Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chipembedzo Chabwino Chimalimbikitsa Anthu Kulemekeza Mawu a Mulungu

Chipembedzo Chabwino Chimalimbikitsa Anthu Kulemekeza Mawu a Mulungu

YESU ankalemekeza Mawu a Mulungu, omwe ndi Baibulo. Tikudziwa zimenezi tikaona mmene anayankhira Mdyerekezi, panthawi imene ankamuyesa. (Mateyo 4:4-11) Mwachitsanzo, kodi Yesu anayankha bwanji Satana atamuuza kuti asandutse miyala kukhala mkate? Poyankha, Yesu anagwiritsa ntchito mawu amene Mose analemba mouziridwa, opezeka pa Deuteronomo 8:3. Nanga kodi Yesu anayankha bwanji Mdyerekezi atamuuza kuti amugwadire ndipo am’patsa maufumu onse adziko lapansi? Iye anakana pogwiritsa ntchito mfundo ya pa lemba la Deuteronomo 6:13.

Tangoganizani, ngakhale kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu, zonse zimene ankaphunzitsa zinali zogwirizana ndi Baibulo. Iye sananyalanyaze Mawu a Mulungu ngakhale pang’ono potsatira miyambo ya anthu. (Yohane 7:16-18) Koma atsogoleri ambiri achipembedzo panthawiyo sankalemekeza Mawu a Mulungu. N’chifukwa chiyani iwo ankachita zimenezi? Chifukwa choti ankaona kuti miyambo ya anthu ndi yofunika kwambiri kuposa Malemba Opatulika. Yesu anauza atsogoleri achipembedzowa mosapita m’mbali kuti: “Mupeputsa mawu a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu. Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yawo; koma mtima wawo uli kutali ndi Ine. Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.”​—Mateyo 15:6-9, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Zipembedzo zambiri zachikhristu ndiponso zomwe si zachikhristu zimanena kuti zimalemekeza Baibulo. Komano kodi ndi zipembedzo zingati zimene inuyo mukudziwa kuti sizichita nawo miyambo inayake ngati aona kuti sikugwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu amaphunzitsa? Onani zitsanzo ziwiri zokha.

NKHANI: Maina aulemu.

ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: Yesu anadzudzula atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake chifukwa chofuna kutchuka ndiponso kuti anthu aziwatchula maina aulemu. Iye ananena kuti anthu amenewa “amakonda malo a ulemu pa maphwando ndi malo ofunika kwambiri m’masunagoge; amakonda kupatsidwa moni m’misika kuti anthu aziwatchula kuti ‘Rabi.’” Kenako Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Inu simuyenera kutchulidwa ‘Rabi,’ popeza muli naye Mbuye mmodzi ndipo inu nonse ndinu abale. Ndipo musatchule wina aliyense pansi pano kuti ‘Atate,’ pakuti muli ndi Atate mmodzi ndipo ali kumwamba.”​—Mateyo 23:1-10, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

FUNSO: Kodi atsogoleri achipembedzochi amakonda maina aulemu ndiponso kutchuka? Kapena kodi iwo amamvera lamulo la Yesu loletsa khalidweli?

NKHANI: Kugwiritsa ntchito mafano polambira.

ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo.”​—Eksodo 20:4, 5, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Mtumwi Yohane analembera Akhristu kuti: “Muthawe mafano.”​—1 Yohane 5:21, Malembo Oyera.

FUNSO: Kodi chipembedzochi chimamvera lamulo lomveka bwino la m’Baibulo loletsa kugwiritsa ntchito mafano ndi zizindikiro polambira Mulungu?

Mungathe Kupeza Chipembedzo Chabwino

Ngakhale kuti masiku ano pali zipembedzo zambirimbiri, inuyo mukhoza kupeza chipembedzo chabwino chimene chingakuthandizeni kupeza moyo wosatha. Ndipo pali zizindikiro zambiri zodziwira “chipembedzo choona ndi chokoma pamaso pa Mulungu.” (Yakobe 1:27, Malembo Oyera) Malemba omwe takambirana mu nkhanizi angakuthandizeni kwambiri kudziwa chipembedzo chabwino.

Choncho mungachite bwino kupempha Mboni za Yehova kuti zikuthandizeni kupeza mayankho a mafunso omwe ali m’nkhanizi. Mukamaganizira zimene akukuphunzitsani, tsatirani chitsanzo cha anthu a ku Bereya, a m’nthawi ya atumwi. Iwo atamvetsera ulaliki wa mtumwi Paulo, “anasanthula Malembo tsiku ndi tsiku kuti awone ngati ndi zoona zimene Paulo amanena.” (Machitidwe 17:11, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Nanunso mukamalemekeza Mawu a Mulungu ndiponso mukamawaphunzira mwakhama, ngati mmene ankachitira anthu a ku Bereya, mudzapeza chipembedzo chimene chingakuthandizeni kupeza moyo wosatha. Komabe, zili ndi inu kusankha kulowa m’chipembedzo chimenecho.

Kodi ndi chipembedzo chiti chimene chimalimbikitsa anthu kuwerenga Malemba n’cholinga choti aone ngati zimene akuphunzirazo zili zoona?