“Uthenga Wabwino” Ukulalikidwa Kuzilumba Zakumpoto kwa Australia
“Uthenga Wabwino” Ukulalikidwa Kuzilumba Zakumpoto kwa Australia
YESU ananena kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mateyo 24:14) A Mboni za Yehova amatsatira lamulo la Yesu limeneli ndipo amayesetsa kulalikira uthenga wa m’Baibulo kwa anthu am’madera onse. (Mateyo 28:19, 20) Iwo amagwira ntchito imeneyi mongodzipereka ndipo nthawi zina amakumana ndi mavuto osiyanasiyana komanso amagwiritsa ntchito ndalama zawo.
Mwachitsanzo, Nathan ndi Carly anasiya moyo wawo wapamwamba kuti akwanitse kukalalikira kuzilumba zakutali zam’dera lotchedwa Torres Strait. Mu 2003, munthu wina woimira nthambi ya Mboni za Yehova ku Australia anawalimbikitsa kuti asamukire kuchilumba cha Thursday kuti azikagwira ntchito yolalikira limodzi ndi Mboni zamumpingo wapachilumbacho. Chilumba cha Thursday chili m’gulu la zilumba zimene zili m’nyanja ya Pacific pakati pa dziko la Australia ndi New Guinea.
Mu 2007, banja lawo linagula sitima yamatabwa yotchedwa Teisan-Y. Sitimayi anaigula kwa asodzi amene ankaigwiritsa ntchito pofufuza ngale zamtengo wapatali. Pogwiritsa ntchito ndalama zawo, iwo anakonzanso bwinobwino sitimayo n’kuyamba kuigwiritsa ntchito pokalalikira kuzilumba 10 zakutali kwambiri. Popita kuzilumba zimenezi, iwo ankachokera pachilumba cha Thursday. Nkhani yotsatirayi ikufotokoza mmene zinkakhalira pa maulendowa.
January 2008: Lero ndinatenga boti lamusitima yathu yotchedwa Teisan-Y n’kupita ku Bamaga kukatenga Mboni zina zokwana 6. Ulendowu ndi wautali makilomita 80, kupita ndi kubwera. Kenako tinakwera sitima yathuyo n’kuyamba ulendo wopita kuzilumba za Warraber ndi Poruma. Mathanki onse a sitimayi anali odzaza chifukwa tinathiramo mafuta okwana malita 5,500. Mafutawa tinagula pa mtengo wa madola awiri lita imodzi. Sitimayi imayenda pang’onopang’ono kwambiri ndipo imangolekeza makilomita 10 okha pa ola limodzi. Koma nyengo inali bwino kwambiri moti panyanja panalibe mafunde aliwonse.
Titafika, tinaimitsa sitima yathu m’madzi momwemo n’kukweza m’boti lija anthu ochepa amene ali ndi achibale awo ku Warraber. Kenako, tinapita kwa khansala wapachilumbacho kuti tikapemphe chilolezo cholalikira m’deralo. Iye anatilola kulalikira kwa anthu a pachilumbachi ngakhale kuti ndi m’busa wa tchalitchi china m’derali. Titafika ku Poruma, tinapemphanso chilolezo ndipo anatilola kulalikira. Anthu ake ndi ansangala kwambiri ndipo ndi ofunitsitsa kuwerenga mabuku athu. Tinayambitsa maphunziro a Baibulo ambiri.
April 2008: Tinakonzekera ulendo wopita kuzilumba zitatu zakutali kwambiri zotchedwa Dauan, Saibai, ndi Boigu. Zilumbazi zili kufupi ndi malire a dziko la Papua New Guinea (PNG). Koma nyengo inasintha mwadzidzidzi moti tinaganiza zopita kuchilumba cha Mabuiag. Chilumba cha Mabuiag chili pa mtunda wa makilomita 70 okha basi kuchokera ku doko lakwathu koma tinayenera kuyenda mtunda wa makilomita 140 chifukwa choti kayendedwe
kake kanali kokhotakhota popewa mapiri am’nyanja.Chifukwa cha mafunde amphamvu, boti lija linasiyana ndi sitima yathu. Ngakhale kuti mafundewo anali aatali kwambiri tinakhotetsa sitimayo kuti tikalikoke. Anthu ambiri amene anali m’sitimamo anayamba kuchita nseru chifukwa cha mafundewo.
