Kodi Mafanizo a M’Baibulo Mumawamvetsa Bwino?
Kodi Mafanizo a M’Baibulo Mumawamvetsa Bwino?
M UNTHU akhoza kudziwa zambiri zokhudza nkhani inayake atangoona chithunzi chojambulidwa. Pamene nthawi zina, kungolankhula mawu amodzi kapena awiri okha kungachititse munthuyo kukhala ndi chithunzi chonse cha nkhaniyo. Ndipotu m’Baibulo muli mawu kapena kuti mafanizo ambiri oterowo, amene amathandiza munthu kukhala ndi chithunzi cha nkhani m’maganizo mwake. * Mwachitsanzo, Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo oposa 50 mu ulaliki wake wa paphiri.
N’chifukwa chiyani muyenera kuchita chidwi ndi mafanizo a m’Baibulo? N’chifukwa choti mukawamvetsa bwino, zimathandiza kuti muzisangalala mukawerenga Baibulo ndipo zimenezi zimachititsa kuti muziyamikira kwambiri Mawu a Mulungu. Komanso, mukazindikira mafanizo ndi kuwamvetsa bwino, mungamvetse uthenga wa m’Baibulo. Koma mukalephera kumvetsa fanizo la m’Baibulo, zingakusokonezeni kwambiri ndiponso nkhaniyo mungaimve molakwika.
Kumvetsa Tanthauzo la Fanizo
Mawu akuti fanizo akutanthauza kuyerekezera mfundo inayake ndi chinthu china. Chinthu chimene tikuyerekezeracho chimakhala mfundo yaikulu, pamene chinthu chimene tikuchiyerekezera ndi mfundoyo, chimakhala chithunzi cha nkhaniyo. Ndipo tikayerekezera zinthu ziwirizo timapeza kufanana kwake. Motero, kuti munthu amvetse bwino tanthauzo lenileni la fanizo, ayenera kuzindikira ndiponso kumvetsa bwino mbali zitatu zonsezi.
Nthawi zina zingakhale zosavuta kuzindikira mfundo yaikulu ndi chithunzi cha nkhaniyo. Koma nthawi zina pangakhale mbali zosiyanasiyana zosonyeza kufanana kwake. Nanga kodi mungatani kuti muzindikire kufanana kwake kwenikweni? Nthawi zambiri, kuwerenga nkhani yonse imene mukupezeka fanizolo n’kumene kungakuthandizeni. *
Mwachitsanzo, Yesu anauza mpingo wa ku Sade kuti: “Ndithudi, ukapanda kudzuka, ndidzabwera ngati mbala.” Apa, Yesu anayerekezera kubwera kwake (yomwe ndi mfundo yaikulu) ndi kubwera kwa mbala (chomwe ndi chithunzi cha nkhaniyo). Koma kodi pamenepa kufanana kwake kuli pati? Tingathe kuzindikira zimenezi poona nkhani yonse. Yesu anapitiriza kunena kuti: “Sudzadziwa konse ola limene ndidzafika pa iwe.” (Chivumbulutso 3:3) Choncho, mfundo yosonyeza kufanana kwake si yokhudza cholinga chimene iye akubwerera ayi. Yesu sankatanthauza kuti akubwera kudzaba. Koma ankatanthauza kuti adzabwera mosayembekezereka ngati mmene amachitira wakuba.
Nthawi zina, fanizo limene lili palemba lina lingatithandize kumvetsa fanizo lofanana nalo, lomwe lili palemba linanso. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito fanizo lofanana ndi la Yesu lija. Iye analemba kuti: “Pakuti inu eni mukudziwa bwino lomwe kuti tsiku la Yehova lidzabwera ndendende ngati mbala usiku.” (1 Atesalonika 5:2) Vesili silikusonyeza moonekeratu mfundo ya kubwera kwa tsiku la Yehova ndi kubwera kwa mbala. Komabe, kuyerekezera fanizoli ndi fanizo la Yesu la pa Chivumbulutso 3:3, kungakuthandizeni kumvetsa bwino kufanana kwa mfundo ziwirizi. Mafanizowa ali ndi mfundo yamphamvu kwambiri yokumbutsa Akhristu onse oona kuti ayenera kukhalabe maso mwauzimu.
Mafanizo Amene Amatiphunzitsa Makhalidwe a Mulungu
Palibe munthu amene angathe kumvetsa zonse zokhudza mphamvu za Mulungu ndiponso makhalidwe ake. Ponena za Yehova, Mfumu Davide analemba kuti “ukulu wake ngwosasanthulika.” (Salmo 145:3) Ndipo Yobu atasinkhasinkha kwambiri ntchito za Mulungu, ananena kuti: “Taonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong’onezo chaching’ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akuzindikiritsa ndani?”—Yobu 26:14.
