Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mpaka Imfa Idzatilekanitse”

“Mpaka Imfa Idzatilekanitse”

“Mpaka Imfa Idzatilekanitse”

ANTHU ambiri amanena mawu amenewa mosangalala patsiku la ukwati wawo ndipo n’kutheka kuti saganizira n’komwe zoti tsiku lina imfa ingadzawalekanitsedi. Mkazi kapena mwamuna angamwalire chifukwa cha ukalamba, matenda, kapena ngozi ndipo munthu wotsalayo angamasungulumwe komanso angakhale wachisoni.​—Mlaliki 9:11; Aroma 5:12.

Malipoti amasonyeza kuti pafupifupi theka la azimayi a zaka 65 kapena kupitira, ndi amasiye. Popeza kuti kawirikawiri akazi ndi amene amakhala amasiye, anthu ambiri amaganiza kuti umasiye ndi chinthu chimene chimachitikira akazi okha. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti nawo amuna samavutika chifukwa cha imfa ya akazi awo. Pali anthu ambiri amene anaferedwa mkazi kapena mwamuna wawo. Kodi inunso ndinu wamasiye?

Kaya ndinu mwamuna kapena mkazi, kodi mungachite chiyani ngati zimenezi zakuchitikirani? Kodi Baibulo lingakuthandizeni kuthetsa chisoni chanu? Kodi amuna ndiponso akazi ena amene mwamuna kapena mkazi wawo anamwalira anapirira bwanji? Ngakhale kuti mwina njira imene ena anagwiritsa ntchito pa vuto lawo singakhale yothandiza kwa ena, pali mfundo komanso maganizo osiyanasiyana amene angakuthandizeni.

Vomerezani Kuti Zachitikadi

Anthu ambiri amaona kuti kulira sikwabwino ndipo n’kochititsa manyazi. Koma katswiri wina wa zamaganizo, yemwenso ndi wamasiye, dzina lake Dr. Joyce Brothers, anayerekezera misozi ndi chithandizo chimene chimaperekedwa kwa munthu amene wangovulala kumene. Ndipotu kulira munthu ukakhala ndi chisoni n’kwachibadwa ndipo kumathandiza kuti mtima ukhale m’malo. Choncho, musamachite manyazi kugwetsa misozi. Baibulo limafotokoza kuti Abulahamu nayenso anagwetsa misozi. Iye anali ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso anatchedwa bwenzi la Mulungu. Komabe mkazi wake Sara, yemwe ankamukonda kwambiri, atamwalira iye ‘anadza ku maliro ake, kuti amulire.’​—Genesis 23:2.

Ngakhale kuti aliyense amafuna kukhala ndi mpata wokhala payekha, simuyenera kufika podzipatula. Lemba la Miyambo 18:1 limatichenjeza kuti: “Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda.” (NW) Choncho, m’malo modzipatula, ndi bwino kupempha kuti abale anu ndiponso anzanu akuthandizeni. Malo abwino kumene mungapeze thandizo limeneli ndi mumpingo wachikhristu. Kumeneko abale okhwima mwauzimu angakupatseni thandizo komanso malangizo ngati akufunikira.​—Yesaya 32:1, 2.

Anthu ena aona kuti kuyankha makalata ndiponso makadi opepesa amene anthu anawalembera n’kothandiza. Kuchita zimenezi kungakupatseni mwayi wolemba zinthu zabwino zimene mkazi kapena mwamuna wanuyo ankachita komanso zinthu zosangalatsa zimene munkachitira limodzi. Komanso zingakuthandizeni ngati mutapanga buku lokhala ndi zithunzi, makalata, ndiponso mawu ofotokoza zochitika zina zosaiwalika. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kupirira.

Nthawi zambiri munthu amene waferedwa kumene amasokonezeka maganizo. Koma vutoli lingachepe ngati mutapitirizabe kuchita zimene mumachita nthawi zonse. Mwachitsanzo, ngati muli ndi nthawi yokhazikika imene mumagona, kudzuka, kudya, kapena kugwira ntchito zina, yesetsani kupitiriza kuchita zimenezi. Konzeranitu zimene mudzachite Loweruka ndi Lamlungu ndiponso masiku ena apadera, monga tsiku limene munakwatirana, popeza panthawi imeneyi m’pamene chisoni chimawonjezereka. Komanso ndi bwino kupitiriza kutsatira ndandanda yanu yochitira zinthu zauzimu.​—1 Akorinto 15:58.

