Munthu Amene Anasintha Dziko
Munthu Amene Anasintha Dziko
Anthu ambiri amabadwa, kukula kenako n’kumwalira. Ambiri akafa, sasiya mbiri iliyonse. Koma ndi anthu ochepa chabe amene zochita zawo zakhudza kwambiri anthufe, mwinanso zochita zathu zatsiku ndi tsiku.
TIYEREKEZERE kuti mwangodzuka kumene m’mawa ndipo mwayatsa magetsi n’kumakonzekera kupita kuntchito. Kenako mukutenga buku kapena magazini kuti muziwerenga m’basi popita kuntchitoko. Ndiyeno popeza kuti simukupeza bwino kwenikweni, mukumwa mankhwala amene munalandira kuchipatala opha tizilombo toyambitsa matenda. Ngakhale kuti kunja kwangocha kumene, mwagwiritsa kale ntchito zinthu zingapo zimene anthu ena otchuka, monga otsatirawa, anatulukira.
Michael Faraday Anabadwa m’chaka cha 1791, ndipo anali katswiri wa sayansi wa ku England, yemwe anatulukira kapangidwe ka magetsi. Zimene anatulukirazo zathandiza kuti anthu ambiri azigwiritsa ntchito magetsi.
Ts’ai Lun Anali wogwira ntchito kunyumba yachifumu ya ku China ndipo cha m’ma 105 C.E., anapeza njira yopangira mapepala ambiri.
Johannes Gutenberg Anali wa ku Germany ndipo cha m’ma 1450, anapanga makina oyamba osindikizira mabuku. Makinawa athandiza kuti pasamawonongedwe ndalama zambiri popanga mabuku ndipo zimenezi zathandiza kuti anthu ambiri azipeza mosavuta mabuku a nkhani zosiyanasiyana.
Alexander Fleming Anali katswiri wazofufuzafufuza wa ku Scotland ndipo mu 1928, anatulukira kapangidwe ka mankhwala omwe anawatcha penicillin, ndipo amapha tizilombo toyambitsa matenda. Masiku ano, mankhwala opha tizilombo toyambitsa matenda akugwiritsidwa ntchito kwambiri.
Apa n’zoonekeratu kuti zinthu zimene anthu ena ochepa anatulukira zikuthandiza anthu ambiri m’njira zosiyanasiyana, monga kukhala ndi thanzi labwino.
Komabe, pali munthu mmodzi yekha wotchuka kwambiri amene sangafanane ndi wina aliyense. Iye sanatchuke chifukwa chotulukira zinthu zosiyanasiyana monga zasayansi kapena zamankhwala. Koma anatchuka chifukwa cha uthenga wake, womwe ndi wamphamvu chifukwa ndi wopatsa chiyembekezo komanso wotonthoza. Munthuyu ndi wotchuka kwambiri ngakhale kuti anabadwira m’banja losauka ndipo anamwalira zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Anthu akaona mmene uthenga wake wakhudzira anthu ambiri padziko lonse, amavomereza kuti iye anasintha zinthu kwambiri padziko lapansili.
Munthu ameneyo ndi Yesu Khristu. Kodi iye ankalalikira uthenga wotani? Ndipo uthenga wake ungakhudze bwanji moyo wanu?