Ngakhale kuti sitingamvetse zonse zokhudza mphamvu za Mulungu, Baibulo limagwiritsa ntchito mafanizo amene angatithandize kumvetsa pang’ono chabe makhalidwe ake ochititsa chidwi. Baibulo limasonyeza kuti Yehova ndi Mfumu, Wopanga malamulo, Woweruza, ndiponso Wankhondo. Ndipo n’zodziwikiratu kuti tiyenera kumulemekeza kwambiri chifukwa cha makhalidwe amenewa. Komanso tiyenera kumukonda kwambiri chifukwa Baibulo limasonyeza kuti iye ndi Mbusa, Mlangizi, Mphunzitsi, Tate, Wochiritsa ndiponso Mpulumutsi. (Salmo 16:7; 23:1; 32:8; 71:17; 89:26; 103:3; 106:21; Yesaya 33:22; 42:13; Yohane 6:45) Maina ofanizirawa akutithandiza kukhala ndi chithunzi cha mmene iye amachitira zinthu mofanana ndi winawake. Ndiponso maina ofanizirawa akutithandiza kumvetsa mfundo zochuluka koma m’mawu ochepa chabe.
Baibulo limayerekezeranso Yehova ndi zinthu zina zopanda moyo. Mwachitsanzo, limati iye ndi “Thanthwe la Isiraeli,” “thanthwe,” ndiponso “linga.” (2 Samueli 23:3; Salmo 18:2; Deuteronomo 32:4) Kodi zinthu zimenezi zikufanana bwanji ndi Yehova? Monga mmene thanthwe lilili lolimba ndiponso losasunthika, Yehova Mulungu ndiye chitetezo chathu cholimba ndiponso chosasunthika.
M’buku la Masalmo muli mafanizo ambiri amene amalongosola makhalidwe osiyanasiyana a Yehova. Mwachitsanzo, Salmo 84:11 limanena kuti Yehova ali ngati “dzuwa ndi chikopa,” chifukwa chakuti iye amatipatsa kuunika, moyo, mphamvu ndiponso amatiteteza. Komanso, Salmo 121:5 limati “Yehova ndiye mthunzi wako wa ku dzanja lako lamanja.” Anthu amene amam’tumikira, Yehova amawateteza ku mavuto otentha kwambiri ngati dzuwa, mofanana ndi mmene mthunzi umatetezera munthu kuti asapse ndi dzuwa. Amachita zimenezi powaphimba ndi mthunzi wa “dzanja” lake kapena wa “mapiko” ake.—Yesaya 51:16; Salmo 17:8; 36:7.
Mafanizo Onena za Yesu
Nthawi zambiri, Baibulo limanena kuti Yesu ndi “Mwana wa Mulungu.” (Yohane 1:34; 3:16-18) Anthu ena omwe si Akhristu samvetsa mfundo imeneyi chifukwa choti Mulungu alibe mkazi ndiponso iye si munthu. Ndiponso n’zodziwikiratu kuti Mulungu sangabereke mwana ngati mmene amachitira munthu. Motero, mawu amenewa ndi fanizo chabe. Cholinga cha fanizoli n’kuthandiza anthu kumvetsa bwino mfundo yakuti ubwenzi wa pakati pa Yesu ndi Mulungu, uli ngati mmene umakhalira ubwenzi wa pakati pa bambo ndi mwana wake. Fanizo limeneli limatsindika mfundo yakuti Yehova ndi amene analenga Yesu. Nayenso munthu woyamba, Adamu, amatchedwa “mwana wa Mulungu.”—Luka 3:38.
Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo pofotokoza ntchito zosiyanasiyana zimene iye amachita pokwaniritsa chifuniro cha Mulungu. Mwachitsanzo, iye anati: “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam’munda.” Kenako Yesu anayerekezera ophunzira ake ndi nthambi za mpesa. (Yohane 15:1, 4) Kodi fanizo limeneli likutiphunzitsa mfundo zofunika ziti? Kuti nthambi za mpesa zikhalebe ndi moyo ndiponso kuti zizibala zipatso, zimafunika kukhalabe kumtengo wake. Mofanana ndi zimenezi, ophunzira a Khristu ayenera kukhala ogwirizana naye. N’chifukwa chake Yesu anati: “Simungathe kuchita kalikonse popanda ine.” (Yohane 15:5) Ndipotu monga mmene mlimi amayembekezera kuti mpesa ubala zipatso, Yehova nayenso amayembekezera kuti anthu amene ali ogwirizana ndi Khristu, azibala chipatso cha mzimu.—Yohane 15:8.