Nthawi zambiri munthu amalephera kusankha zinthu mwanzeru akakhala kuti ali ndi nkhawa. Ndipo nthawi zina anthu amaganizo oipa angafune kupezerapo mwayi pa vuto lanulo. Choncho, pewani kuchita zinthu mopupuluma pa nkhani monga kugulitsa nyumba yanu, kuyamba bizinezi yaikulu, kusamuka, kapena kukwatiranso. Mwambi wina wothandiza umati: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu; koma yense wansontho angopeza umphawi.” (Miyambo 21:5) Muyenera kudikira kaye musanasankhe zochita pa nkhani zikuluzikulu ngati zimenezi mpaka maganizo anu atakhazikika.

Kusankha zochita pa katundu wa mwamuna kapena mkazi wanu kungakupatseni maganizo ambiri, makamaka ngati munakhala naye pabanja kwa zaka zambiri. Komabe simungachitire mwina chifukwa mukazengereza zingakutengereni nthawi yaitali kuti musiye kuganizira kwambiri za imfayo. (Salmo 6:6) Ena amaona kuti ndi bwino kusankha paokha zoyenera kuchita ndi katunduyu, pamene ena amaona kuti ndi bwino kukhala ndi mnzawo wapamtima amene angamvetse chisoni chawo. Mungapemphenso mnzanu kapena wachibale kuti akuthandizeni posainira zinthu zosiyanasiyana monga zikalata zakuchipatala zokhudza imfa ya malemuwo, zikalata zakubanki, makampani opereka zinthu pangongole, kusintha zikalata zosonyeza mwini wake wa katundu, chithandizo chakuboma kapena kuntchito, ndiponso kulipira ndalama zakuchipatala.

Kumbukirani kuti tikukhala m’dziko limene anthu ake ndi okonda makhalidwe oipa. Popeza tsopano muli nokha, zingakhale zovuta kuti mupitirize kukhala odziletsa. Mawu a mtumwi Paulo ndi othandizabe masiku ano. Iye anati: “Aliyense wa inu akhale woyera mwa kudziwa kusunga thupi lake m’chiyero ndi ulemu. Osati mwa chilakolako chosalamulirika cha kugonana, chonga chimenenso amitundu aja osadziwa Mulungu ali nacho.” (1 Atesalonika 4:4, 5) Choncho, ndi nzeru kupewa mafilimu, mabuku, ndiponso nyimbo zachikondi kapena zokhudza kugonana.

Mfundo yofunika kwambiri ndi yakuti, zimatenga nthawi kuti maganizo a munthu akhazikikenso ngati poyamba. Nyuzipepala ya USA Today inanena kuti kafukufuku amene akatswiri apayunivesite ina (University of Michigan Institute for Social Research) anachita, anasonyeza kuti munthu amene mkazi kapena mwamuna wake wamwalira, amafunika miyezi 18 kuti maganizo ake komanso thanzi lake ziyambenso kubwerera mwakale. Pempherani kwa Mulungu kuti akuthandizeni kupirira, komwe kumatheka chifukwa cha zipatso za mzimu wake. (Agalatiya 5:22, 23) Ngakhale kuti panopo mungaone ngati zosatheka, dziwani kuti pang’ono ndi pang’ono, zinthu zidzayambiranso kuyenda bwino.

Zimene Zathandiza Anthu Ena

Anna, yemwe wakhala m’banja kwa zaka 40, anakhudzidwa kwambiri ndi imfa ya mwamuna wake. Iye anati: “Mayi anga anamwalira ine ndili ndi zaka 13, kenako bambonso anamwalira. Ndinalinso ndi achimwene anga awiri ndi mchemwali wanga ndipo onsewa anamwaliranso. Komabe ndinganene kuti imfa ya anthu onsewa sinandikhudze kwambiri ngati mmene inandikhudzira imfa ya mwamuna wanga. Zinangokhala ngati andidula pakati moti ululu wake unali wosapiririka.” Kodi n’chiyani chinamuthandiza? Iye anapitiriza kuti: “Ndinapanga buku lalikulu limene ndinaikamo mauthenga ndiponso makadi okhala ndi mawu achikondi ndiponso oyamikira makhalidwe onse abwino amene mwamuna wanga Darryl anali nawo. Pa khadi lililonse ndinalembapo khalidwe limodzi lapadera limene anali nalo. Ndikukhulupirira kuti Yehova nayenso amamukumbukira ndipo adzamuukitsa akamadzaukitsa akufa.”

