingayembekezere zabwino, popeza kuli mawu akuti: “Mphatso imene Mulungu amapereka ndiyo moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” Chifukwa chakuti Yesu anapereka moyo wake nsembe, n’zotheka kuti anthu omvera, amene amayamikira nsembe imeneyi ayeretsedwe ku uchimo wa Adamu. * (Mateyo 20:28; 1 Petulo 1:18, 19) Kodi muyenera kumva bwanji ndi zimenezi?
Chikondi cha Khristu “Chitikakamiza”
Mtumwi Paulo ananena maganizo a Mulungu pa nkhani imeneyi. Iye analemba kuti: “Chikondi chimene Khristu ali nacho chitikakamiza, chifukwa tatsimikiza kuti, munthu mmodzi anafera onse; . . . Iye anaferanso onse kuti amoyo asadzikhalire moyo wa iwo eni, koma akhalire moyo iye amene anawafera naukitsidwa.” (2 Akorinto 5:14, 15) Ngati munthu amadziwa kuti nsembe ya Yesu ikhoza kumumasula ku uchimo ndiponso akufuna kusonyeza kuyamikira mphatso imeneyi, ayenera kuyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Zimenezi zimaphatikizapo kumvetsa zimene Mulungu amafuna, kuphunzitsa chikumbumtima chake motsatira mfundo za m’Baibulo, komanso kutsatira mfundozo pa moyo wake.—Yohane 17:3, 17.
Kuchita zoipa kumawononga ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu. Mfumu Davide atazindikira kuopsa kwa chigololo chimene anachita ndi Bateseba ndiponso atapha mwamuna wake, n’zachidziwikire kuti anachita manyazi kwambiri. Koma chimene chinamuvutitsa maganizo kwambiri n’chakuti tchimo limene anachitalo linakhumudwitsa Mulungu. Iye analapa kwa Yehova kuti: “Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu.” (Salmo 51:4) Chimodzimodzinso ndi Yosefe. Iye atayesedwa kuti achite chigololo, chikumbumtima chake chinamupangitsa kufunsa kuti: “Nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?”—Genesis 39:9.
Choncho, sikuti tchimo ndi loipa chifukwa chakuti munthu angachite manyazi akagwidwa. Ndiponso si nkhani yongoti ‘akandigwira ndikayankha.’ Mfundo ndi yakuti, kusamvera malamulo a Mulungu pa nkhani zogonana, kusaona mtima, ulemu, kulambira, ndiponso zinthu zina, kumawononga ubwenzi wathu ndi iye. Ngati timachita dala machimo, ndiye kuti tikudzipangitsa kukhala mdani wa Mulungu. Mfundo yoona 1 Yohane 3:4, 8.
imeneyi imafunika kuiganizira mofatsa.—Choncho kodi pali chimene chasintha pa nkhani ya uchimo? Ayi, palibe. Kungoti anthu anayamba kuutchula ndi mayina ena n’cholinga choti usamaoneke ngati nkhani yaikulu. Anthu ena samvera chikumbumtima chawo. Koma anthu onse amene amafuna kuti Mulungu aziwakonda ayenera kupewa zimenezi. Monga taonera, mphoto ya uchimo si kungowononga mbiri ya munthu kapena kuchita manyazi basi, koma ndi imfa. Choncho uchimo ndi nkhani ya moyo ndi imfa.
Nkhani yabwino ndi yakuti, n’zotheka kukhululukidwa machimo kudzera mu nsembe ya Yesu imene inatiwombola ku uchimo ndipo zimenezi zingatheke ngati tilapa machimo athu moona mtima ndi kuwasiya. Paulo analemba kuti: “Osangalala ndi awo amene akhululukidwa mphulupulu zawo ndipo machimo awo akwiriridwa; wosangalala ndi munthu amene tchimo lake, Yehova sadzaliwerengera konse.”—Aroma 4:7, 8.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 10 Kuti mumve zambiri zokhudza mmene nsembe ya Yesu ingapulumutsire anthu omvera, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? kuyambira patsamba 47 mpaka 54, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 10]
Tchalitchi cha Katolika Chasintha Maganizo
Akatolika ambiri akhala asakumvetsa chiphunzitso chakuti kuli malo ena ake otchedwa Limbo kumene kumapita mizimu ya anthu abwino amene amwalira asanabatizidwe kuphatikizaponso ana. M’zaka makumi angapo zapitazo, chiphunzitsochi chakhala chikuzimiririka moti panopo asiya kuchilemba mu akatekizimu awo. Ndipo mu 2007, Tchalitchi cha Katolika chinalemba kalata yothetseratu chiphunzitso chakuti kuli malo ena ake otchedwa Limbo. Kalatayo inafotokoza kuti “pali umboni womveka bwino wosonyeza kuti ana akhanda amene amamwalira asanabatizidwe adzapulumuka n’kulandira moyo wosatha.”—International Theological Commission.