Onetsetsani Kuti Mwamvetsa Kufanana Kwake
Nthawi zina munthu angathe kumva zolakwika ngati wangowerenga fanizo koma osamvetsa mfundo yosonyeza kufanana kwake. Mwachitsanzo, lemba la Aroma 12:20 limati: “Ngati mdani wako ali ndi njala, m’patse chakudya; ngati ali ndi ludzu, m’patse chakumwa; pakuti mwakutero udzamuunjikira makala a moto pamutu pake.” Kodi mawu akuti kumuunjikira makala amoto akutanthauza kubwezera choipa? Ayi sichoncho, chifukwa tikamvetsa mfundo yosonyeza kufanana kwake timaona kuti mawuwa sakutanthauza zimenezo. Fanizoli linachokera ku zimene anthu akale ankachita poyenga zitsulo. Miyala yopangira zitsulo ankaiika m’ng’anjo, ndiyeno ankaika makala amoto pamwamba ndi pansi pa miyalayo. Makala amoto omwe anali pamwamba ankatenthetsa kwambiri miyala yolimbayo moti inkasungunuka kenako n’kusiyana ndi zinthu zosafunika za m’miyalayo. N’chimodzimodzinso ifeyo, tikamachitira adani athu zinthu zabwino, tingafewetse mtima wawo kuti iwonso ayambe kusonyeza makhalidwe abwino.
Kumvetsa bwino tanthauzo la fanizo sikumangotithandiza kudziwa zinthu chabe koma kumatikhudzanso mtima kwambiri. Mwachitsanzo timazindikira kuopsa kwa tchimo akaliyerekezera ndi ngongole. (Luka 11:4, mawu a m’munsi) Ndipotu Yehova akatikhululukira machimo athu omwe amakhala ngati ngongole, timasangalala kwambiri. Timasangalalanso tikadziwa kuti iye ‘amakwirira’ machimo athu ndiponso kuti ‘amawafafaniza’ ngati mmene munthu angafufutire pabolodi. Ndipo n’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova akatikhululukira, iye sadzatiimbanso mlandu chifukwa cha machimo amene tinachitawo. (Salmo 32:1, 2; Machitidwe 3:19) Komanso n’zolimbikitsa kudziwa kuti ngakhale machimo athu atakhala ofiira chotani, Yehova akhoza kuwayeretsa kwambiri.—Yesaya 1:18.
M’nkhani ino tangoona mafanizo ochepa chabe mwa mafanizo ambiri omwe ali m’Baibulo. Choncho, mukamawerenga Baibulo yesetsani kuzindikira mafanizo ndipo fufuzani mfundo yaikulu ndiponso chithunzi chake, kenako sinkhasinkhani zimene mukuwerengazo. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kumvetsa bwino ndiponso kuyamikira Malemba.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 M’nkhani ino, mawu akuti “fanizo” akutanthauza mawu onse okuluwika ndiponso oyerekezera zinthu.
^ ndime 6 Buku lachingelezi lakuti Insight on the Scriptures, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, lili ndi mfundo zambiri zimene zingakuthandizeni kumvetsa bwino mafanizo.
[Bokosi patsamba 13]
Kodi Mafanizo Amatithandiza Bwanji?
Mafanizo amatithandiza m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, tingayerekezere mfundo inayake yovuta ndi chinthu china chosavuta kumvetsa. Pofuna kumvetsa mfundo inayake, tingagwiritse ntchito mafanizo osiyanasiyana omwenso akufotokoza mbali zosiyanasiyana za mfundoyo. Ndiponso tingagwiritse ntchito mafanizo kuti mfundo ikhale yosavuta kumva komanso yosangalatsa kwambiri.
[Bokosi patsamba 14]
Zindikirani Mbali Zosiyanasiyana M’fanizo
FANIZO: “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi.”(Mateyo 5:13)
MFUNDO YAIKULU: Inu (kutanthauza ophunzira a Yesu)
CHITHUNZI CHA NKHANI: Mchere
KUFANANA KWAKE: Kuteteza zinthu kuti zisawonongeke
PHUNZIRO: Ophunzira a Yesu anali ndi uthenga umene ukanathandiza kuti anthu asawonongeke
[Chithunzi patsamba 15]
“Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.”—SALMO 23:1