Titafika ku Mabuiag anatipatsa chilolezo choti titha kulalikira. Anthu akumeneko anatilandira mwansangala kwambiri moti tinaiwala za mavuto onse amene tinakumana nawo. Mayi wina anafunitsitsa kwambiri kumvetsera uthenga wathu moti anapempha kuti tim’patse mabuku ena kuti akawaike m’nyumba yowerengeramo mabuku yam’deralo komwe iyeyo amagwira ntchito.
May Mpaka October 2008: Chifukwa cha kusintha kwa nyengo, tinalephera kupita kuzilumba zija. Tinagwiritsa ntchito mpata umenewu kulalikira kwa anthu akonkuno, kugwira ntchito, komanso kukonza bwinobwino sitima yathu.
Panali zinthu zambiri zofunika kukonza pa sitimayi moti tinaganiza zopita kudoko la Weipa, lomwe lili m’mbali mwa dziko la Australia n’kukweza sitimayo pa chingolo chachikulu kuti tiipititse kumtunda. Zimenezi zingamveke ngati zophweka, koma ntchito yake sinali yamasewera. Anthu a Mboni za Yehova amumpingo wa m’derali anasiya zintchito zawo n’kubwera kudzatithandiza. Ena anatithandiza kukonza mapaipi a madzi, kupenta, ndiponso ena ankagwira ntchito zaukalipentala. Mboni zina zinkatibweretsera chakudya. Ena ankabweretsa zinthu zosiyanasiyana zoti tidzagwiritse ntchito paulendo wotsatira wokalalikira kuzilumba zakutali. Tinayamikira kwambiri mtima wawo wochereza ndiponso thandizo lawo.
December 2008: Tinakonzekeranso zopita ku zilumba za Dauan, Saibai, ndi Boigu. Pogwiritsira ntchito makina ounikira am’sitimayo tinatha kuzemba mphepo yamkuntho, ndiponso mapiri am’nyanja. Kuti tifike ku Dauan tinayenda ulendo wautali wa maola 12, komabe tinasangalala chifukwa sitinaonepo chilumba chokongola ngati chimenechi. Pachilumbachi pali mapiri amiyala aatali kwambiri omwe anali okutidwa ndi mitambo. Anthu a ku Dauan anamvetsera uthenga wathu mwachidwi ndipo tinakonza zoti tikakafika kwathu, tidzapitirize kuphunzira nawo Baibulo pa telefoni.
Mayi wina wapachilumbachi, dzina lake Lettie, anali atalandira kale magazini athu ndipo analembera kalata ofesi ya nthambi ya ku Australia yopempha kuti amutumizire mabuku ena. Ofesiyi inamutumizira mabukuwo ndipo inatumizanso kalata kumpingo wathu n’kupempha kuti, ngati tingakwanitse, tikaonane naye. Tinayesetsa mpaka tinam’peza ndipo tinasangalala kuti pang’ono pokha tinathandiza kum’patsa zosowa zake zauzimu.
Titafika ku Saibai, khansala wapachilumbachi anatikaniza kulalikira. Iye anangololeza kuti anthu amene ali ndi achibale awo pachilumbachi angathe kupita kukawachezera. Boma linandilemba ntchito yakanthawi kochepa yopenta nyumba za ku Saibai. Ntchito imeneyi inandithandiza kupeza ndalama zogulira zinthu zina ndi zina.