N’chifukwa chiyani tchalitchichi chasintha maganizo chonchi? Chachita zimenezi pofuna kumasuka ku zimene munthu wina wa ku France wolemba nkhani m’nyuzipepala, dzina lake Henri Tincq, ananena. Iye anati, chimenechi ndi “chiphunzitso cholemetsa kwambiri chomwe anthu anali kuchikana ndipo chinkafunika kuchiikira kumbuyo nthawi zonse kuyambira m’zaka za m’ma 1100 mpaka kumapeto kwa zaka za m’ma 1900. Tchalitchi chinayambitsa chiphunzitso chimenechi n’cholinga chofuna kuopseza makolo kuti azikabatizitsa ana awo mwachangu.” Komabe, kusintha kwa chiphunzitsochi kwayambitsanso nkhani zina.
Kodi Chinali Chiphunzitso cha M’malemba Kapena cha Anthu? Mbiri imasonyeza kuti chiphunzitso chakuti kuli malo otchedwa Limbo chinayamba chifukwa cha kusagwirizana kwa akuluakulu atchalitchi pa nkhani ya anthu amene amapita ku purigatoliyo m’zaka za m’ma 1100. Tchalitchi cha Katolika chinkaphunzitsa kuti munthu akamwalira, mzimu wake sufa. Choncho zinali zovuta kufotokoza kumene mizimu ya ana akhanda amene amamwalira asanabatizidwe imapita. Zinali choncho, chifukwa iwo ankakhulupirira kuti popeza anawo ndi osabatizidwa, sapita kumwamba komanso anali osayenera kukaotchedwa ndi moto. Apa ndi pamene panayambira chiphunzitso cha Limbo.
Baibulo siliphunzitsa kuti munthu ali ndi chinthu chinachake chimene chimapitiriza kukhala ndi moyo munthuyo akamwalira. Koma limaphunzitsa momveka bwino kuti “akufa sadziwa kanthu bi” ndiponso kuti munthu akamwalira ‘amabwerera ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zimatayika.’ (Salmo 146:4; Mlaliki 9: 5, 10) Popeza kuti munthu alibe chinthu chimene chimapitiriza kukhala ndi moyo iye akamwalira, ndiye kuti malo otchedwa Limbo kulibe. Ndiponso Baibulo limafotokoza kuti munthu akafa amakhala ngati ali m’tulo.—Yohane 11:11-14.
Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amaona ana aang’ono omwe makolo awo ndi Akhristu kukhala oyera. (1 Akorinto 7:14) Mfundo imeneyi bwenzi ili yosamveka zikanakhala kuti makanda amafunika kubatizidwa kuti akapulumuke.
Chiphunzitso cha Limbo chinali chonyozetsa Mulungu ndipo chinkachititsa kuti m’malo moti anthu aziona Mulungu ngati Atate wawo wachikondi komanso wachilungamo, azimuona ngati Mulungu wankhanza kwambiri amene amalanga anthu osalakwa. (Deuteronomo 32:4; Mateyo 5:45; 1 Yohane 4:8) Choncho n’zosadabwitsa kuti Akhristu oona mtima zinkawavuta kukhulupirira chiphunzitso chosachokera m’Malemba chimenechi.
[Zithunzi patsamba 9]
Kutsatira mfundo za Mawu a Mulungu kumatithandiza kuti tikhale ndi ubwenzi wabwino ndi Mulungu ndiponso anthu anzathu