Akuluakulu a Katolika Akufuna Kusiyiratu Kugwiritsa Ntchito Dzina la Mulungu
Akuluakulu a Katolika Akufuna Kusiyiratu Kugwiritsa Ntchito Dzina la Mulungu
AKULUAKULU a Katolika akufuna kuti asiyiretu kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu pa mapemphero awo. Chaka chatha, bungwe la ku Vatican la akuluakulu a Katolika loona za kulambira ndiponso loika malamulo a kayendetsedwe ka Misa, linatumiza chikalata cha malangizo okhudza nkhaniyi kwa mabishopu a Katolika padziko lonse, “molangizidwa” ndi papa.
Chikalatachi chinalembedwa pa June 29, 2008, ndipo chinanena kuti Akatolika anali atalangizidwa kale kuti asamagwiritse ntchito dzina la Mulungu wa Isiraeli. Komabe, “m’zaka za posachedwapa iwo ayambiranso kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu, lomwe amati ndi lopatulika, ndipo limalembedwa ndi zilembo zinayi za Chiheberi izi, יהוה (YHWH).” Chikalatachi chinanenanso kuti dzina la Mulungu lakhala likulembedwa mosiyanasiyana monga kuti, “Yahweh,” “Yahwè,” “Jahweh,” “Jahwè,” “Jave,” ndiponso “Yehovah.” * Koma chikalatachi chinalamula kuti anthu asiyiretu kugwiritsa ntchito dzina limeneli. Zimenezi zikutanthauza kuti pamene pali dzina la Mulungu aziikapo mawu akuti “Ambuye.” Komanso panthawi ya mapemphero a Katolika, poimba nyimbo ndiponso popemphera, “ayenera kusiyiratu kutchula dzina la Mulungu lomwe amalilemba kuti YHWH.”
Chikalatachi chinanenanso kuti “kuyambira kale” Akatolika sankagwiritsa ntchito dzina limeneli. Chikalatachi chinanenanso kuti ngakhalenso m’Baibulo la Septuagint, lomasulira Malemba Achiheberi, limene linalembedwa Chikhristu chisanayambe, dzina la Mulungu ankalilemba ndi mawu a Chigiriki akuti Kyʹri·os, kutanthauza kuti “Ambuye.” N’chifukwa chake chikalatachi chinati, “Kuyambira kale Akhristu nawonso sankagwiritsa ntchito dzina la Mulungu.” Komabe zimenezi si zoona, chifukwa m’Baibulo lakale la Septuagint munali dzina la Mulungu lolembedwa ndi zilembo izi, יהוה osati Kyʹri·os (Ambuye). Otsatira a Khristu oyambirira, ankadziwa dzina la Mulungu ndiponso katchulidwe kake. Popemphera kwa Atate ake, Yesu anati: “Dzina lanu ndalidziwitsa.” (Yohane 17:26) Ndiponso m’pemphero lake lachitsanzo lomwe ndi lotchuka kwambiri, Yesu anatiphunzitsa kupemphera kuti: “Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.”—Mateyo 6:9.
Akhristu onse ayenera kuyesetsa kuchita zinthu zoyeretsa dzina la Mulungu. Choncho, Zimene akuchita atsogoleri a Chikatolika pofuna kusiyiratu kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu zikusonyeza kusalemekeza Mulungu amene anati: “Ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m’mibadwo mibadwo.”—Eksodo 3:15.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Dzina lakuti Yehova lakhala likugwiritsidwa ntchito kwa zaka zambiri ndipo limapezeka m’mabaibulo ambiri.
[Mawu Otsindika patsamba 30]
“Ili ndi dzina langa nthawi yosatha.”—Eksodo 3:15
[Chithunzi patsamba 30]
Chidutswa cha Baibulo la “Septuagint” cha m’nthawi ya atumwi. Dzina la Mulungu lomwe limalembedwa ndi zilembo za Chiheberi izi יהוה, (YHWH), lili mu mzere wozungulira
[Mawu a Chithunzi]
Courtesy of the Egypt Exploration Society