Kodi Adamu ndi Hava Anali Anthu Enieni?
Kodi Adamu ndi Hava Anali Anthu Enieni?
ANTHU ambiri amaona kuti nkhani ya Adamu ndi Hava yopezeka m’buku la Genesis ndi nthano chabe yosangalatsa. Kalata ina yopita kwa mkonzi wa magazini ina inati: “Anthu a m’zipembedzo zikuluzikulu zachikhristu amakhulupirira kuti nkhani za m’buku la Genesis monga ya Adamu ndi Hava ndi nthano.” (Time) Anthu ambiri achikatolika, a matchalitchi ena, ndiponso akatswiri amaphunziro achiyuda amakhulupirira zimenezi. Iwo amati nkhani zambiri za m’buku la Genesis sizigwirizana ndi mbiri yakale kapena nkhani za sayansi.
Kodi inuyo mumaona bwanji nkhani imeneyi? Kodi mumakhulupirira kuti Adamu ndi Hava anali anthu enieni? Kodi pali umboni wosonyeza kuti iwo anakhalapodi? Nanga pangakhale mavuto otani ngati anthu atamakhulupirira kuti nkhani ya m’buku la Genesis ndi nthano chabe?
Nkhani ya M’buku la Genesis Imagwirizana ndi Sayansi
Choyamba, tiyeni tione mfundo zikuluzikulu za nkhani ya kulengedwa kwa munthu woyambirira. Ponena za Adamu, Baibulo limati: “Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.” (Genesis 2:7) Kodi mawu amenewa ndi ogwirizana ndi zimene asayansi apeza?
Buku lina (Nanomedicine) linafotokoza kuti thupi la munthu linapangidwa ndi zinthu zosiyanasiyana zokwana 41. Zinthu zimenezi ndi mpweya umene timapuma, mpweya wa kaboni ndiponso mchere wosiyanasiyana monga aironi. Ndipotu zinthu zonsezi zimapezeka ‘m’dothi’ lapansi. N’chifukwa chake buku la Genesis limati anthu anapangidwadi ndi “dothi lapansi.”
Kodi zinatheka bwanji kuti zinthu zopanda moyo zimenezi zipange munthu wamoyo? Kuti timvetse mmene zinakhalira, tiyeni tiyerekezere ndi chombo chopangidwa ndi bungwe la NASA, chomwe anthu amakwera popita mu mlengalenga. * Kodi thupi, lomwe n’lopangidwa mwaluso ndiponso lodabwitsa kwambiri, linakhalako bwanji? Linakhalako mwangozi kapena linachita kulengedwa?
Chombochi chinapangidwa movuta kumvetsa kuposa makina alionse amene anthu apanga. Chombo chimenechi chili ndi zipangizo zochuluka kwambiri zokwana 2.5 miliyoni. Ndipo akatswiri ambirimbiri anagwira nawo ntchito yopanga chombochi ndipo inawatengera zaka zochuluka. Tsopano ganizirani za thupi la munthu. Linapangidwa ndi tinthu ting’onoting’ono totchedwa maatomu tokwana 7 okitiliyoni, maselo 100 thililiyoni, ziwalo zambirimbiri, ndiponso mbali zofunika kwambiri zosachepera 9.Nanga n’chiyani chimachititsa kuti munthu akhale ndi moyo? Kodi moyo unachokera kuti? Asayansi amavomereza kuti sakudziwa. Ndipotu iwo sagwirizana pa nkhani yakuti moyo n’chiyani. Koma anthu amene amakhulupirira kuti kuli Mlengi, yankho n’lodziwikiratu. Moyo unachokera kwa Mulungu. *
Kodi muyenera kukhulupirira zimene buku la Genesis limanena kuti Hava analengedwa kuchokera ku nthiti ya Adamu? (Genesis 2:21-23) Musananene kuti zimenezi ndi nthano kapena zongopeka chabe, taganizirani mfundo iyi: Mu January 2008, asayansi ku California, m’dziko la America, anapanga koyamba miluza ya anthu imene imakula bwino, kuchokera ku maselo a khungu la munthu wamkulu. Ndipotu pogwiritsa ntchito njira yomweyi, asayansi apanga nyama zosachepera 20. Imodzi mwa nyama zimenezi ndi nkhosa yotchuka kwambiri, dzina lake Dolly, imene anaipanga mu 1996 kuchokera ku maselo a mabere a nkhosa. *
Sitikudziwa kuti zitha bwanji ndi zinthu zamoyo zimene asayansi akupangazi. Koma mfundo ndi yakuti: Ngati anthu akutha kugwiritsa ntchito zinthu zamoyo kupanga chinthu china chamoyo chofanana nacho, kodi Mlengi Wamphamvuyonse angalephere kupanga munthu kuchokera ku chiwalo cha munthu wina? Chochititsa chidwi n’chakuti madokotala ochita opaleshoni yodzikongoletsa, nthawi zambiri amagwiritsa ntchito nthiti pokonza ziwalo zina chifukwa nthiti zimatha kumera ndi kukulanso.