Mkazi wina wazaka 88, dzina lake Esther, nayenso anafotokoza chimene chamuthandiza kupirira. Iye anati: “Ndakhala limodzi ndi mwamuna wanga kwa zaka 46, choncho panopo vuto lalikulu limene ndili nalo ndi kusungulumwa. Komano ndazindikira kuti kutanganidwa ndi zinthu zauzimu kwandithandiza kwambiri. Sindinasiye chizolowezi changa chopezeka pamisonkhano yachikhristu, kulalikira, ndiponso kuwerenga Baibulo pandekha. Chinanso chimene chandithandiza ndicho kusakonda kukhala pandekha. Ndimakonda kukhala ndi anzanga amene amandimvetsera ndikamawalongosolera mavuto anga. Nthawi zina samakhala ndi mawu aliwonse olimbikitsa oti n’kundiuza, komabe ndimawayamikira chifukwa chokhala ndi nthawi yomvetsera zimene ndikuwafotokozera.”

Mkazi wa Robert anamwalira ndi matenda a khansa atakhala pabanja zaka 48. Iye anafotokoza kuti: “N’zovuta kwambiri kupirira imfa ya mkazi wako amene wakhala ukucheza naye, kupita naye koyenda, kuthandizana naye posankha zinthu, ndiponso kumuuza zinthu zosiyanasiyana zimene zachitika tsikulo. Imfa ya mkazi wanga inandikhudza kwambiri, komabe ndaona kuti ndifunika kupitirizabe kuchita zinthu ndiponso kusangalala ngati kale. Kukhala ndi zochita zambiri kwandithandiza kwambiri. Nalonso pemphero landithandiza kwambiri kuti ndipirire imfa ya mkazi wanga.”

Mungathe Kukhalabe Osangalala

Munthu aliyense amakhudzidwa kwambiri chifukwa cha imfa ya mkazi kapena mwamuna wake, koma dziwani kuti amenewa si mathero a zonse. Panthawiyi, mukhoza kukhala ndi mpata wambiri kuposa poyamba wochita zinthu monga kupita kocheza kapena kupuma. Kuchita zinthu ngati zimenezi n’kothandiza kuti muzisangalala. Kwa ena, zimenezi zingawapatsenso mpata wambiri wochita nawo utumiki wachikhristu. N’zachidziwikire kuti kugwira nawo ntchito ngati zimenezi kungakupatseni chimwemwe chifukwa Yesu anati: “Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

Musamakhale ndi maganizo akuti simudzasangalalanso pamoyo wanu. Khulupirirani kuti Yehova Mulungu angakusamalireni ngati mutamupempha. Wamasalmo Davide anati: “[Yehova] agwiriziza . . . mkazi wamasiye.” (Salmo 146:9) N’zosangalatsa kuti Baibulo limalongosola kuti Yehova ndi “Tate wa chifundo chachikulu ndi Mulungu wa chitonthozo chonse.” Limanenanso za Yehova kuti: “Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.” (2 Akorinto 1:3; Salmo 145:16) Ndithudi, Mulungu wachikondi, Yehova, ali ndi mphamvu ndipo ndi wokonzeka komanso wofunitsitsa kuthandiza aliyense amene amamudalira. Choncho, muyenera kukhala ndi maganizo ofanana ndi amene Aisiraeli anali nawo. Iwo anaimba kuti: “Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.”​—Salmo 121:1, 2.

[Mawu Otsindika patsamba 19]

Pali anthu ambiri amene anaferedwa mkazi kapena mwamuna wawo. Kodi inunso ndinu wamasiye?

[Bokosi patsamba 21]

Kodi Ndi Bwino Kukwatiranso?

Baibulo limanena kuti ukwati umatha ngati mwamuna kapena mkazi wamwalira ndipo munthu wotsalayo amakhala ndi ufulu wokwatiranso. (1 Akorinto 7:39) Komabe, munthu ayenera kusankha yekha kukwatiranso kapena ayi. Ngakhale zili choncho, ngati n’kotheka, ana ayenera kudziwa zimene kholo lawo lasankha pa nkhaniyi ndipo ayenera kugwirizana nazo. (Afilipi 2:4) Mwachitsanzo, Andrés poyamba sankafuna kuti bambo ake akwatirenso. Iye ankawakonda kwambiri mayi ake moti ankaona kuti sibwino kuti wina alowe m’malo mwawo. Iye anati: “Koma kenako ndinazindikira kuti bambo anachita bwino posankha kukwatiranso. Iwo anayambanso kukhala osangalala ngati poyamba. Anayambiranso kuchita zinthu zimene anali atasiya kwa nthawi yaitali, monga kupita koyenda. Ndiponso ndimayamikira zimene mkazi wawo watsopanoyu amachita powasamalira bwino kwambiri komanso kuonetsetsa kuti akumakhala osangalala.”

[Zithunzi pamasamba 20, 21]

Kukhala ndi zochita zambiri ndiponso kupemphera kwa Mulungu kungathandize munthu kupirira