Mmodzi wa alongo athu, dzina lake Tassie, anachokera m’mudzi wina wa ku PNG womwe uli pamtunda wa makilomita pafupifupi 4 kuchokera ku Saibai. Boma la Australia linavomera kuti anthu a ku PNG azibwera ku Saibai kudzachita malonda. Tassie anakumana ndi anthu ambiri akumudzi kwawo moti mabuku amene anali nawo anawaperewera. Aka kanali koyamba kuti Tassie aonanenso ndi anthu akumudzi kwawo chikhalire wa Mboni za Yehova. Tinapita kumene kunali sitima yathu ndipo tinamubweretsera bokosi la mabuku. Mabuku ambiri
anali m’chilankhulo cha ku PNG chotchedwa Chitoku Pisini. Tassie analalikira gulu la anthu oposa 30 ochokera ku PNG ndipo mabuku onse omwe anali mu bokosi lija anaperekedwa kwa anthu achidwi. Anthuwa amakhala kumudzi umene munthu angakafike pogwiritsa ntchito boti kapena sitima basi, moti mwina sakanadzapeza mwayi wochezeredwa ndi Mboni za Yehova.Ulendo wopita kuchilumba chathu chomaliza cha Boigu unali wovuta kwambiri. Tinkayenda pa mtunda wamakilomita pafupifupi 4 kuchokera kumtunda koma madzi ake anali akuya mamita awiri ndi theka basi. Zimenezi zinali zoopsa chifukwa sitima yathu ikakhala panyanja, mbali yopitirira mita imodzi ndi theka imakhala m’madzi. Motero ine ndi munthu wina amene tinali naye paulendowu tinatenga boti lam’sitima yathu lija kuti tifufuze njira yabwino imene tingadzere kuti tikafike pachilumbacho. Mvula inkavumba kwambiri moti tinali madzi okhaokha. Zinatitengera maola awiri kuti tipeze njira yokafika kuchilumbachi.
Titafika, anthu apachilumbachi anandiuza kuti mapu athu anali olakwika ndipo ngakhale asilikali olondera panyanja safika kuno. Khansala wapachilumbacho anatikaniza kulalikira koma analola anthu amene anali ndi achibale awo pachilumbapo kuti angathe kukaonana nawo. Ife tinamvera zimene khansalayo ananena motero tinapita kukaona achibale athu basi. Munthu wina analandira buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, * ndipo analiwerenga nthawi yomweyo. Kenaka anayamba kulemba m’Baibulo mwake mafunso amene anali nawo. Munthuyu tinadzakumana nayenso pamene anabwera kuchilumba cha Thursday.
January 2009: Tinabwerera ku chilumba cha Moa ndi Mabuiag kuti tikachezenso ndi anthu amene anachita chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo umene tinawauza. Pazilumba zonse ziwiri tinalandiridwa ndi manja awiri. Anthu am’mudzi wa St. Paul pachilumba cha Moa anatiuza kuti tikabwerenso mwamsanga kudzacheza nawo. Khansala wapachilumbachi anatiuza kuti tikhale omasuka kudzalalikira m’derali nthawi iliyonse imene tingafune.
Ku Torres Strait kuli zilumba 17 zimene kumakhala anthu. Sitikudziwa ngati tingathe kuphunzira ndi anthu onse apazilumbazi. Komabe tonse amene tili mumpingo wa kuno kuzilumba za kumpoto kwambiri kwa Australia timasangalala tikamayesetsa kutamanda Mlengi wathu Wamkulu, Yehova.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 17 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mapu patsamba 23]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
AUSTRALIA
Weipa
Bamaga
ZILUMBA ZA KU TORRES STRAIT
PAPUA NEW GUINEA
[Mawu a Chithunzi]
Based on NASA/Visible Earth imagery
[Mapu pamasamba 24, 25]
Bamaga
Chilumba cha Thursday
Chilumba cha Moa
Chilumba cha Warraber
Chilumba cha Poruma
Chilumba cha Mabuiag
Chilumba cha Saibai
Chilumba cha Dauan
Chilumba cha Boigu
PAPUA NEW GUINEA
[Mawu a Chithunzi]
Based on NASA/Visible Earth imagery
[Chithunzi patsamba 24]
Tikufika pachilumba cha Thursday
[Chithunzi patsamba 24]
Tikupita kukacheza ndi anthu a pa chilumba cha Saibai
[Chithunzi patsamba 25]
Kulalikira uthenga wabwino m’Chitoku Pisini