Umboni wa M’Baibulo
Anthu ena amadabwa kuti Adamu ndi Hava amatchulidwa kawirikawiri m’Baibulo. Kodi zimenezi zimatsimikizira bwanji kuti nkhani ya m’buku la Genesis ndi yoona?
m’buku la 1 Mbiri chaputala 1 mpaka 9, ndiponso Uthenga Wabwino wa Luka chaputala 3. Buku la 1 Mbiri limatchula mwatsatanetsatane makolo a mibadwo 48 ndipo Luka amatchula makolo a mibadwo 75. Buku la Luka limatchula m’badwo wa makolo a Yesu Khristu, pomwe buku la 1 Mbiri limatchula mibadwo ya ansembe a mtundu wa Isiraeli. Mabuku onsewa amatchula maina a anthu odziwika bwino monga Solomo, Davide, Yakobo, Isake, Abulahamu ndi Nowa ndipo pomalizira pake amatchula Adamu. Maina onse a m’mabuku amenewa ndi a anthu enieni, ndipo Adamu anali munthu weniweni pa m’ndandanda uliwonse.
Mwachitsanzo, onani ndandanda ya makolo achiyuda otchulidwa m’BaibuloKomanso, kawirikawiri Baibulo limatchula Adamu ndi Hava kuti anali anthu enieni, osati anthu ongopeka. Mwachitsanzo, taonani malemba otsatirawa:
• “Kuchokera mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu.”—MACHITIDWE 17:26.
• “Uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo . . . choncho, imfa inalamulira monga mfumu kuyambira kwa Adamu mpaka kwa Mose.”—AROMA 5:12, 14.
• “Munthu woyambirira, Adamu, anakhala munthu wamoyo.”—1 AKORINTO 15:45.
• “Adamu ndiye anayamba kupangidwa, kenako Hava.”—1 TIMOTEYO 2:13.
• “Inoke, wa m’badwo wachisanu ndi chiwiri kuchokera kwa Adamu, ananenera za [anthu oipa].”—YUDA 14.
Yesu Khristu, mboni yokhulupirika kwambiri yotchulidwa m’Baibulo, anasonyeza umboni wamphamvu kwambiri wakuti Adamu ndi Hava anakhalakodi. Yesu atafunsidwa zankhani ya kuthetsa banja, iye anayankha kuti: “Kuyambira pachiyambi pa chilengedwe, ‘Mulungu anapanga iwo mwamuna ndi mkazi. Pa chifukwa chimenechi, mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’ . . . Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Maliko 10:6-9) Kodi Yesu akanagwiritsa ntchito nthano pophunzitsa anthu zofunika kuchita pankhani ya ukwati? Ayi ndithu. Yesu anagwira mawu a m’buku la Genesis chifukwa ndi nkhani yeniyeni.
Poikira ndemanga pa umboni wa m’Malemba umenewu, buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo linati: “Chipangano Chatsopano chimatsimikizira kuti nkhani yofotokozedwa m’machaputala oyambirira a m’buku la Genesis inachitikadi.”—The New Bible Dictionary.
Nkhani ya Adamu ndi Hava Imakhudza Nkhani Zonse za M’Baibulo
Anthu ambiri okonda kupemphera amakhulupirira kuti nkhani ya Adamu ndi Hava si yofunikira kuti munthu akhale Mkhristu wabwino. Zimenezi zingaoneke ngati zoona. Koma tiyeni tione ngati maganizo amenewa ali oona.
Mwachitsanzo, taonani nkhani ya m’Baibulo yokhudza dipo imene anthu ambiri opemphera amaona kuti ndi yofunika kwambiri. Mawu akuti dipo amatanthauza kuti Yesu Khristu anapereka moyo wake wangwiro monga nsembe yopulumutsa anthu ku uchimo. (Mateyo 20:28; Yohane 3:16) Monga tikudziwira, dipo ndi mtengo wokwanira kuwombolera kapena kugulanso chinthu chomwe chinatayika kapena kuwonongedwa. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti Yesu ndi ‘dipo lolingana.’ (1 Timoteyo 2:6) Koma tingafunse kuti, kodi ndi dipo lolingana ndi chiyani? Baibulo limayankha kuti: “Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.” (1 Akorinto 15:22) Moyo wangwiro umene Yesu anapereka kuti awombole anthu omvera unali wolingana ndi moyo wangwiro umene Adamu anataya pamene anachimwa m’munda wa Edene. (Aroma 5:12) Ndithudi, ngati Adamu sanali munthu weniweni, ndiye kuti nsembe ya dipo imene Khristu anapereka ikanakhala yopanda tanthauzo.
Kukana kapena kusavomereza nkhani ya m’buku la Genesis ya Adamu ndi Hava kumakhudza pafupifupi ziphunzitso zonse zikuluzikulu za m’Baibulo. * Maganizo amenewa amabweretsa mafunso ambiri amene alibe mayankho ndipo amapangitsa kuti zimene anthu amakhulupirira zikhale zopanda maziko.—Aheberi 11:1.
Kodi Cholinga cha Moyo N’chiyani?
Tsopano tafika pa funso lofunika ili: Kodi kukana zoti nkhani ya m’buku la Genesis ndi yeniyeni kumapangitsa kuti anthu apeze zimene amafuna, zomwe ndi moyo wosangalala ndiponso watanthauzo? Malinga ndi maganizo a munthu wina wotchuka dzina lake Richard Dawkins, yemwe amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina, ndiponso kuti kulibe Mulungu, zinthu za kumwamba ndi padziko lapansi “sizinachite kulengedwa ndiponso zilibe cholinga chilichonse.” Amenewatu ndi maganizo osalimbikitsa, osagwirizana ndi umunthu.
Mosiyana ndi maganizo amenewa, Baibulo limapereka mayankho ogwira mtima a mafunso ofunika kwambiri ngati awa: Kodi anthufe tinachokera kuti? Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? N’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri? Kodi kuipa kudzatha? Limaperekanso mayankho a mafunso ena ambiri. Komanso kukhulupirira dipo la Khristu kumapangitsa kuti tikhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’Paradaiso, ngati wa m’munda wa Edene, umene Mulungu anaika anthu oyambirira aja, Adamu ndi Hava. (Salmo 37:29; Chivumbulutso 21:3-5) Umenewutu ndi moyo wabwino kwambiri umene tikuuyembekezera. *
Ngakhale kuti nkhani ya Adamu ndi Hava sigwirizana ndi maganizo akuti zamoyo zinachita kusanduka ku zinthu zina, nkhaniyi imagwirizana ndi sayansi. Komanso imagwirizana kwambiri ndi Mawu onse ouziridwa ndi Mulungu, omwe ndi Baibulo, amene amathandiza anthu kukhala ndi moyo wosangalala komanso watanthauzo.
Choncho, bwanji osayamba kuphunzira Baibulo mwakhama? Mboni za Yehova ndi zokonzeka ndiponso zofunitsitsa kukuthandizani.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Malinga ndi kawerengedwe ka manambala ka ku America, 7 okitiliyoni ndi 7 ndi mazilo 27, pomwe 100 thililiyoni ndi 100 ndi mazilo 12.
^ ndime 8 Kuti mumve zambiri, onani buku lakuti, Is There a Creator Who Cares About You? ndi lakuti, Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Mabukuwa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ ndime 9 Komabe, asayansi amenewa sikuti amalenga zinthu zamoyo. Koma, amangogwiritsa ntchito maselo a zinthu zamoyo zimene zilipo kale.
^ ndime 25 Zina mwa ziphunzitso zimenezi ndi zokhudza ulamuliro wa Mulungu, kukhulupirika kwa anthu, nkhani yokhudza chabwino ndi choipa, ufulu wosankha zochita, mmene akufa alili, ukwati, Mesiya wolonjezedwa, dziko laparadaiso, Ufumu wa Mulungu ndi zina zambiri.
^ ndime 28 Kuti mumve zambiri, onani buku lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? mutu 3, wakuti, “Kodi Mulungu Ali Nalo Cholinga Chotani Dziko Lapansili?,” ndi mutu 5, wakuti, “Dipo la Yesu Ndilo Mphatso ya Mulungu ya Mtengo Wapatali Koposa Zonse.”
[Mawu Otsindika patsamba 14]
Ndithudi, ngati Adamu sanali munthu weniweni, ndiye kuti nsembe ya dipo imene Khristu anapereka ikanakhala yopanda tanthauzo
[Zithunzi pamasamba 12, 13]
Mofanana ndi mmene chombo chinapangidwira mwaluso, thupi la munthunso linachita kulengedwa
[Chithunzi patsamba 15]
Yesu anasonyeza kuti Adamu ndi Hava anali anthu enieni